Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chizunzo

Chizunzo

N’chifukwa chiyani Akhristu saona zachilendo anthu ena akamawazunza?

N’chifukwa chiyani timadalira Yehova kuti atithandize pamene tikuzunzidwa?

Sl 55:22; 2Ak 12:9, 10; 2Ti 4:16-18; Ahe 13:6

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 1Mf 19:1-18​—Pamene mneneri Eliya ankazunzidwa, anapemphera kwa Yehova ndipo analimbikitsidwa

    • Mac 7:9-15​—Pamene azibale ake a Yosefe ankamuzunza, Yehova anakhalabe wokhulupirika kwa iye, anamupulumutsa komanso anamugwiritsa ntchito kuti apulumutse banja lake

Kodi pali mitundu iti ya chizunzo?

Kunyozedwa

2Mb 36:16; Mt 5:11; Mac 19:9; 1Pe 4:4

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 2Mf 18:17-35​—Rabisake yemwe ankalankhula m’malo mwa mfumu ya Asuri, ananyoza Yehova ndiponso analankhula zachipongwe kwa anthu a ku Yerusalemu

    • Lu 22:63-65; 23:35-37​—Anthu omwe ankazunza Yesu anamulankhula zonyoza komanso zachipongwe pa nthawi yomwe anamugwira komanso ali pamtengo wozunzikirapo

Achibale akamatitsutsa

Kumangidwa komanso kuonekera pamaso pa akuluakulu a boma

Nkhanza

Gulu la anthu oukira

Kupha

Kodi Akhristu ayenera kutani akamazunzidwa?

Mt 5:44; Mac 16:25; 1Ak 4:12, 13; 1Pe 2:23

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Mac 7:57–8:1​—Ngakhale kuti anali atatsala pang’ono kumwalira chifukwa cha nkhanza zomwe gulu la anthu linamuchitira, Sitefano anapempha Mulungu kuti achitire chifundo anthuwo kuphatikizapo Saulo wa ku Taliso

    • Mac 16:22-34​—Ngakhale kuti mtumwi Paulo anamenyedwa komanso kuikidwa m’matangadza, anakomera mtima munthu yemwe anamumanga, ndipo zimenezi zinachititsa kuti munthuyo ndi banja lake lonse akhale Akhristu

Kodi n’chiyani chimene chinachitikira Akhristu a m’nthawi ya Atumwi?

Kodi tiyenera kumva bwanji anthu ena akamatizunza?

Kodi chiyembekezo chathu chingatilimbikitse bwanji pa nthawi ya chizunzo?

N’chifukwa chiyani sitiyenera kulola kuti anthu amene amatizunza atichititse manyazi, mantha kapena kutifooketsa? Nanga n’chifukwa chiyani sitiyenera kusiya kutumikira Yehova?

Sl 56:1-4; Mac 4:18-20; 2Ti 1:8, 12

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 2Mb 32:1-22​—Pamene Mfumu Hezekiya ankaopsezedwa ndi asilikali amphamvu a Mfumu Senakeribu, iye anadalira Yehova komanso analimbikitsa anthu onse ndipo Yehova anamudalitsa kwambiri

    • Ahe 12:1-3​—Pamene anthu ankazunza Yesu kuti amuchititse manyazi, iye sanalole kuti zimenezo zimufooketse

Kodi tingakumane ndi zinthu zabwino ziti tikamazunzidwa?

Tikamapirira mayesero, Yehova amasangalala komanso dzina lake limalemekezedwa

1Pe 2:19, 20; 4:12-16

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Yob 1:6-22; 2:1-10​—Yobu anakana kuchitira zachipongwe Yehova ngakhale kuti sankadziwa kuti Satana ndi amene ankachititsa mavuto ake, ndipo Mulungu analemekezeka n’kutsimikizira kuti Satana ndi wabodza

    • Da 1:6, 7; 3:8-30​—Hananiya, Misayeli, Azariya (Shadireki, Misheki ndi Abedinego) anali okonzeka kuphedwa m’malo mosamvera Yehova; zotsatirapo zake Mfumu Nebukadinezara analemekeza Yehova pamaso pa anthu onse

Chizunzo chingatsegule mwayi woti anthu ena adziwe zokhudza Yehova

Lu 21:12, 13; Mac 8:1, 4

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Mac 11:19-21​—Akhristu omwe anabalalika chifukwa cha chizunzo anapitiriza kufalitsa uthenga wabwino m’madera ambiri

    • Afi 1:12, 13​—Mtumwi Paulo anasangalala kuti kumangidwa kwake kunathandiza anthu kumva uthenga wabwino

Tikamapirira pozunzidwa zingalimbitse chikhulupiriro cha Akhristu anzathu

Kodi atsogoleri achipembedzo ndi andale amazunza bwanji Akhristu okhulupirika?

Yer 26:11; Mko 3:6; Yoh 11:47, 48, 53; Mac 25:1-3

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Mac 19:24-29​—Anthu omwe anapanga tiakachisi ta Atemi ku Efeso, ankaona kuti uthenga womwe Akhristu ankalalikira wokhudza kulambira mafano ukanachititsa kuti bizinesi yawo isamayende bwino, choncho ankazunza Akhristu

    • Aga 1:13, 14​—Paulo (Saulo) asanakhale Mkhristu, anali wakhama m’chipembedzo cha Chiyuda, choncho ankazunza mpingo

Ndi ndani amene ankachititsa kuti atumiki a Yehova azizunzidwa?