Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ntchito

Ntchito

Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa ntchito ndi chimwemwe?

Kodi pali ubwino wotani ngati munthu waphunzira bwino ntchito n’cholinga choti aziigwira mwaluso?

Miy 22:29

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 1Sa 16:16-23​—Davide ali wamng’ono anali ndi luso loimba bwino nyimbo ndipo mfumu ya Isiraeli ikamamvetsera nyimbozo inkamva bwino mumtima

    • 2Mb 2:13, 14​—Hiramu-abi anali ndi luso pa ntchito yake, choncho Mfumu Solomo inamudalira kuti agwire nawo ntchito yaikulu yomanga

N’chifukwa chiyani atumiki a Yehova amagwira bwino ntchito komanso amalimbikira?

Aef 4:28; Akl 3:23

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Ge 24:10-21​—Rabeka anali wolimbikira ntchito ndipo anachita zambiri zoposa zimene mtumiki wa Abulahamu anamupempha kuchita

    • Afi 2:19-23​—Mtumwi Paulo anapatsa Timoteyo utumiki waukulu chifukwa choti anali wodzichepetsa komanso wolimbikira ntchito

N’chifukwa chiyani mtumiki wa Yehova safunika kukhala waulesi?

Miy 13:4; 18:9; 21:25, 26; Mla 10:18

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Miy 6:6-11​—Mfumu Solomo anagwiritsa ntchito chitsanzo cha nyerere pofuna kutiphunzitsa kufunika kogwira ntchito mwakhama komanso kuti tisamakhale anthu aulesi

N’chifukwa chiyani tifunika kugwira ntchito mwakhama kuti tipeze zofunika pa moyo wathu?

N’chifukwa chiyani tifunika kumagwira ntchito mwakhama kuti tipezere anthu am’banja lathu zinthu zofunika?

1Ti 5:8

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Ru 1:16, 17; 2:2, 3, 6, 7, 17, 18​—Rute yemwe anali mtsikana wamasiye ankagwira ntchito molimbikira ndipo anatha kusamalira apongozi ake a Naomi

    • Mt 15:4-9​—Yesu anadzudzula anthu amene ankanena kuti ankalephera kuthandiza makolo awo chifukwa choti akutumikira Mulungu zomwe zinali zosemphana ndi Malemba

N’chifukwa chiyani Akhristu ayenera kumagawana ndi ena zinthu zomwe azigwirira ntchito mwakhama?

Kodi tiyenera kukhala ndi maganizo otani pa nkhani za ndalama zomwe timapeza pambuyo pogwira ntchito?

Kodi timadziwa bwanji kuti Yehova amafuna kuti tizigwira bwino ntchito yathu komanso tizipeza zinthu zofunika pa moyo?

Mt 6:25, 30-32; Lu 11:2, 3; 2Ak 9:10

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Ge 31:3-13​—Labani sanachite zinthu zachilungamo kwa Yakobo koma Yehova anaona khama limene anasonyeza pogwira ntchito ndipo anamudalitsa

    • Ge 39:1-6, 20-23​—Yehova anadalitsa ntchito imene Yosefe ankagwira pa nthawi imene anali kapolo m’nyumba ya Potifara komanso ali m’ndende

N’chifukwa chiyani sitiyenera kulola kuti ntchito imene timagwira izitilepheretsa kupeza nthawi yotumikira Mulungu?

Sl 39:5-7; Mt 6:33; Yoh 6:27

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Lu 12:15-21​—Yesu anapereka fanizo losonyeza kuti n’kupanda nzeru kuganiza kuti kugwira ntchito n’cholinga choti tipeze ndalama zambiri n’kofunika kwambiri kuposa kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu

    • 1Ti 6:17-19​—Mtumwi Paulo anachenjeza Akhristu olemera za kuopsa kodzikweza ndipo anawalimbikitsa kuti “akhale olemera pa ntchito zabwino”

Kodi ndi mfundo ziti zimene zingatithandize kuti tisankhe mwanzeru ntchito yomwe tikufuna kugwira?

Kugwira ntchito ndi Yehova

Kodi Akhristu ayenera kugwira ntchito yofunika kwambiri iti?

N’chifukwa chiyani timafunitsitsa kuchita khama potumikira Yehova?

N’chifukwa chiyani sitiyenera kuyembekezera kuti atumiki a Yehova onse azichita zinthu mofanana?

Aga 6:3-5

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Mt 25:14, 15​—Fanizo la Yesu likusonyeza kuti iye samayembekezera kuti otsatira ake onse azigwira ntchito mofanana

    • Lu 21:2-4​—Yesu anayamikira chopereka cha mzimayi wamasiye yemwe anali wosauka ndi anachiona kuti chinali chamtengo wapatali

Kodi timapeza kuti mphamvu zoti tikwanitse kuchita utumiki umene Yehova watipatsa?

2Ak 4:7; Aef 3:20, 21; Afi 4:13

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 2Ti 4:17​—Mtumwi Paulo anayamikira mphamvu zimene anapatsidwa pa nthawi yomwe ankafunikira mphamvuzo

N’chifukwa chiyani timasangalala tikamachita khama pogwira ntchito limodzi ndi Yehova?