Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

ULENDO WOBWEREZA

PHUNZIRO 9

Kukhala Achifundo

Kukhala Achifundo

Mfundo yaikulu: “Muzisangalala ndi anthu amene akusangalala ndipo muzilira ndi anthu amene akulira.”​—Aroma 12:15.

Zomwe Yesu Anachita

1. Onerani VIDIYO, kapena werengani Maliko 6:30-34. Kenako kambiranani mafunso otsatirawa:

  1.    N’chifukwa chiyani Yesu ndi atumwi ake anaganiza zopita “kwaokhaokha”?

  2.   N’chiyani chinachititsa Yesu kuti alalikire gulu la anthulo?

Zomwe Tikuphunzira kwa Yesu

2. Chifundo chimatilimbikitsa kuti tizithandiza anthu, osati kungofuna kuwalalikira kokha.

Zomwe Mungachite Potsanzira Yesu

3. Muzimvetsera mwatcheru. Muzimupatsa mpata wofotokoza maganizo ake. Musamamudule mawu kapena kunyalanyaza zomwe akunena. Mukamamvetsera anthu mwatcheru, adzaona kuti mumalemekeza maganizo awo.

4. Muzimuganizira. Potengera zomwe mwaona pocheza naye, dzifunseni kuti:

  1.    ‘N’chifukwa chiyani akufunikira kumva choonadi?’

  2.   ‘Kodi kuphunzira Baibulo kungamuthandize bwanji pa moyo wake komanso kuti akhale ndi tsogolo labwino?’

5. Muzikambirana naye zinthu zomwe zingamuthandize. Pasanapite nthawi yaitali, musonyezeni mmene phunziro la Baibulo lingamuthandizire pa zochitika za tsiku ndi tsiku komanso kupeza mayankho a mafunso ake.