KUPHUNZITSA ANTHU

PHUNZIRO 11

Kuphunzitsa M’njira Yosavuta

Kuphunzitsa M’njira Yosavuta

Mfundo yaikulu: ‘Muzilankhula zomveka.’​—1 Akor. 14:9.

Zomwe Yesu Anachita

1. Onerani VIDIYO, kapena werengani Mateyu 6:25-27. Kenako kambiranani mafunso otsatirawa:

  1.    Kodi Yesu anasonyeza bwanji mmene Yehova amatikondera?

  2.   Ngakhale kuti Yesu ankadziwa zambiri zokhudza mbalame, koma kodi anangosankha kutchula mfundo iti? N’chifukwa chiyani imeneyi inali njira yabwino yophunzitsira?

Zomwe Tikuphunzira kwa Yesu

2. Tikamaphunzitsa m’njira yosavuta kumva, tidzathandiza anthu kukumbukira zomwe tawaphunzitsa ndipo zidzawafika pa mtima.

Zomwe Mungachite Potsanzira Yesu

3. Musamalankhule kwambiri. M’malo mofotokoza chilichonse chomwe mukudziwa pa nkhaniyo, gwiritsani ntchito mfundo zomwe zili m’mutu womwe mukuphunzirawo. Mukafunsa funso, muzimudikira moleza mtima kuti ayankhe. Ngati sakudziwa yankho kapena ngati wayankha zosemphana ndi zomwe Baibulo limaphunzitsa, funsani mafunso owonjezera omuthandiza kuganizira nkhaniyo. Wophunzirayo akangomvetsa mfundo yaikulu, pitani pa mfundo ina.

4. Muzithandiza wophunzira kugwirizanitsa mfundo zatsopano ndi zomwe akudziwa kale. Mwachitsanzo, musanayambe kukambirana nkhani ya kuuka kwa akufa, bwerezani mwachidule zomwe munaphunzira kale zokhudza mmene akufa alili.

5. Muzigwiritsa ntchito mafanizo mwanzeru. Musananene fanizo, dzifunseni kuti:

  1.    ‘Kodi fanizoli ndi losavuta kumva?’

  2.   ‘Kodi angamvetse mfundo ya mufanizoli mosavuta?’

  3.   ‘Kodi lingamuthandize kukumbukira mfundo yaikulu, osati fanizo lokhalo?’