Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

KUYAMBITSA MAKAMBILANO

Machitidwe 26:2, 3

PHUNZILO 4

Kudzicepetsa

Kudzicepetsa

Mfundo Yaikulu: ‘Modzicepetsa muziona ena kukhala okuposani.’—Afil. 2:3.

Mmene Paulo Anaonetsela Khalidwe Limeneli

1. Tambani VIDIYO, kapena ŵelengani Machitidwe 26:2, 3. Kenaka ganizilani pa mafunso otsatilawa:

  1.    Kodi Paulo anaonetsa bwanji kudzicepetsa pokamba na Mfumu Agiripa?

  2.   Kodi Paulo anaika motani patsogolo Yehova na Malemba m’malo mwa iyemwini?—Onani Mac. 26:22.

Tiphunzilaponji kwa Paulo?

2. Anthu amakopeka na uthenga wathu tikamakamba nawo modzicepetsa komanso mwaulemu.

Tengelani Citsanzo ca Paulo

3. Osalankhula modzionetsela. Pewani kulankhula monga mudziŵa zonse ndipo munthuyo palibe cimene adziŵa. Kambani naye mwaulemu.

4. Onetsani bwino lomwe kuti coonadi cimene muphunzitsa n’cocokela m’Baibo. Mfundo za m’Mawu a Mulungu zimatha kuwasintha mtima anthu. Pophunzitsa anthu Mawu a Mulungu timakhala tikumanga cikhulupililo cawo pa maziko olimba.

5. Khalanibe ofatsa. Osacita nthota pofuna kumveketsa mfundo yanu. Sitifuna kukangana ni anthu. Onetsani kudzicepetsa poika mtima wanu m’malo, komanso kucokapo mwamsanga ngati paoneka kuti pangabuke mkangano. (Miy. 17:14; Tito 3:2) Ngati tiyankha mofatsa, tingasiye khomo lili citsegukile kaamba ka makambilano abwino m’tsogolo.

ONANINSO MALEMBA AWA

Aroma. 12:16-18; 1 Akor. 8:1; 2 Akor. 3:5