Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

KUPHUNZITSA ANTHU

PHUNZIRO 12

Kulangiza Molimba Mtima

Kulangiza Molimba Mtima

Mfundo yaikulu: “Mafuta ndi zofukiza zonunkhira n’zimene zimasangalatsa mtima. Chimodzimodzinso kukhala ndi mnzako wabwino amene amakupatsa malangizo mosapita m’mbali.”​—Miy. 27:9.

Zomwe Yesu Anachita

1. Onerani VIDIYO, kapena werengani Maliko 10:17-22. Kenako kambiranani mafunso otsatirawa:

  1.    Kodi Yesu angakhale kuti anaona makhalidwe abwino ati mwa wolamulira wachinyamatayu?

  2.   N’chifukwa chiyani pankafunika chikondi komanso kulimba mtima kuti amupatse malangizo?

Zomwe Tikuphunzira kwa Yesu

2. Kuti wophunzira wathu apite patsogolo mwauzimu, tiyenera kumulankhula mwachikondi koma mosabisa mawu.

Zomwe Mungachite Potsanzira Yesu

3. Muzimuthandiza kukhala ndi zolinga komanso mmene angazikwaniritsire.

  1.    Muzigwiritsa ntchito mbali yakuti “Zolinga,” m’buku la Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale.

  2.   Muzimuthandiza kudziwa zomwe angachite kuti akwaniritse zolinga zing’onozing’ono komanso zikuluzikulu.

  3.   Muzimuyamikira chifukwa cha mmene akupitira patsogolo.

4. Muzizindikira zomwe zingamulepheretse kupita patsogolo, n’kumuthandiza.

  1.    Dzifunseni kuti:

    • ‘N’chiyani chomwe chingakhale kuti chikumulepheretsa kupita patsogolo kuti abatizidwe?’

    • Ndingatani kuti ndimuthandize?

  2.   Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kulankhula mwachikondi komanso mosabisa mawu pothandiza wophunzira wanu.

5. Muzisiya kuphunzira naye ngati sakupita patsogolo.

  1.    Dzifunseni mafunso awa kuti mudziwe ngati phunzirolo likupitadi patsogolo kapena ayi:

    • ‘Kodi amagwiritsa ntchito zomwe amaphunzira?’

    • ‘Kodi amapezeka pamisonkhano komanso kuuza ena zokhudza choonadi?’

    • ‘Popeza waphunzira kwa nthawi yotalikirapo, kodi akufuna kukhala wa Mboni za Yehova?’

  2.   Ngati wophunzira Baibulo sakupita patsogolo:

    • Mufunseni chimene chikumulepheretsa kuti asapite patsogolo.

    • Muuzeni mokoma mtima chifukwa chake simungapitirize kuphunzira naye.

    • Muuzeni zomwe angachite ngati atadzafunanso kupitiriza kuphunzira.