Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chifundo

Chifundo

Kodi munthu wachifundo amakhalanso ndi makhalidwe ena ati?

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Sl 51:1, 2​—Mfumu Davide atapempha Yehova kuti amuchitire chifundo, anapemphanso kuti amukhululukire ndi kumuyeretsa

    • Lu 10:29-37​—Yesu anatithandiza kumvetsa mmene tingasonyezere ena chifundo pofotokoza fanizo la Msamariya amene anachitira chifundo Myuda wina

N’chifukwa chiyani anthu onse amafunika kusonyezedwa chifundo?

Kodi timadziwa bwanji kuti Yehova ndi wachifundo?

Eks 34:6; Ne 9:17; Sl 103:8; 2Ak 1:3

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Yob 42:1, 2, 6-10; Yak 5:11​—Yehova anachitira chifundo Yobu ndipo anamuphunzitsa mmene iyenso angasonyezere ena chifundo

    • Lu 15:11-32​—Yesu anagwiritsa ntchito fanizo la bambo yemwe anachitira chifundo mwana wake wosamvera, pofuna kutithandiza kumvetsa mmene Yehova amatisonyezera chifundo

N’chifukwa chiyani Yehova amatichitira chifundo?

Kodi nsembe ya Khristu imathandiza bwanji kuti machimo athu azikhululukidwa?

N’chifukwa chiyani tiyenera kupempha kuti Yehova atichitire chifundo komanso kusonyeza kuyamikira?

Lu 11:2-4; Ahe 4:16

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Sl 51:1-4​—Mfumu Davide anadzimvera chisoni kwambiri chifukwa cha machimo amene anachita ndipo anadzichepetsa n’kupempha kuti Yehova amuchitire chifundo

    • Lu 18:9-14​—Yesu ananena fanizo pofuna kusonyeza kuti Yehova amasonyeza chifundo anthu amene amadzichepetsa n’kuvomereza zolakwa zawo

N’chifukwa chiyani Yehova amatha kuchitira chifundo ngakhale anthu amene achita machimo aakulu?

De 4:29-31; Yes 55:7

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 2Mb 33:9-13, 15​—Ngakhale kuti Manase anali mfumu yoipa kwambiri, iye analapa ndi kupempha kuti Yehova amuchitire chifundo; kenako anamubwezeranso pa ufumu ndipo pambuyo pake anapitiriza kuchita zinthu zabwino posonyeza kuti analidi atalapa

    • Yon 3:4-10​—Anthu a ku Nineve anali achiwawa komanso anapha anthu ambiri, koma analapa ndipo Mulungu anawachitira chifundo

Kuti Yehova atichitire chifundo, n’chifukwa chiyani tikachimwa tiyenera kuulula machimo athu kwa Iye ndi kulapa?

Ngakhale kuti Yehova amatisonyeza chifundo, sizikutanthauza kuti sitingalandire chilango kapena kukumana ndi mavuto chifukwa cha zolakwa zathu

N’chifukwa chiyani tiyenera kuchitira ena chifundo?

N’chiyani chingachitikire ubwenzi wathu ndi Yehova ngati titalephera kuchitira ena chifundo?

Mt 9:13; 23:23; Yak 2:13

Onaninso Miy 21:13

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Mt 18:23-35​—Yesu ananena fanizo lotithandiza kudziwa kuti ngati titalephera kusonyeza ena chifundo, nafenso Yehova sangatichitire chifundo

    • Lu 10:29-37​—Yesu ananena fanizo lomwe likutithandiza kudziwa kuti Yehova ndi Yesu, sasangalala ndi anthu amene sachitira ena chifundo, koma amasangalala ndi anthu amene amasonyeza chifundo ngati Msamariya wachifundo

Kodi Yehova amawachitira chiyani anthu achifundo?