Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Banja

Banja

Yehova ndi amene anayambitsa banja

Makolo

Onani “Makolo

Abambo

Onani “Abambo

Amayi

Onani “Amayi

Mwamuna Wokwatira, Mkazi Wokwatiwa

Onani “Ukwati

Ana Aamuna ndi Aakazi

Kodi ana ali ndi udindo wotani m’banja?

N’chifukwa chiyani ana ayenera kumvera makolo awo?

Aef 6:1-3; Akl 3:20

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Sl 78:1-8​—Aisiraeli akamafotokozera ana awo zimene makolo awo akale ankachita, zinkawathandiza anawo kuti azikhulupirira Yehova komanso kumumvera

    • Lu 2:51, 52​—Ngakhale kuti Yesu anali wangwiro, ali mwana ankamverabe makolo ake omwe sanali angwiro ndipo anachita zimenezi kwa moyo wake wonse

N’chifukwa chiyani nthawi zina ana angalephere kumvera makolo awo?

Kodi Mulungu amaona bwanji ana osamvera?

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • De 21:18-21​—Chilamulo cha Mose chinkanena kuti mwana wamwamuna yemwe sakumvera makolo ake komanso ndi chidakwa ndipo akukana kutsatira malangizo, aziphedwa

    • 2Mf 2:23, 24​—Pamene gulu la anyamata linkanyoza mneneri Elisa yemwe anali mtumiki wa Mulungu, zimbalangondo ziwiri zinawapha

N’chifukwa chiyani makolo ayenera kuona kuti kulera ana ndi mwayi waukulu?

Sl 127:3; 128:3

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Le 26:9​—Aisiraeli ankaona kuti kubereka ana chinali chizindikiro cha madalitso ochokera kwa Yehova

    • Yob 42:12, 13​—Yehova anadalitsa Yobu limodzi ndi mkazi wake chifukwa cha kukhulupirika kwake ndipo anamupatsa ana 10 enanso

Kodi Yehova amafuna kuti anthu apachibale azichitirana bwanji zinthu?

Sl 34:14; Miy 15:23; 19:11

  • Nkhani ya m’Baibulo yomwe ingakuthandizeni:

    • Ge 27:41; 33:1-11​—Yakobo anachita zambiri posonyeza kuti ankalemekeza m’bale wake Esau, zomwe zinachititsa kuti akhazikitse mtendere

Kodi ana akakula angathandize bwanji makolo awo komanso agogo awo?

Miy 23:22; 1Ti 5:4

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Ge 11:31, 32​—Pamene Abulahamu ankachoka ku Uri, anatenga bambo ake a Tera ndipo anawasamalira mpaka imfa yawo

    • Mt 15:3-6​—Yesu anagwiritsa ntchito Chilamulo cha Mose posonyeza kuti ana akakula amafunika kusamalira makolo awo omwe akufunika thandizo

Makolo a Mwamuna Kapena Mkazi Wanu

Agogo

Onani “Agogo