Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

ULENDO WOYAMBA

PHUNZIRO 6

Kulimba Mtima

Kulimba Mtima

Mfundo yaikulu: “Tinalimba mtima mothandizidwa ndi Mulungu wathu kuti tikuuzeni uthenga wabwino wa Mulungu.”​—1 Ates. 2:2.

Zomwe Yesu Anachita

1. Onerani VIDIYO, kapena werengani Luka 19:1-7. Kenako kambiranani mafunso otsatirawa:

  1.    Kodi mwina n’chiyani chinkachititsa anthu ena kuti azipewa Zakeyu?

  2.   Ngakhale zinali choncho, n’chiyani chinachititsa Yesu kuti amuuze uthenga wabwino?

Zomwe Tikuphunzira kwa Yesu

2. Tiyenera kukhala olimba mtima kuti tilalikire uthenga wa Ufumu kwa aliyense.

Zomwe Mungachite Potsanzira Yesu

3. Muzidalira Yehova. Mzimu wa Mulungu unamupatsa Yesu mphamvu kuti alalikire. Ifenso ungatipatse mphamvu. (Mat. 10:19, 20; Luka 4:18) Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kukhala olimba mtima kuti mukwanitse kulalikira anthu omwe mukuchita nawo mantha.​—Mac. 4:29.

4. Musamaweruze anthu. Tingamazengereze kulalikira anthu ena chifukwa cha maonekedwe awo, chuma chawo, mmene amakhalira kapena chifukwa cha zomwe amakhulupirira. Komabe muzikumbukira kuti:

  1.    Yehova komanso Yesu yekha, ndi omwe amaona za mumtima mwa munthu.

  2.   Musamaganize kuti Yehova sangamuchitire chifundo.

5. Muzilimba mtima komanso kuchita zinthu mosamala. (Mat. 10:16) Musamakangane ndi anthu. Ngati munthuyo sakufuna kumvetsera uthenga wabwino kapenanso ngati mukuona kuti moyo wanu uli pangozi, chokanipo mwaulemu.​—Miy 17:14.