Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuthetsa Kusamvana

Kuthetsa Kusamvana

N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kupsa mtima kapena kubwezera munthu wina akatilakwira?

Miy 20:22; 24:29; Aro 12:17, 18; Yak 1:19, 20; 1Pe 3:8, 9

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 1Sa 25:9-13, 23-35​—Nabala atanyoza Davide ndi anyamata ake n’kukana kuwapatsa thandizo, mopupuluma Davide anaganiza zopha Nabala ndi amuna onse am’banja lake. Kenako malangizo anzeru amene Abigayeli anapereka anathandiza kuti asabwezere

    • Miy 24:17-20​—Mouziridwa, Mfumu Solomo inachenjeza anthu a Mulungu kuti Yehova samafuna kuti tizisangalala adani athu akamavutika; m’malomwake tizingozisiya m’manja mwa Yehova yemwe ndi woweruza wachilungamo

Kodi Mkhristu ayenera kusiya kulankhulana kapena kusiya kucheza ndi munthu amene wamulakwira?

Le 19:17, 18; 1Ak 13:4, 5; Aef 4:26

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Mt 5:23, 24​—Yesu anafotokoza kuti ngati tasemphana maganizo ndi m’bale wathu, tifunika kuchita zonse zimene tingathe pokhazikitsa mtendere

Kodi tiyenera kuchita chiyani munthu wina akatilakwira?

N’chifukwa chiyani tifunika kupitiriza kukhululukira anthu ena ngakhale atatilakwira mobwerezabwereza?

Ngati Mkhristu mnzathu watilakwira, mwachitsanzo kutinena miseche kapena kutichitira zachinyengo, ndi ndani amene ayenera kulankhula naye, nanga n’cholinga chotani?

Mt 18:15

Onaninso Yak 5:20

Ngati munthu yemwe watinena miseche kapena kutichitira zachinyengo akukana kupepesa titalankhulana naye pa awiri, kodi tiyenera kuchita chiyani?