Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

KUYAMBITSA MAKAMBILANO

Yohane 9:1-7

PHUNZILO 3

Kukoma Mtima

Kukoma Mtima

Mfundo Yaikulu: “Cikondi . . . n’cokoma mtima.”—1 Akor. 13:4.

Mmene Yesu Anaonetsela Khalidwe Limeneli

1. Tambani VIDIYO, kapena ŵelengani Yohane 9:1-7. Kenaka ganizilani mafunso otsatilawa:

  1.    Kodi Yesu anayambila citi—kucilitsa munthu wa khungu, kapena kum’lalikila uthenga wabwino?—Onani Yoh. 9:35-38.

  2.   N’cifukwa ciyani njila imeneyi inamufeŵetsa munthuyo kuti amvetsele uthenga wabwino?

Tiphunzilaponji kwa Yesu?

2. Munthu akaona kuti timasamala za iye, amamvetsela uthenga wathu.

Tengelani Citsanzo ca Yesu

3. Khalani wacifundo kwa munthuyo. Yesani kuganizila mmene munthuyo akumvela.

  1.    Dzifunseni kuti: ‘Kodi cikumudetsa nkhawa cingakhale ciyani? Ni mfundo iti ingam’thandize kapena kumukopa cidwi?’ Mukatelo mudzaonetsa cifundo cocokela pansi pa mtima, osati caciphamaso.

  2.   Onetsani kuti mumasamala za munthuyo pomumvetsela mwachelu. Ngati iye wakuuzani mmene amaonela nkhani ina yake, kapena wakuchulilani vuto limene ali nalo, musanyalanyaze.

4. Kambani mokoma mtima komanso mwaulemu. Ngati munthuyo mwamumvela cifundo, ndipo mufunadi kum’thandiza, makambidwe anu amaonetsa zimenezo. Sankhani mawu abwino, komanso kambani mokoma mtima. Pewani kukamba zimene zingakhumudwitse munthu.

5. Khalani na mtima wofuna kuthandiza. Pezani njila zimene mungamuthandizile munthuyo. Kuthandizilako anthu pa zinthu zina kumatsegula khomo la makambilano.

ONANINSO MALEMBA AWA

Aroma 12:15, 16; Agal. 6:10; Aheb. 13:16