Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kumvera

Kumvera

Kodi kumvera kuli ndi ubwino wotani?

Eks 19:5; De 10:12, 13; Mla 12:13; Yak 1:22

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 1Sa 15:17-23​—Mneneri Samueli anadzudzula Mfumu Sauli chifukwa chosamvera Yehova; kenako Samueli akumuuza mwamphamvu za kufunika komvera

    • Ahe 5:7-10​—Ngakhale kuti nthawi zonse Yesu ankamvera Atate wake, ali padzikoli anaphunzira kumvera pa nthawi imene anthu ankamuzunza

Kodi Mkhristu ayenera kuchita chiyani ngati akuluakulu a boma atamuuza kuti asamvere Mulungu?

Mac 5:29

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Da 3:13-18​—Aheberi atatu anakana kugwadira fano limene Mfumu Nebukadinezara inaimika, ngakhale kuti kuchita zimenezi kunaika moyo wawo pangozi

    • Mt 22:15-22​—Yesu anafotokoza kuti otsatira ake amamvera maboma a anthu koma samamvera mabomawo ngati akuwauza kuchita zinthu zosemphana ndi zimene Yehova Mulungu amafuna

    • Mac 4:18-31​—Atumwi sanasiye kulalikira ngakhale kuti olamulira anawaletsa

Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tisasiye kumvera Yehova?

De 6:1-5;Sl 112:1; 1Yo 5:2, 3

Onaninso Sl 119:11, 112; Aro 6:17

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Eza 7:7-10​—Ezara anali wansembe wokhulupirika ndipo anakonzekeretsa mtima wake kuti akhale chitsanzo chabwino pa nkhani yomvera Chilamulo cha Yehova komanso kuphunzitsa ena

    • Yoh 14:31​—Yesu anafotokoza chifukwa chake amachita zinthu ndendende mmene Atate wake anamutumira

N’chifukwa chiyani tiyenera kumvera Yehova ndi Yesu?

Kodi kumvera kumasonyeza bwanji kuti tili ndi chikhulupiriro?

Aro 1:5; 10:16, 17; Yak 2:20-23

Onaninso De 9:23

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Ge 6:9-22; Ahe 11:7​—Nowa anasonyeza chikhulupiriro pomanga chingalawa ndendende mogwirizana ndi mmene Yehova anamulamulira ndipo “anachitadi zomwezo”

    • Ahe 11:8, 9, 17​—Abulahamu anasonyeza chikhulupiriro pomvera Yehova atamuuza kuti achoke ku Uri, komanso atamuuza kuti apereke mwana wake nsembe

Kodi Yehova amadalitsa bwanji anthu omvera?

Yer 7:23; Mt 7:21; 1Yo 3:22

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Le 26:3-6​—Yehova analonjeza kuti adzadalitsa ndi kusamalira anthu amene amamumvera

    • Nu 13:30, 31; 14:22-24​—Kalebe anali womvera ndipo Yehova anamudalitsa

Kodi kusamvera kumabweretsa mavuto otani?

Aro 5:19; 2At 1:8, 9

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Ge 2:16, 17; 3:17-19​—Adamu ndi Hava anataya mwayi wokhala ndi moyo wangwiro kwamuyaya, m’Paradaiso, chifukwa sanamvere Yehova Mulungu

    • De 18:18, 19; Mac 3:12, 18, 22, 23​—Yehova analosera kuti kudzabwera mneneri wamkulu kuposa Mose komanso kuti amene sadzamvera mneneriyu adzalandira chilango

    • Yuda 6, 7​—Angelo opanduka komanso anthu osamvera a ku Sodomu ndi Gomora anaputa mkwiyo wa Yehova

N’chifukwa chiyani tiyenera kumvera Yesu Khristu?

Ge 49:10; Mt 28:18

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Yoh 12:46-48; 14:24​—Yesu anafotokoza kuti tikapanda kumvera mawu ake, tidzalandira chilango m’tsogolo

N’chifukwa chiyani Akhristu ayenera kumvera akulu mumpingo?

N’chifukwa chiyani mkazi wa Chikhristu ayenera kumvera mwamuna wake?

N’chifukwa chiyani ana ayenera kumvera makolo awo?

Miy 23:22; Aef 6:1; Akl 3:20

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Ge 37:3, 4, 8, 11-13, 18​—Yosefe ali mwana ankamvera bambo ake ndipo anapita kukaona azichimwene ake ngakhale kuti ankadana naye

    • Lu 2:51​—Yesu anapitirizabe kumvera Yosefe ndi Mariya ngakhale kuti iye anali wangwiro koma makolo akewo sanali angwiro

N’chifukwa chiyani ndi nzeru kumamvera mabwana athu ngakhale pamene anthu ena sakutiona?

N’chifukwa chiyani Akhristu amamvera maboma?