Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

KUBWELELAKO

PHUNZILO 9

Cifundo

Cifundo

Mfundo Yaikulu: “Sangalalani ndi anthu amene akusangalala. Lilani ndi anthu amene akulila.”—Aroma 12:15.

Mmene Yesu Anaonetsela Khalidwe Limeneli

1. Tambani VIDIYO, kapena ŵelengani Maliko 6:30-34. Kenaka ganizilani pa mafunso otsatilawa:

  1.    N’cifukwa ciyani Yesu na atumwi ake anafuna “kupita kwaokhaokha ku malo opanda anthu”?

  2.   N’ciyani cinapangitsa Yesu kuti awaphunzitsebe anthuwo?

Tiphunzilaponji kwa Yesu?

2. Cifundo cimatipangitsa kuwaganizila anthu, osati kungoganiza za uthenga wathu cabe.

Tengelani Citsanzo ca Yesu

3. Muzimvetsela mosamala. Lolani munthuyo akambe maganizo ake momasuka. Musam’dule mawu, ndiponso musangoponya ku nkhongo zimene wakamba, maganizo ake, nkhawa zake, kapena mfundo zake zotsutsa. Pomumvetsela mwachelu, mumaonetsa kuti mufunadi kumvetsa maganizo ake.

4. Sinkhasinkhani za munthu wacidwiyo. Malinga ni zimene mwakambilanapo naye, dzifunseni kuti:

  1.    ‘N’cifukwa ninji munthu uyu afunikiladi kumva coonadi?’

  2.   ‘Kodi kuphunzila Baibo kungam’pindulile bwanji pa umoyo wake wa tsiku na tsiku, kutinso akhale na tsogolo labwino?’

5. Kambilanani naye zinthu zimene zingam’thandizedi pa umoyo wake. Pasanapite nthawi yaitali, muonetseni mmene phunzilo la Baibo lingayankhile mafunso ake, na mmene lingam’pindulile pa umoyo wake.

ONANINSO MALEMBA AWA

Aroma 10:13, 14; Afil. 2:3, 4; 1 Pet. 3:8