ULENDO WOBWEREZA

PHUNZIRO 8

Kuleza Mtima

Kuleza Mtima

Mfundo yaikulu: “Chikondi n’choleza mtima.”​—1 Akor. 13:4.

Zomwe Yesu Anachita

1. Onerani VIDIYO, kapena werengani Yohane 7:3-5 ndi 1 Akorinto 15:3, 4, 7. Kenako kambiranani mafunso otsatirawa:

  1.    Kodi poyamba azichimwene ake a Yesu ankalandira bwanji uthenga wake?

  2.   Tikutsimikiza bwanji kuti Yesu sanamugwere ulesi mchimwene wake Yakobo?

Zomwe Tikuphunzira kwa Yesu

2. Tiyenera kukhala oleza mtima chifukwa anthu ena zimawatengera nthawi yaitali kuti alandire uthenga wabwino.

Zomwe Mungachite Potsanzira Yesu

3. Muziyesa njira ina. Ngati munthu sakuvomereza mwamsanga kuti muziphunzira naye, musamukakamize. Ngati ndi zotheka, mungamuonetse mavidiyo kapena kukambirana naye nkhani za m’mabuku athu pofuna kumuthandiza kudziwa mmene phunziro la Baibulo limachitikira komanso mmene angapindulire.

4. Musamamuyerekezere ndi munthu wina. Anthu amasiyana. Ngati wachibale kapena amene tinamulalikirapo nthawi ina akuzengereza kuti tiyambe kuphunzira naye, ganizirani chomwe chikuchititsa zimenezi. Kodi amakonda mwambo winawake wachipembedzo? Kodi akunyozedwa ndi achibale kapenanso anzake? M’patseni mpata woganizira zomwe mwamuuza kuti aone yekha ubwino wotsatira mfundo za m’Baibulo.

5. Muzimupempherera. Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kukhala ndi luso komanso kuti musagwe ulesi. Mupempheni kuti akupatseni nzeru kuti muthe kuzindikira ngati munthuyo alibe chidwi kuti musiye kumuyendera.​—1 Akor. 9:26.