Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Azimayi

Azimayi

Kodi azimayi ali ndi maudindo otani?

Miy 31:17, 21, 26, 27; Tit 2:4

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Ge 21:8-12​—Sara ataona Isimaeli akuzunza mwana wake Isaki, anachonderera Abulahamu kuti ateteze mwana wakeyo

    • 1Mf 1:11-21​—Bati-seba atadziwa kuti ufumu komanso moyo wa mwana wake Solomo unali pangozi, anapempha Mfumu Davide kuti amuteteze

N’chifukwa chiyani tiyenera kumvera komanso kulemekeza amayi athu?

Eks 20:12; De 5:16; 27:16; Miy 1:8; 6:20-22; 23:22

Onaninso 1Ti 5:9, 10

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 1Pe 3:5, 6​—Mtumwi Petulo anafotokoza kuti Sara anali ngati mayi kwa ana aakazi ambiri chifukwa anali ndi chikhulupiriro cholimba

    • Miy 31:1, 15, 21, 28​—Mayi a Mfumu Lemueli anapereka malangizo othandiza kwa mwana wawoyu okhudza ukwati komanso udindo wa mkazi wokwatiwa ndi azimayi

    • 2Ti 1:5; 3:15​—Mtumwi Paulo anayamikira mayi ake a Timoteyo, a Yunike, chifukwa chophunzitsa mwana wawo Malemba kuchokera pamene anali wakhanda ngakhale kuti amuna awo anali osakhulupirira