Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kukonda Chuma

Kukonda Chuma

Kodi Baibulo limanena kuti n’kulakwa kukhala ndi ndalama kapena katundu?

Mla 7:12

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 1Mf 3:11-14​—Yehova anadalitsa Mfumu Solomo pomupatsa chuma chochuluka chifukwa chakuti anali wodzichepetsa

    • Yob 1:1-3, 8-10​—Ngakhale kuti Yobu anali wolemera kwambiri, ankaona kuti ubwenzi wake ndi Yehova ndi wofunika kwambiri kuposa chilichonse

N’chifukwa chiyani ndalama komanso katundu sizingapangitse kuti tizikhala osangalala?

Kodi chuma chingakhale bwanji chopanda ntchito?

Kodi ndi mavuto aakulu ati omwe amabwera chifukwa chokhala ndi chuma?

Kodi chuma chingapusitse bwanji munthu?

Miy 11:4, 18, 28; 18:11; Mt 13:22

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Mac 8:18-24​—Simoni anaganiza mopanda nzeru kuti akhoza kugula udindo mumpingo wa Chikhristu ndi ndalama

Kodi tingataye mwayi wotani ngati timakonda ndalama?

Mt 6:19-21; Lu 17:31, 32

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Mko 10:17-23​—Mnyamata wina wachuma ankakonda kwambiri katundu wake zomwe zinamulepheretsa kukhala wotsatira wa Yesu

    • 1Ti 6:17-19​—Mtumwi Paulo anachenjeza Akhristu olemera kuti asamadzikweze chifukwa Mulungu angasiye kuwakonda

Kodi kukonda chuma kungafooketse bwanji chikhulupiriro chathu? Nanga kungachititse bwanji kuti Mulungu asiye kutikonda?

De 8:10-14; Miy 28:20; 1Yo 2:15-17

Onaninso Sl 52:6, 7; Amo 3:12, 15; 6:4-8

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Yobu ankadziwa bwino kuti kungakhale kulakwa kudalira chuma chake chifukwa zikanachititsa kuti asiye kudalira Mulungu

    • Lu 12:15-21​—Yesu ananena fanizo la munthu wolemera yemwe sanali wolemera kwa Mulungu pofuna kutichenjeza zokhudza kuopsa kokonda chuma

Kodi tingatani kuti tizikhutira ndi zimene tili nazo?

Kodi ndi chuma chiti chimene chimaposa katundu aliyense amene tingakhale naye, nanga n’chifukwa chiyani?

Miy 3:11, 13-18; 10:22; Mt 6:19-21

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Hag 1:3-11​—Kudzera mwa mneneri Hagai, Yehova ananena kuti asiya kudalitsa anthu ake chifukwa choti ankatanganidwa ndi kusamalira nyumba zawo m’malo mothandiza nawo pa ntchito yomanganso nyumba ya Yehova

    • Chv 3:14-19​—Yesu anadzudzula mpingo wa ku Laodikaya chifukwa choti unkakonda kwambiri chuma m’malo moika kutumikira Yehova pamalo oyamba

N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira kuti Yehova azitipatsa zinthu zimene timafunikira pa moyo wathu?