Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

KUPANGA OPHUNZILA

PHUNZILO 12

Kulimba Mtima

Kulimba Mtima

Mfundo Yaikulu: “Mafuta ndi zofukiza zonunkhila n’zimene zimasangalatsa mtima, cimodzimodzinso kukoma kwa mnzako cifukwa ca malangizo ake ocokela pansi pa mtima.”—Miy. 27:9.

Mmene Yesu Anaonetsela Khalidwe Limeneli

1. Tambani VIDIYO, kapena ŵelengani Maliko 10:17-22. Kenaka ganizilani pa mafunso otsatilawa:

  1.    Kodi n’kutheka Yesu anaona makhalidwe abwino ati mwa wolamulila wacinyamata ameneyu?

  2.   N’cifukwa ciyani Yesu anafunikila cikondi komanso kulimba mtima kuti am’patse uphungu mnyamatayo?

Tiphunzilaponji kwa Yesu?

2. Ophunzila athu tizilankhula nawo mwacikondi komanso mosapita m’mbali kuti apite bwino patsogolo kuuzimu.

Tengelani Citsanzo ca Yesu

3. Thandizani wophunzila wanu kudziikila zolinga na kuzikwanilitsa.

  1.    Seŵenzetsani mbali yakuti “Colinga” m’buku la Kondwelani na Moyo Kwamuyaya!

  2.   Thandizani wophunzila wanu kudziŵa zimene ayenela kucita kuti akwanilitse zolinga zing’ono-zing’ono komanso zikulu-zikulu.

  3.   Muyamikileni nthawi zonse pamene akupita patsogolo.

4. Zindikilani zopinga zimene zingam’bweze kumbuyo, ndipo m’thandizeni kuti azigonjetse.

  1.    Dzifunseni kuti:

    • ‘Ngati wophunzila wanga sakupita patsogolo kuti akabatizike, cikum’pinga n’ciyani?’

    • ‘Nanga ningam’thandize bwanji?’

  2.   Pemphelelani kulimba mtima kuti mukathe kukambilana naye, mwacikondi komabe mosapita m’mbali, zimene afunikila kucita.

5. Asiyeni maphunzilo amtatakuya osapita patsogolo.

  1.    Kuti mudziŵe ngati wophunzila wanu akupita patsogolo kapena ayi, dzifunseni kuti:

    • ‘Kodi amagwilitsa nchito zimene akuphunzila?’

    • ‘Kodi amapezeka ku misonkhano ya mpingo, ndipo amauzako ena zimene amaphunzila?’

    • ‘Popeza waphunzila kwa nthawi ndithu, kodi lomba akufuna kukhala Mboni?’

  2.   Ngati wophunzila Baibo sakufuna kupita patsogolo, citani izi:

    • M’pempheni kuti aganizilepo pa cimene cikumulepheletsa.

    • Mosamala komanso mwaubwino, m’fotokozeleni cifukwa cake simudzapitiliza kuphunzila naye.

    • Muuzeni zofunikila kugwililapo nchito ngati akufuna kuti m’tsogolo mukayambilenso kuphunzila naye.

ONANINSO MALEMBA AWA

Sal. 141:5; Miy. 25:12; 27:6; 1 Akor. 9:26; Akol. 4:5, 6