Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Makolo

Makolo

Kodi n’chifukwa chiyani Yehova anayambitsa banja?

Kodi makolo ayenera kuwaona bwanji ana awo?

Sl 127:3-5; 128:3

Onaninso “Ana; Achinyamata

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Ge 33:4, 5​—Yakobo ankaona kuti ana ake ndi madalitso ochokera kwa Yehova

    • Eks 1:15, 16, 22; 2:1-4; 6:20​—Amuramu ndi Yokebedi anabereka Mose ndipo iwo analolera kuika moyo wawo pangozi kuti ateteze mwanayo

Kodi makolo ayenera kuchitira ana awo zinthu zotani?

De 6:6, 7; 11:18, 19; Miy 22:6; 2Ak 12:14; 1Ti 5:8

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 1Sa 1:1-4​—Elikana anapita ndi banja lake ku Silo ndipo anaonetsetsa kuti ana ake onse akulambira Yehova limodzi naye

    • Lu 2:39, 41​—Nthawi zonse Yosefe ndi Maria ankayenda ndi ana awo kuchokera ku Nazareti kupita ku Yerusalemu kuchikondwerero cha Pasika

N’chifukwa chiyani ndi bwino kuphunzitsa ana kuti azimvera Yehova?

Miy 1:8, 9; 22:6

Onaninso 2Ti 3:14, 15

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 1Sa 2:18-21, 26; 3:19 ​—Makolo a Samueli anapereka mwana wawo kuti azikatumikira kuchihema, komabe iwo ankapita kukamuona komanso kukamupatsa zofunikira; zimenezi zinathandiza kuti akhale munthu wokonda Yehova ndiponso azimutumikira mokhulupirika

    • Lu 2:51, 52​—Yesu anapitirizabe kumvera makolo ake ngakhale kuti iwo sanali angwiro

Kodi makolo angapeze kuti malangizo ophunzitsira ana awo?

De 6:4-9; Aef 6:4; 2Ti 3:14-17

Onaninso Sl 127:1; Miy 16:3

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Owe 13:2-8​—Mngelo atauza Manowa kuti mkazi wake adzakhala ndi mwana, iye anapempha Yehova kuti awapatse nzeru za mmene angalerere mwanayo

    • Sl 78:3-8​—Yehova amafuna kuti makolo aziphunzitsa ana awo mfundo za m’Baibulo

N’chifukwa chiyani ana amene akulira m’banja lokonda Mulungu amatha kusankha kusatumikira Yehova?

Eze 18:1-13, 20

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Ge 6:1-5; Yuda 6​—Angelo ambiri anasankha kupandukira Yehova ngakhale kuti anali atakhala naye kwa zaka zambiri kumwamba

    • 1Sa 8:1-3​—Ngakhale kuti Samueli anali mneneri wokhulupirika komanso wolungama, ana ake ankachita ziphuphu komanso zinthu zopanda chilungamo

Kodi makolo ayenera kuyamba liti kuphunzitsa ana awo zimene Mulungu amafuna kuti azichita?

2Ti 3:15

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • De 29:10-12, 29; 31:12; Eza 10:1​—Aisiraeli akasonkhana pamodzi kuti aphunzire zokhudza Yehova, ankakhala limodzi ndi ana awo

    • Lu 2:41-52​—Chaka chilichonse, Yosefe ndi Mariya ankatenga ana awo kuphatikizapo Yesu popita kuchikondwerero cha Pasika kukachisi wa ku Yerusalemu

Kodi makolo ayenera kutsatira zitsanzo ziti pamene akufuna kuteteza ana awo kwa anthu amene angawachitire nkhanza?

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Eks 19:4; De 32:11, 12​—Yehova anadziyerekezera ndi chiwombankhanga chimene chimanyamula, kuteteza komanso kusamalira ana ake

    • Yes 49:15​—Yehova analonjeza kuti adzasamalira komanso kuteteza atumiki ake kuposa mmene mayi woyamwitsa amasamalirira mwana wake wakhanda

    • Mt 2:1-16​—Satana ankafuna kupha Yesu ali wakhanda potsogolera anthu okhulupirira nyenyezi kwa Mfumu Herode, koma Yehova anateteza Mwana wake pouza Yosefe kuti athawire ku Iguputo

    • Mt 23:37​—Yesu anasonyeza kuti ndi wofunitsitsa kuthandiza anthu ake mofanana ndi mmene nkhuku yathadzi imatetezera ana ake powabisa m’mapiko

N’chifukwa chiyani makolo ayenera kuphunzitsa ana awo nkhani zokhudza kugonana?

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Le 15:2, 3, 16, 18, 19; De 31:10-13​—Chilamulo cha Mose chinkanena mosapita m’mbali nkhani zokhudza kugonana ndipo Yehova analamula kuti ana azimvetsera nawo Chilamulochi chikamawerengedwa mokweza

    • Sl 139:13-16​—Wamasalimo Davide anatamanda Yehova chifukwa cha mmene thupi la munthu linalengedwera modabwitsa komanso m’njira yoti anthu azitha kubereka ana

    • Miy 2:10-15​—Kudziwa zinthu komanso nzeru zochokera kwa Yehova zingatiteteze kwa anthu oipa komanso achinyengo

N’chifukwa chiyani makolo ayenera kulangiza kapena kuphunzitsa ana awo mwachikondi?

Miy 13:24; 29:17; Yer 30:11; Aef 6:4

Onaninso Sl 25:8; 145:9; Akl 3:21

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Sl 32:1-5​—Yehova anapereka chilango kwa Mfumu Davide chifukwa cha tchimo lomwe anachita komabe analimbikitsidwa atadziwa kuti Yehova amakhululukira anthu omwe alapa kuchokera pansi pa mtima

    • Yon 4:1-11​—Mneneri Yona analankhula kwa Yehova mopsa mtima komanso mopanda ulemu; komabe Yehova anamulezera mtima pofuna kumuphunzitsa kuti Iye ndi wachifundo

N’chifukwa chiyani tinganene kuti makolo amasonyeza chikondi akamapereka chilango kwa ana awo?