ULENDO WOBWEREZA Maliko 6:30-34 PHUNZIRO 9 Kukhala Achifundo YAMBANI Kukhala Achifundo Pepani, zalephereka. Koperani Vidiyoyi Onetsani Kaonekedwe ka Mawu Bisani Kaonekedwe ka Mawu Mfundo yaikulu: “Muzisangalala ndi anthu amene akusangalala ndipo muzilira ndi anthu amene akulira.”—Aroma 12:15. Zomwe Yesu Anachita VIDIYO: Yesu Anachitira Chifundo Gulu la Anthu 1. Onerani VIDIYO, kapena werengani Maliko 6:30-34. Kenako kambiranani mafunso otsatirawa: N’chifukwa chiyani Yesu ndi atumwi ake anaganiza zopita “kwaokhaokha”? N’chiyani chinachititsa Yesu kuti alalikire gulu la anthulo? Zomwe Tikuphunzira kwa Yesu 2. Chifundo chimatilimbikitsa kuti tizithandiza anthu, osati kungofuna kuwalalikira kokha. Zomwe Mungachite Potsanzira Yesu 3. Muzimvetsera mwatcheru. Muzimupatsa mpata wofotokoza maganizo ake. Musamamudule mawu kapena kunyalanyaza zomwe akunena. Mukamamvetsera anthu mwatcheru, adzaona kuti mumalemekeza maganizo awo. 4. Muzimuganizira. Potengera zomwe mwaona pocheza naye, dzifunseni kuti: ‘N’chifukwa chiyani akufunikira kumva choonadi?’ ‘Kodi kuphunzira Baibulo kungamuthandize bwanji pa moyo wake komanso kuti akhale ndi tsogolo labwino?’ 5. Muzikambirana naye zinthu zomwe zingamuthandize. Pasanapite nthawi yaitali, musonyezeni mmene phunziro la Baibulo lingamuthandizire pa zochitika za tsiku ndi tsiku komanso kupeza mayankho a mafunso ake. ONANINSO MALEMBA AWA Aroma 10:13, 14; Afil. 2:3, 4; 1 Pet. 3:8 Yam'mbuyo Yotsatira Sindikizani Patsani ena Patsani ena Kukhala Achifundo MUZIKONDA ANTHU—MUZIWAPHUNZITSA Kukhala Achifundo Chinenero Chamanja cha ku Malawi Kukhala Achifundo https://cms-imgp.jw-cdn.org/img/p/1102023309/univ/art/1102023309_univ_sqr_xl.jpg lmd 9