Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulalikira Uthenga Wabwino

Kulalikira Uthenga Wabwino

N’chifukwa chiyani Akhristu oona onse amauza ena zimene amakhulupirira?

Kodi Yesu anatipatsa chitsanzo chotani pa nkhani yolalikira?

Lu 8:1; Yoh 18:37

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Lu 4:42-44​—Yesu ananena kuti anabwera padziko lapansi kudzagwira ntchito yolalikira

    • Yoh 4:31-34​—Yesu anafotokoza kuti ntchito yolalikira inali ngati chakudya chake

Kodi ndi amuna audindo okha mumpingo amene ayenera kumagwira ntchito yolalikira uthenga wabwino?

Sl 68:11; 148:12, 13; Mac 2:17, 18

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 2Mf 5:1-4, 13, 14, 17​—Kamtsikana ka Chiisiraeli kanauza mkazi wa Namani zokhudza Elisa mneneri wa Yehova

    • Mt 21:15, 16​—Yesu anatsutsa ansembe aakulu ndi alembi pamene ankaletsa ana kumutamanda m’kachisi

Kodi oyang’anira angasonyeze bwanji chitsanzo chabwino polalikira uthenga wabwino komanso kuphunzitsa ena mumpingo kuti azilalikira?

Kodi Yehova ndi Yesu amatithandiza bwanji pamene tikugwira ntchito yolalikira?

2Ak 4:7; Afi 4:13; 2Ti 4:17

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Mac 16:12, 22-24; 1At 2:1, 2​—Ngakhale kuti mtumwi Paulo ndi anzake ankachitidwa zachipongwe, Mulungu anawathandiza kupitiriza kulalikira molimba mtima

    • 2Ak 12:7-9​—Mtumwi Paulo yemwe anali mlaliki wakhama, anali ndi “minga m’thupi,” yomwe mwina inali matenda a m’thupi; koma Yehova anamupatsa mphamvu kuti apitirize kugwira ntchito yolalikira

Kodi ndi ndani amene amapatsa Akhristu ufulu komanso mphamvu zolalikira?

1Ak 1:26-28; 2Ak 3:5; 4:13

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Yoh 7:15​—Ngakhale kuti Yesu sanapite kusukulu ya Arabi, koma ankadziwa zinthu zambiri komanso kuphunzitsa mogwira mtima zomwe zinadabwitsa anthu ambiri

    • Mac 4:13​—Anthu ankaona kuti ophunzira a Yesu ndi osaphunzira komanso anthu wamba; koma iwo sankaopa kulalikira komanso kuphunzitsa molimba mtima

Kodi timadziwa bwanji kuti Yehova amafuna kuti tiziphunzitsa ena kuti azitha kulalikira komanso kuphunzitsa

Mko 1:17; Lu 8:1; Aef 4:11, 12

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Yes 50:4, 5​—Asanabwere padzikoli, Mesiya analandira maphunziro kuchokera kwa Yehova Mulungu

    • Mt 10:5-7​—Ali padzikoli, Yesu anaphunzitsa ophunzira ake moleza mtima kugwira ntchito yolalikira

Kodi tiyenera kuona bwanji ntchito yathu yolalikira uthenga wabwino?

Kodi Akhristu amamva bwanji akamagwira ntchito yolalikira?

Kodi timalankhula zinthu ziti tikamalalikira uthenga wabwino?

N’chifukwa chiyani timauza anthu ena mosabisa zokhudza ziphunzitso zabodza?

2Ak 10:4, 5

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Mko 12:18-27​—Yesu anagwiritsa ntchito Malemba posonyeza Asaduki kuti ankalakwitsa posakhulupirira za kuuka kwa akufa

    • Mac 17:16, 17, 29, 30​—Mtumwi Paulo anafotokozera anthu a ku Atene zifukwa zosonyeza kuti n’kulakwa kulambira mafano

Kodi timatani pogwira ntchito yolalikira?

N’chifukwa chiyani timalalikira kulikonse kumene kuli anthu?

Pamene tikugwira ntchito yolalikira, n’chifukwa chiyani timafunika kuleza mtima ndiponso kupirira?

Kodi uthenga wabwino umakhudza bwanji anthu amene ali ndi chidwi?

N’chifukwa chiyani Mkhristu aliyense afunika kugwiritsa ntchito mpata uliwonse umene ali nawo kuti alalikire?

1Ak 9:23; 1Ti 2:4; 1Pe 3:15

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Yoh 4:6, 7, 13, 14​—Ngakhale kuti Yesu anatopa, koma analalikirabe uthenga wabwino kwa mzimayi wa Chisamariya pachitsime

    • Afi 1:12-14​—Ngakhale kuti mtumwi Paulo anamangidwa chifukwa cha chikhulupiriro chake, anagwiritsa ntchito mpata umene anali nawo kuti alalikire komanso kulimbikitsa ena

Kodi tiziyembekezera kuti wina aliyense angamvetsere uthenga wathu?

Yoh 10:25, 26; 15:18-20; Mac 28:23-28

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Yer 7:23-26​—Kudzera mwa Yeremiya, Yehova anafotokoza zokhudza anthu Ake kuti anakana mobwerezabwereza uthenga umene aneneri Ake ankawauza

    • Mt 13:10-16​—Yesu anafotokoza kuti mofanana ndi mmene zinalili m’nthawi ya Yesaya, anthu ambiri adzamva uthenga wabwino koma adzakana kutsatira zimene amvazo

N’chifukwa chiyani sitimadabwa anthu ambiri akamanena kuti ndi otanganidwa moti sakufuna kumvetsera uthenga wathu?

N’chifukwa chiyani anthu ena amamvetsera ulendo woyamba koma kenako n’kusiya kuphunzira?

Ndi zitsanzo ziti zimene zingatithandize ngati anthu akutsutsa uthenga umene tikulalikira?

Kodi timatani anthu ena akamafuna kutiletsa kulalikira?

N’chiyani chimatitsimikizira kuti anthu ena akhoza kumvetsera uthenga wabwino?

Kodi anthu amene amalalikira uthenga wabwino adzayankha chiyani kwa Mulungu?

N’chifukwa chiyani tifunika kulalikira kwa anthu amitundu yonse kuphatikizapo azipembedzo zonse komanso mayiko onse?

Kodi n’zoyenera kulalikira tsiku lililonse kuphatikizapo limene ena amati ndi la Sabata?

Kodi ndi zitsanzo ziti zomwe zikusonyeza kuti tiyenera kulalikira kwa anthu onse kuphatikizapo amene ali ndi Baibulo komanso ali m’chipembedzo chawo?