Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

KUBWELELAKO

Machitidwe 19:8-10

PHUNZILO 7

Khama

Khama

Mfundo Yaikulu: “Anapitiliza mwakhama kuphunzitsa ndi kulengeza uthenga wabwino.”—Mac. 5:42.

Mmene Paulo Anaonetsela Khalidwe Limeneli

1. Tambani VIDIYO, kapena ŵelengani Machitidwe 19:8-10. Kenaka ganizilani pa mafunso otsatilawa:

  1.    M’malo mokhwethemuka cifukwa ca anthu omutsutsa, kodi Paulo anacita bwanji kuti awathandizebe anthu acidwi?

  2.   Kodi Paulo anabwelelako kangati kuti akaphunzitse anthu acidwi, ndipo anacita zimenezi kwa utali wotani?

Tiphunzilaponji kwa Paulo?

2. Kuti tipange maulendo obwelelako ofika pamtima, na kuyambitsa maphunzilo a Baibo, tiyenela kutayilapo nthawi komanso kucita khama.

Tengelani Citsanzo ca Paulo

3. Sankhani tsiku lokomela munthuyo. Dzifunseni kuti: ‘Kodi iye amapeza liti mpata wabwino, ndipo nthawi yanji? Nanga angakonde nizicezela naye kuti?’ Yesetsani kubwelelako ngakhale pamene si nthawi yabwino kwa inu.

4. Panganani pasadakhale. Nthawi zonse mukamaliza makambilano anu, panganani za tsiku na nthawi pamene mudzacezenso. Yesetsani kusunga cipangano.

5. Khalanibe na cidalilo. Musafulumile kuganiza kuti munthuyo alibe cidwi cabe cifukwa sapezeka-pezeka pa nyumba, kapena amakhala wotangwanika kwambili. (1 Akor. 13: 4, 7) Ngakhale n’telo, samalani nawo anthu amene angangokutayilani nthawi.—1 Akor. 9:26.

ONANINSO MALEMBA AWA

Mac. 10:42; 1 Akor. 9:22, 23; 2 Akor. 4:1; Agal. 6:9