Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kufatsa

Kufatsa

Kodi timadziwa bwanji kuti Yehova ndi wofatsa?

Mt 11:28, 29; Yoh 14:9

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 1Mf 19:12​—Pamene Eliya ankavutika maganizo, Yehova anamulankhula mawu “achifatse apansipansi”

    • Yon 3:10–4:11​—Ngakhale kuti Yona analankhula ndi Yehova atakwiya, zimene anamuchitira mokoma mtima zinam’phunzitsa khalidwe la chifundo

Kodi tingasonyeze bwanji kufatsa?

Miy 15:1; Aef 4:1-3; Tit 3:2; Yak 3:13, 17; 1Pe 3:15

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Nu 11:26-29​—Mneneri Mose anayankha mofatsa pamene Yoswa anamuuza kuti aletse anthu ena amene ankanenera

    • Owe 8:1-3​—Woweruza Gidiyoni anayankha mofatsa anthu omwe ankafuna kukangana naye