ULENDO WOYAMBA
PHUNZIRO 1
Kuchita Chidwi ndi Anthu
Mfundo yaikulu: “Chikondi . . . sichisamala zofuna zake zokha.”—1 Akor. 13:4, 5.
Zomwe Yesu Anachita
1. Onerani VIDIYO, kapena werengani Yohane 4:6-9. Kenako kambiranani mafunso otsatirawa:
Zomwe Tikuphunzira kwa Yesu
2. Zikhoza kutiyendera bwino kwambiri tikamakambirana ndi anthu nkhani yomwe angachite nayo chidwi.
Zomwe Mungachite Potsanzira Yesu
3. Muzikhala okonzeka kusintha. Musamakakamire kuti muyambe kukambirana ndi munthu nkhani yokhayo yomwe mwakonzekera. Mungayambe ndi kukambirana nkhani ina yomwe ili m’kamwam’kamwa. Dzifunseni kuti:
4. Muzichita chidwi. Dzifunseni kuti:
-
‘Kodi munthuyu akutani? Kodi angakhale kuti akuganiza chiyani?’
-
‘Kodi zomwe wavala, mmene akuonekera kapena mmene pakhomo pake palili zikundiuza chiyani zokhudza chikhalidwe chake komanso zomwe amakhulupirira?’
5. Muzimvetsera.