Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

ULENDO WOYAMBA

PHUNZIRO 4

Kudzichepetsa

Kudzichepetsa

Mfundo yaikulu: “Modzichepetsa, muziona kuti ena amakuposani.”​—Afil. 2:3.

Zomwe Paulo Anachita

1. Onerani VIDIYO, kapena werengani Machitidwe 26:2, 3. Kenako kambiranani mafunso otsatirawa:

  1.    Kodi Paulo anasonyeza bwanji kudzichepetsa pomwe ankalankhula ndi Mfumu Agiripa?

  2.   Kodi Paulo anatani kuti anthu aziganizira kwambiri za Yehova komanso Malemba m’malo moganizira za iyeyo?​—Onani Machitidwe 26:22.

Zomwe Tikuphunzira kwa Paulo

2. Anthu amachita chidwi ndi uthenga wathu tikakhala odzichepetsa ndi aulemu.

Zomwe Mungachite Potsanzira Paulo

3. Muzilankhula mwaulemu. Pewani kudzionetsera ngati wodziwa chilichonse komanso ngati kuti winayo palibe chomwe akudziwa. Muzilankhula naye mwaulemu.

4. Muzisonyeza kuti uthenga wanu ukuchokera m’Baibulo. Mawu a Mulungu ali ndi mfundo zomwe zimafika anthu pa mtima. Tikamawagwiritsa ntchito, timathandiza anthu kukhala ndi chikhulupiriro cholimba.

5. Muzikhala odekha. Musamakakamire kuonetsa kuti mfundo yanu ndi imene ili yolondola. Sitifunikira kumakangana ndi anthu. Muzisonyeza kudzichepetsa pokhala odekha komanso kuchokapo zinthu zisanafike poipa. (Miy. 17:14; Tito 3:2) Mukakhala odekha mutha kudzalankhulanso ndi munthuyo nthawi ina.