ULENDO WOYAMBA Luka 19:1-7 PHUNZIRO 6 Kulimba Mtima YAMBANI Kulimba Mtima Pepani, zalephereka. Koperani Vidiyoyi Onetsani Kaonekedwe ka Mawu Bisani Kaonekedwe ka Mawu Mfundo yaikulu: “Tinalimba mtima mothandizidwa ndi Mulungu wathu kuti tikuuzeni uthenga wabwino wa Mulungu.”—1 Ates. 2:2. Zomwe Yesu Anachita VIDIYO: Yesu Analalikira Zakeyu 1. Onerani VIDIYO, kapena werengani Luka 19:1-7. Kenako kambiranani mafunso otsatirawa: Kodi mwina n’chiyani chinkachititsa anthu ena kuti azipewa Zakeyu? Ngakhale zinali choncho, n’chiyani chinachititsa Yesu kuti amuuze uthenga wabwino? Zomwe Tikuphunzira kwa Yesu 2. Tiyenera kukhala olimba mtima kuti tilalikire uthenga wa Ufumu kwa aliyense. Zomwe Mungachite Potsanzira Yesu 3. Muzidalira Yehova. Mzimu wa Mulungu unamupatsa Yesu mphamvu kuti alalikire. Ifenso ungatipatse mphamvu. (Mat. 10:19, 20; Luka 4:18) Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kukhala olimba mtima kuti mukwanitse kulalikira anthu omwe mukuchita nawo mantha.—Mac. 4:29. 4. Musamaweruze anthu. Tingamazengereze kulalikira anthu ena chifukwa cha maonekedwe awo, chuma chawo, mmene amakhalira kapena chifukwa cha zomwe amakhulupirira. Komabe muzikumbukira kuti: Yehova komanso Yesu yekha, ndi omwe amaona za mumtima mwa munthu. Musamaganize kuti Yehova sangamuchitire chifundo. 5. Muzilimba mtima komanso kuchita zinthu mosamala. (Mat. 10:16) Musamakangane ndi anthu. Ngati munthuyo sakufuna kumvetsera uthenga wabwino kapenanso ngati mukuona kuti moyo wanu uli pangozi, chokanipo mwaulemu.—Miy 17:14. ONANINSO MALEMBA AWA Mac. 4:31; Aef. 6:19, 20; 2 Tim. 1:7 Yam'mbuyo Yotsatira Sindikizani Patsani ena Patsani ena Kulimba Mtima MUZIKONDA ANTHU—MUZIWAPHUNZITSA Kulimba Mtima Chinenero Chamanja cha ku Malawi Kulimba Mtima https://cms-imgp.jw-cdn.org/img/p/1102023306/univ/art/1102023306_univ_sqr_xl.jpg lmd 6