Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

KUYAMBITSA MAKAMBILANO

Machitidwe 17:22, 23

PHUNZILO 5

Kukhala Wosamala

Kukhala Wosamala

Mfundo Yaikulu: “Nthawi zonse mawu anu azikhala acisomo.”—Akol. 4:6.

Mmene Paulo Anacitila Zimenezi

1. Tambani VIDIYO, kapena ŵelengani Machitidwe 17:22, 23. Kenaka ganizilani pa mafunso otsatilawa:

  1.    Kodi Paulo anamva bwanji poona anthu akulambila mafano ku Atene?—Onani Mac. 17:16.

  2.   M’malo mowadzudzula, kodi mosamala Paulo analoŵela bwanji ku zikhulupililo zawo kuti awagaŵile uthenga wabwino?

Tiphunzilaponji kwa Paulo?

2. Anthu angatimvetsele tikamasankha bwino zokamba, mozikambila, komanso nthawi yozikambila.

Tengelani Citsanzo ca Paulo

3. Kambani zimene munthuyo angagwilizane nazo. Mwacitsanzo, pokamba na munthu amene si wacipembedzo cacikhristu, mungafunikile kusintha mmene mumachulila za Baibo kapena Yesu.

4. Musafulumile kuwongolela munthu. Muloleni afotokoze za kukhosi kwake momasuka. Akakamba mfundo yosemphana na Baibo, dzigwileni musamukonze. (Yak. 1:19) Mukadekha na kumvetsela, mudzakhala na cithunzi cabwino ca zimene amakhulupilila na zifukwa zake.—Miy. 20:5.

5. Pezani zimene mungagwilizanepo ndipo muyamikileni. Munthuyo angakhale akukhulupilila na mtima wonse kuti ziphunzitso za cipembedzo cake ni zoona. Conco, yambilani pa mfundo imene nonse aŵili mukuivomeleza. Pang’ono-m’pang’ono, muthandizeni kumvetsa bwino zimene Baibo imaphunzitsa.

ONANINSO MALEMBA AWA

Miy. 25:15; 2 Tim. 2:23-26; 1 Pet. 3:15