Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Okondedwa Abale ndi Alongo:

Chifukwa choti timakonda Mulungu ndi anthu, chikondichi chimatilimbikitsa kuti ‘tipite kukaphunzitsa anthu a mitundu yonse ndi kuwabatiza.’ (Mat. 28:19, 20; Maliko 12:28-31) Chikondi chenicheni ndi champhamvu. Chimakhudza mtima anthu ‘amaganizo abwino amene angawathandize kukapeza moyo wosatha.’—Machitidwe 13:48.

M’mbuyomu, tinkakonda kuloweza zitsanzo za ulaliki komanso kugawira mabuku. Koma panopo tikufuna kuwonjezera luso lathu lokambirana ndi anthu. Tikufuna kusonyeza kuti timakonda anthu pokambirana nawo nkhani zomwe zimawachititsa chidwi. Choncho tizikhala okonzeka kusintha zomwe tinakonzekera komanso tiziganizira zimene munthu aliyense akufunikira. Kodi kabukuka katithandiza bwanji kuti zimenezi zitheke?

Kabukuka kali ndi maphunziro 12, ofotokoza makhalidwe omwe tiyenera kuyesetsa kukhala nawo kuti tizikonda anthu ndi cholinga choti tiziphunzira nawo. Phunziro lililonse lachokera pa nkhani inayake ya m’Baibulo pomwe Yesu kapena mmodzi wa atumiki omwe ankalalikira mwakhama anasonyeza khalidwe linalake muutumiki. Cholinga chathu si kuloweza zomwe anachita koma kupeza njira zomwe tingasonyezere kuti timakonda anthu. Ngakhale kuti makhalidwe onsewa ndi ofunika pa utumiki wathu, komabe tiona mmene makhalidwe ena alili ofunika kwambiri pa ulendo woyamba, wobwereza kapenanso pochititsa phunziro la Baibulo.

Mukamaona zomwe zili m’phunziro lililonse, ganizirani mofatsa mmene mungasonyezere khalidwe lomwe mukuphunziralo mukamalankhula ndi anthu a m’dera lanu. Yesetsani kuti muzikonda kwambiri Yehova komanso anthu. Kuposa luso lililonse lomwe mungagwiritse ntchito, chikondi ndi chomwe chingakuthandizeni kuti mukwanitse cholinga chanu choti muziphunzira ndi anthu.

Tikuyamikira kwambiri mwayi waukulu womwe tili nawo wotumikira nanu limodzi mogwirizana. (Zef. 3:9) Yehova akudalitseni pamene mukupitiriza kukonda anthu ndi kuwaphunzitsa.

Ndife abale anu,

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova