Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

ULENDO WOYAMBA

PHUNZIRO 3

Kukoma Mtima

Kukoma Mtima

Mfundo yaikulu: “Chikondi . . . n’chokoma mtima.”​—1 Akor. 13:4.

Zomwe Yesu Anachita

1. Onerani VIDIYO, kapena werengani Yohane 9:1-7. Kenako kambiranani mafunso otsatirawa:

  1.    Kodi Yesu anayamba n’kutani, kuchiritsa munthuyo kapena kukambirana naye uthenga wabwino?​—Onani Yohane 9:35-38.

  2.   N’chifukwa chiyani tinganene kuti mmene Yesu anafikira, zinathandiza kuti munthuyo amvetsere uthenga wabwino?

Zomwe Tikuphunzira kwa Yesu

2. Nthawi zambiri munthu angachite chidwi ndi uthenga wathu akaona kuti tikuchita naye zinthu momuganizira.

Zomwe Mungachite Potsanzira Yesu

3. Muzikhala achifundo. Muziganizira mmene munthuyo akumvera.

  1.    Dzifunseni kuti: ‘Kodi akhoza kukhala kuti akuda nkhawa ndi chiyani? Kodi angasangalale nditamuuza zotani?’ Mukamaganizira zimenezi, mwachibadwa mudzamusonyeza kukoma mtima.

  2.   Muzisonyeza kuti mukumudera nkhawa pomumvetsera. Akakuuzani mmene akumvera ndi nkhani inayake kapena akakuuzani mavuto omwe akukumana nawo, musamasinthe nkhani.

4. Muzilankhula mokoma mtima komanso mwaulemu. Ngati mwakhudzika ndi munthuyo ndipo mukufunitsitsa kumuthandiza, adzazindikira zimenezo poona mmene mukulankhulira. Muzisamala ndi zomwe mukulankhula komanso mmene mukulankhulira kuti musamukhumudwitse.

5. Muzikhala ofunitsitsa kuthandiza. Yesetsani kupeza mipata yothandizira munthuyo. Mukamachita zinthu mokoma mtima simudzavutika kuyamba kukambirana ndi anthu.