Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chisoni

Chisoni

Ndi zitsanzo za m’Baibulo ziti zimene zikusonyeza kuti si kulakwa kumva chisoni munthu wina akamwalira?

N’chiyani chikusonyeza kuti Yehova ndi wofunitsitsa kutonthoza anthu amene akumva chisoni?

Kodi kudziwa zoona zokhudza akufa kumatitonthoza bwanji?

Mla 9:5, 10; 1At 4:13

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Lu 20:37, 38​—Yesu anafotokoza kuti nkhani ya kuuka kwa akufa ndi yotsimikizirika ndipo kwa Yehova onse ndi amoyo

    • Yoh 11:5, 6, 11-14​—Lazaro yemwe anali mnzake wa Yesu wapamtima atamwalira, Yesu anayerekezera imfa ndi tulo

    • Ahe 2:14, 15​—Mtumwi Paulo anafotokoza kuti anthu ambiri ali mu ukapolo woopa imfa, koma ifeyo sitiyenera kuopa imfa

N’chifukwa chiyani Yehova amaona kuti munthu wapanga dzina labwino pa nthawi yomwe wamwalira kuposa pa nthawi imene ankabadwa?

Kodi Baibulo limanena zotani zokhudza imfa? Nanga Mulungu adzachita zotani ndi imfa?

N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira kuti kudzakhala kuuka kwa akufa?

Yes 26:19; Yoh 5:28, 29; Mac 24:15

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Baibulo limanena za anthu 9 amene anaukitsidwa, koma 8 mwa iwo ataukitsidwa anakhalanso ndi moyo padziko lapansi pompano. Ngati wokondedwa wathu wamwalira, nkhani zimenezi zimatitonthoza komanso kutipatsa chiyembekezo

      • 1Mf 17:17-24​—Mneneri Eliya anaukitsa mwana wamwamuna wa mayi wamasiye wa ku Zarefati, m’tawuni ya Sidoni

      • 2Mf 4:32-37​—Mneneri Elisa anaukitsa mnyamata wina m’tawuni ya Sunemu kenako anamupereka kwa makolo ake

      • 2Mf 13:20, 21​—Munthu wina yemwe anali atangomwalira kumene anauka mtembo wake utangogunda mafupa a mneneri Elisa

      • Lu 7:11-15​—Yesu anakumana ndi gulu la anthu omwe ankapita kukaika maliro a mwana wamwamuna wa mkazi wamasiye kenako anamuukitsa

      • Lu 8:41, 42, 49-56​—Yesu anaukitsa mwana wamkazi wa Yairo, yemwe anali mtsogoleri wa sunagoge

      • Yoh 11:38-44​—Yesu anaukitsa mnzake wapamtima Lazaro ndipo anapitiriza kukhala ndi azichemwali ake aja Marita ndi Mariya

      • Mac 9:36-42​—Mtumwi Petulo anaukitsa Dorika yemwe anali mzimayi wa Chikhristu wodziwika ndi ntchito zachifundo zambiri

      • Mac 20:7-12​—Mtumwi Paulo anaukitsa mnyamata wina dzina lake Utiko, yemwe anafa atagwa kuchokera pawindo la nyumba yosanja

    • Yesu Khristu anaukitsidwa kukakhala ndi moyo wosafa kumwamba ndipo zimenezi zinatsimikizira kuti Mulungu adzakwaniritsa malonjezo onse am’tsogolo

    • Yesu anali woyamba kuukitsidwa kupita kumwamba komanso kupatsidwa moyo wosafa koma sanali womaliza; otsatira ake okwanira 144,000 nawonso amalandira moyo wofanana ndi umenewu

Kodi tingathandize bwanji anthu omwe akumva chisoni chifukwa cha imfa ya wokondedwa awo?