Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kusakhala Pabanja

Kusakhala Pabanja

N’chifukwa chiyani kusakhala pabanja kukhoza kukhala kwabwino?

N’chifukwa chiyani n’kulakwa kukakamiza m’bale kapena mlongo kuti akwatire kapena kukwatiwa?

1Ak 7:28, 32-35; 1At 4:11

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Aro 14:10-12​—Mtumwi Paulo anafotokoza chifukwa chake n’kulakwa kuweruza Akhristu anzathu

    • 1Ak 9:3-5​—Mtumwi Paulo anali ndi ufulu wokwatira; komabe, chifukwa choti sanali pabanja, ankatha kuchita zambiri potumikira Yehova

Kodi anthu omwe sali pabanja ayenera akuganiza kuti akufunika kukhala pabanja n’cholinga choti azikhala moyo wosangalala?

1Ak 7:8

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Owe 11:30-40​—Mwana wamkazi wa Yefita anasankha kusakhala pabanja koma ankakhala moyo wosangalala potumikira panyumba ya Yehova

    • Mac 20:35​—Ngakhale kuti Yesu sanakwatire, mawu akewa akusonyeza kuti ankakhala mosangalala chifukwa cha zimene ankachita pothandiza ena

    • 1At 1:2-9; 2:12​—Mtumwi Paulo yemwe anali wosakwatira anafotokoza mmene kuchita utumiki kunamuthandizira kukhala wosangalala chifukwa choti anathandiza anthu ambiri kudziwa Yehova

N’chifukwa chiyani anthu omwe sali pabanja mofanana ndi atumiki a Yehova onse, afunika kukhalabe ndi makhalidwe oyera?

1Ak 6:18; Aga 5:19-21; Aef 5:3, 4

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Miy 7:7-23​—Mfumu Solomo anafotokoza mavuto amene mnyamata wina anakumana nawo chifukwa cholola kusocheretsedwa ndi mkazi wachiwerewere

    • Nym 4:12; 8:8-10​—Msulami anayamikiridwa chifukwa cha khalidwe lake loyera

Kodi ndi malangizo ati anzeru amene angathandize munthu amene sali pabanja kusankha kukwatira kapena kukwatiwa?