Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mtima Wokhulupirika

Mtima Wokhulupirika

Kodi mawu akuti mtima wokhulupirika amatanthauza chiyani?

Sl 18:23-25; 26:1, 2; 101:2-7; 119:1-3, 80

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Le 22:17-22​—Yehova ankafuna kuti anthu azipereka nsembe ya nyama “yopanda chilema” kapena vuto lina lililonse; mawu akuti “yopanda chilema” amafanana ndi mawu a Chiheberi omwe anamasuliridwa kuti “mtima wokhulupirika,” zomwe zikutanthauza kudzipereka kuti titumikira Yehova ndi mtima wonse

    • Yob 1:1, 4, 5, 8; 2:3​—Zimene Yobu ankachita pa moyo wake zikusonyeza kuti munthu angakhale ndi mtima wokhulupirika ngati amalemekeza kwambiri Yehova, amalambira Iye yekha komanso ngati akuyesetsa kupewa kuchita zimene Yehova amadana nazo

N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi mtima wokhulupirika?

N’chiyani chingatithandize kuti tisasiye kukhala ndi mtima wokhulupirika?

Tingatani kuti tikhale ndi mtima wokhulupirika ndiponso kupitirizabe kukhala nawo?

Yos 24:14, 15; Sl 101:2-4

Onaninso De 5:29; Yes 48:17, 18

  • Nkhani ya m’Baibulo yomwe ingakuthandizeni:

    • Yob 31:1-11, 16-33​—Yobu anasonyeza kuti anali ndi mtima wokhulupirika chifukwa ankapewa chiwerewere komanso ankalemekeza ena ndiponso kuwachitira zinthu mokoma mtima. Iye ankalambira Yehova yekha osati mafano ndiponso ankaona kuti chofunika kwambiri ndi kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu osati kukonda chuma

    • Da 1:6-21​—Danieli ndi anzake atatu anakhalabe ndi mtima wokhulupirika pa nthawi imene ankafunika kusankha zakudya ngakhale kuti ankakhala ndi anthu omwe sankatumikira Yehova

Kodi munthu amene wachita machimo akuluakulu maulendo angapo angathenso kukhala ndi mtima wokhulupirika?

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 1Mf 9:2-5; Sl 78:70-72​—Davide atalapa machimo ake Yehova anamukhululukira ndipo ankamuona kuti ndi munthu wa mtima wokhulupirika

    • Yes 1:11-18​—Ngakhale kuti Yehova anadzudzula anthu ake kuti ndi achinyengo komanso ochimwa, iye anawalonjeza kuti akhoza kuwasambitsa ndi kuwayeretsa ngati angasinthe n’kusiya kuchita zoipa