Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulapa

Kulapa

N’chifukwa chiyani munthu aliyense ayenera kulapa machimo ake komanso kupempha Yehova kuti amukhululukire?

Aro 3:23; 5:12; 1Yo 1:8

Onaninso Mac 26:20

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Lu 18:9-14​—Yesu ananena fanizo losonyeza kufunika kolapa machimo athu komanso kupemphera kwa Yehova kuti azitithandiza

    • Aro 7:15-25​—Ngakhale kuti Paulo anali mtumwi komanso munthu wachikhulupiriro cholimba, komabe ankalimbana ndi maganizo ofuna kuchita zoipa

Kodi Baibulo limanena kuti Yehova amawaona bwanji anthu amene alapa?

Eze 33:11; Aro 2:4; 2Pe 3:9

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Lu 15:1-10​—Yesu anagwiritsa ntchito fanizo posonyeza kuti Yehova ndi angelo kumwamba amasangalala munthu wochimwa akalapa

    • Lu 19:1-10​—Zakeyu, mkulu wa okhometsa msonkho komanso wachinyengo, analapa n’kusintha zochita zake, ndipo Yehova anamukhululukira komanso anakhala ndi mwayi wodzapulumutsidwa

Kodi tingasonyeze bwanji kuti talapadi mochokera pansi pa mtima?

Kodi kudziwa choonadi molondola kumamuthandiza bwanji munthu kuti alapedi mochokera pansi pa mtima?

Aro 12:2; Akl 3:9, 10; 2Ti 2:25

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Mac 17:29-31​—Mtumwi Paulo anafotokozera anthu a ku Atene chifukwa chake kulambira mafano ndi chizindikiro cha umbuli, ndipo anawalimbikitsa kuti alape

    • 1Ti 1:12-15​—Mtumwi Paulo asanadziwe choonadi molondola chokhudza Yesu Khristu, anachita machimo akuluakulu mosadziwa

Kodi kulapa kuli ndi ubwino wotani?

N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira kuti tikalapa, Yehova angathe kutikhululukira ngakhale pamene tachimwa maulendo angapo?

Kodi Yehova amachita bwanji zinthu ndi anthu amene alapa machimo awo n’kusintha zochita zawo?

Kodi timadziwa bwanji kuti kulapa kumaphatikizapo zambiri kuposa kungodzimvera chisoni kapena kupepesa basi?

2Mb 7:14; Miy 28:13; Eze 18:30, 31; 33:14-16; Mt 3:8; Mac 3:19; 26:20

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 2Mb 33:1-6, 10-16​—Ngakhale kuti Mfumu Manase anachita zoipa zambiri kwa nthawi yaitali, iye anadzichepetsa n’kulapa mochokera pansi pa mtima, anapemphera mosalekeza komanso anasintha zochita zake

    • Sl 32:1-6; 51:1-4, 17​—Mfumu Davide anasonyeza kulapa pamene anaulula machimo ake, kupemphera kwa Yehova kuti amukhululukire komanso kudzimvera chisoni chifukwa cha zimene anachitazo

N’chifukwa chiyani tiyenera kukhululukira anthu amene atilakwira?