Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ufulu

Ufulu

Ndi ndani amene ali ndi ufulu wopanda malire m’chilengedwe chonsechi?

Yes 40:13, 15; Aro 9:20, 21

Onaninso Aro 11:33-36

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Da 4:29-35​—Mfumu Nebukadinezara anadziwa kuti Yehova ndi Wolamulira Wamkulu ndipo palibe amene angamuuze zochita

    • Yes 45:6-12​—Monga Mlengi, Yehova ali ndi ufulu wosankha kusafotokoza chilichonse chimene akuchita

Ngakhale kuti Yehova ali ndi ufulu wopanda malire, kodi ndi zinthu zina ziti zimene iye amasankha kusachita?

N’chifukwa chiyani ufulu wa anthu uli ndi malire?

N’chifukwa chiyani nthawi zina Akhristu angasankhe kusachita zinthu zina ngakhale kuti ali ndi ufulu wochitira zimenezo?

N’chifukwa chiyani tinganene kuti atumiki a Yehova ali ndi ufulu?

N’chifukwa chiyani anthu amene amatumikira Yehova amakhala osangalala?

Sl 40:8

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Ge 18:3; Ahe 11:8-10​—Abulahamu sanaiwale zimene Yehova anamulonjeza ndipo zimenezi zinamuthandiza kuti apitirizebe kutumikira Mulungu

    • Ahe 11:24-26​—Mose anasankha kutumikira Yehova ndipo anamupatsa moyo wosangalala, ufulu komanso chiyembekezo cha zinthu zabwino

Kodi Yehova anatimasula ku ukapolo uti?

N’chifukwa chiyani sitiyenera kugwiritsa ntchito molakwika ufulu womwe tili nawo monga Akhristu?

Ndi pa nthawi ziti pamene chikondi chingachititse Akhristu kusankha kusachita zinthu zimene ali ndi ufulu wozichita?

Kodi uthenga womwe timalalikira umathandiza bwanji anthu kukhala ndi ufulu?

Kodi ndi ufulu wotani umene Baibulo limanena kuti tidzakhala nawo m’tsogolo?

Kodi anthu amene amangochita zilizonse zimene akufuna amakhala akapolo m’njira ziti?

Kodi timadziwa bwanji kuti Mulungu amaona kuti anthufe si osiyana?