Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

ZAKUMAPETO A

Mfundo za m’Baibo Zimene Timafunitsitsa Kuphunzitsa Anthu

Mfundo za m’Baibo Zimene Timafunitsitsa Kuphunzitsa Anthu

Yesu anakamba kuti anthu oona mtima adzazindikila coonadi akacimva. (Yoh. 10:4, 27) Conco nthawi zonse pokamba na anthu, timafuna kuwauza coonadi ca m’Baibo cosavuta kumva. Pofuna kuuzako munthu mfundo ya m’Baibo, yesani kuyamba motele: “Kodi mudziŵa kuti . . . ?” kapena kuti “Kodi munamvelapo zakuti . . . ?” Ndiyeno muŵelengeleni malemba amene patsamila mfundoyo. Mwa kungokambilana mfundo ya m’Baibo yosavuta, mungabyale mu mtima mwake mbewu ya coonadi, imene Mulungu angaikulitse!—1 Akor. 3:6, 7.

 TSOGOLO

  1. 1. Zocitika pa dziko na makhalidwe a anthu zionetsa kuti posacedwa zinthu zidzasintha.—Mat. 24:3, 7, 8; Luka 21:10, 11; 2 Tim. 3:1-5.

  2. 2. Dziko lapansi silidzawonongedwa konse.—Sal. 104:5; Mlal. 1:4.

  3. 3. Zacilengedwe zimene zawonongedwa zidzakonzedwa n’kukhalanso zabwino-bwino.—Yes. 35:1, 2; Chiv. 11:18.

  4. 4. Munthu aliyense adzakhala na thanzi langwilo.—Yes. 33:24; 35:5, 6.

  5. 5. Mukhoza kudzakhala na moyo kwamuyaya pa dziko lapansi.—Sal. 37:29; Mat. 5:5.

 BANJA

  1. 6. Mwamuna ayenela kukonda mkazi wake “mmene amadzikondela yekha.”—Aef. 5:33; Akol. 3:19.

  2. 7. Mkazi azicitila mwamuna wake ulemu waukulu.—Aef. 5:33; Akol. 3:18.

  3. 8. Mwamuna na mkazi wake akhale okhulupilika kwa wina na mnzake.—Mal. 2:16; Mat. 19:4-6, 9; Aheb. 13:4.

  4. 9. Ana amene amalemekeza makolo awo na kuwamvela, zinthu zidzawayendela bwino.—Miy. 1:8, 9; Aef. 6:1-3.

NASA, ESA and the Hubble Heritage Team (STScI/AURA)-ESA/Hubble Collaboration. Licensed under CC BY 4.0. Source.

 MULUNGU

  1. 10. Mulungu ali na dzina lake-lake.—Sal. 83:18; Yer. 10:10.

  2. 11. Mulungu anatipatsa uthenga wofunika kwambili.— 2 Tim. 3:16, 17; 2 Pet. 1:20, 21.

  3. 12. Mulungu sakondela, alibe tsankho.—Deut. 10:17; Mac. 10:34, 35.

  4. 13. Mulungu amafuna kutithandiza.—Sal. 46:1; 145:18, 19.

 PEMPHELO

  1. 14. Mulungu amafuna kuti tizipemphela kwa iye.—Sal. 62:8; 65:2; 1 Pet. 5:7.

  2. 15. Baibo imatiphunzitsa mopemphelela.—Mat. 6:7-13; Luka 11:1-4.

  3. 16. Tiyenela kumapemphela kaŵili-kaŵili.—Mat. 7:7, 8; 1 Ates. 5:17.

 YESU

  1. 17. Yesu anali mphunzitsi waluso, ndipo ulangizi wake ni wothandiza ngakhale masiku ano.—Mat. 6:14, 15, 34; 7:12.

  2. 18. Yesu ananenelatu zocitika zimene tikuona masiku ano.—Mat. 24:3, 7, 8, 14; Luka 21:10, 11.

  3. 19. Yesu ni Mwana wake wa Mulungu.—Mat. 16:16; Yoh. 3:16; 1 Yoh. 4:15.

  4. 20. Yesu sali Mulungu Wamphamvuzonse.—Yoh. 14:28; 1 Akor. 11:3.

Based on NASA/Visible Earth imagery

 UFUMU WA MULUNGU

  1. 21. Ufumu wa Mulungu ni boma lenileni lakumwamba.—Dan. 2:44; 7:13, 14; Mat. 6:9, 10; Chiv. 11:15.

  2. 22. Ufumu wa Mulungu udzaloŵa m’malo maboma onse a anthu.—Sal. 2:7-9; Dan. 2:44.

  3. 23. Ufumu wa Mulungu ndiwo yankho lokha ku mavuto onse amene anthu akukumana nawo.—Sal. 37:10, 11; 46:9; Yes. 65:21-23.

 MAVUTO

  1. 24. Mulungu sindiye amacititsa mavuto athu.—Deut. 32:4; Yak. 1:13.

  2. 25. Satana ndiye akulamulila dzikoli.—Luka 4:5, 6; 1 Yoh. 5:19.

  3. 26. Mulungu amakhudzidwa na mavuto anu.—Sal. 34:17-19; Yes. 41:10, 13.

  4. 27. Posacedwa Mulungu adzacotsapo mavuto onse.—Yes. 65:17; Chiv. 21:3, 4.

 IMFA

  1. 28. Akufa sadziŵa kanthu; sakuvutika na ciliconse.—Mlal. 9:5; Yoh. 11:11-14.

  2. 29. Akufa sangatithandize kapena kutivulaza.—Sal. 146:4; Mlal. 9:6, 10.

  3. 30. Okondedwa athu amene anamwalila adzaukitsidwa.—Yobu 14:13-15; Yoh. 5:28, 29; Mac. 24:15.

  4. 31. “Imfa sidzakhalaponso.”—Chiv. 21:3, 4; Yes. 25:8.

 CIPEMBEDZO

  1. 32. Si zipembedzo zonse zimene Mulungu amakondwela nazo.—Yer. 7:11; Mat. 7:13, 14, 21-23.

  2. 33. Cinyengo Mulungu amadana naco.—Yes. 29:13; Mika 3:11; Maliko 7:6-8.

  3. 34. Cipembedzo coona cimadziŵika na cikondi ceniceni.—Mika 4:3; Yoh. 13:34, 35.