ULENDO WOYAMBA

PHUNZIRO 2

Kukambirana Mwachibadwa

Kukambirana Mwachibadwa

Mfundo yaikulu: “Mawu onenedwa pa nthawi yoyenera ndi abwino kwambiri.”—Miy. 15:23.

Zomwe Filipo Anachita

1. Onerani VIDIYO, kapena werengani Machitidwe 8:30, 31. Kenako kambiranani mafunso otsatirawa:

  1.    Kodi Filipo anayamba bwanji kukambirana ndi munthuyo?

  2.   N’chifukwa chiyani kuyamba kukambirana mwanjira imeneyi kunali kwachibadwa? Nanga zimenezi zinathandiza bwanji munthuyo kuphunzira mfundo zatsopano za choonadi?

Zomwe Tikuphunzira kwa Filipo

2. Tikamakambirana ndi anthu mwachibadwa, zimawathandiza kukhala omasuka komanso savutika kuti atimvetsere.

Zomwe Mungachite Potsanzira Filipo

3. Muzichita chidwi ndi anthu. Mungathe kudziwa zambiri zokhudza munthuyo pongoona mmene waimira, akulankhulira komanso mmene nkhope yake ikuonekera. Kodi akuoneka kuti ali ndi chidwi kuti mulankhulane? Mungayambe kukambirana mfundo inayake ya m’Baibulo pofunsa kuti, “Kodi mukudziwa kuti . . . ?” Musakakamize munthu amene sakufuna kuti mukambirane.

4. Muzikhala oleza mtima. Musamakhale ndi maganizo ofuna kuyamba pompopompo kukambirana ndi munthu mfundo ya m’Baibulo. Dikirani mpaka patapezeka mpata wabwino kuti muyambe kukambirana mwachibadwa. Nthawi zina zingafunike kudikira mpaka pomwe mungadzachezenso ndi munthuyo.

5. Muzikhala okonzeka kusintha. Munthu akhoza kuyambitsa nkhani ina. Choncho muzikhala okonzeka kukambirana naye mfundo inayake yogwirizana ndi zomwe akufotokoza ngakhale kuti si zomwe munakonzekera.