Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

KUPANGA OPHUNZILA

PHUNZILO 11

Kuphunzitsa M’njila Yosavuta Kumva

Kuphunzitsa M’njila Yosavuta Kumva

Mfundo Yaikulu: ‘Muzilankhula zomveka.’—1 Akor. 14:9.

Mmene Yesu Anacitila Zimenezi

1. Tambani VIDIYO, kapena ŵelengani Mateyu 6:25-27. Kenaka ganizilani pa mafunso otsatilawa:

  1.    Kodi Yesu anafanizila motani mmene Yehova amatisamalila?

  2.   Ngakhale kuti Yesu anali kudziŵa zambili zokhudza mbalame, kodi anasankha mfundo iti yosavuta kumva imene anaphunzitsilapo? N’cifukwa ciyani njila imeneyi ili yothandiza ngako?

Tiphunzilaponji kwa Yesu?

2. Tikamaphunzitsa mosavuta kumva, anthu adzakumbukila zimene tawaphunzitsa, komanso zidzawafika pa mtima.

Tengelani Citsanzo ca Yesu

3. Musamafotokoze zambili. M’malo mofotokoza zonse zimene mudziŵa pa nkhani imene mukuphunzitsa, kambani maka-maka mfundo zili m’buku limene mukuphunzila. Mukafunsa funso, yembekezelani moleza mtima kuti wophunzila wanu ayankhe. Ngati yankho salidziŵa kapena wayankha zosemphana ni zimene Baibo imaphunzitsa, funsani mafunso oonjezela omuthandiza kuimvetsa nkhaniyo. Akaimvetsa mfundo yaikulu, pitani patsogolo.

4. Gwilitsani nchito zimene akudziŵa kale kuti amvetse mfundo zatsopano. Mwacitsanzo, musanayambe kuphunzila za ciukitso ca akufa, mungamufunseko zimene anaphunzila kale za mkhalidwe wa akufa.

5. Seŵenzetsani mafanizo, koma mosamala. Musanapeleke fanizo dzifunseni kuti:

  1.    ‘Kodi fanizo ili n’losavuta kumva?’

  2.   ‘Kodi wophunzila wanga adzalimva mosavuta?’

  3.   ‘Kodi lidzamuthandiza kukumbukila mfundo yaikulu—m’malo mwa fanizo lokhalo?’

ONANINSO MALEMBA AWA

Mat. 11:25; Yoh. 16:12; 1 Akor. 2:1