ZAKUMAPETO A

Choonadi Chomwe Timakonda Kuphunzitsa Anthu

Choonadi Chomwe Timakonda Kuphunzitsa Anthu

Yesu ananena kuti anthu a mtima wabwino akangomva choonadi, savutika kuchizindikira. (Yoh. 10:4, 27) Choncho tikamalankhula ndi anthu, tiziwauza mfundo inayake yosavuta kumva ya choonadi cha m’Baibulo. Tingachite zimenezi pofunsa kuti: “Kodi mukudziwa kuti . . . ?” kapena “Munayamba mwamvapo kuti . . . ?” Kenako gwiritsani ntchito lemba limodzi kapena angapo ogwirizana ndi mfundoyo. Kungonena mfundo inayake yosavuta ya m’Baibulo, mukhoza kudzala mbewu ya choonadi mumtima mwa munthu ndipo Mulungu akhoza kuthandiza kuti mbewuyo ikule.​—1 Akor. 3:6, 7.

 ZAM’TSOGOLO

  1. 1. Zinthu zomwe zikuchitika masiku ano zikusonyeza kuti posachedwapa zinthu zisintha.​—Mat. 24:3, 7, 8; Luka 21:10, 11; 2 Tim. 3:1-5.

  2. 2. Dziko lapansili silidzawonongedwa.​—Sal. 104:5; Mlal. 1:4.

  3. 3. Chilengedwe chidzabwereranso mwakale.​—Yes. 35:1, 2; Chiv. 11:18.

  4. 4. Aliyense adzakhala ndi moyo wathanzi.​—Yes. 33:24; 35:5, 6.

  5. 5. Mungathe kudzakhala ndi moyo padzikoli mpaka kalekale.​—Sal. 37:29; Mat. 5:5.

 BANJA

  1. 6. Mwamuna ayenera ‘kukonda mkazi wake ngati mmene amadzikondera yekha.’​—Aef. 5:33; Akol. 3:19.

  2. 7. Mkazi ayenera ‘kulemekeza kwambiri mwamuna wake.’​—Aef. 5:33; Akol. 3:18.

  3. 8. Mwamuna ndi mkazi wake ayenera kukhala okhulupirika.​—Mal. 2:16; Mat. 19:4-6, 9; Aheb. 13:4.

  4. 9. Ana omwe amalemekeza ndi kumvera makolo awo zinthu zimawayendera bwino.​—Miy. 1:8, 9; Aef. 6:1-3.

 MULUNGU

  1. 10. Mulungu ali ndi dzina.​—Sal. 83:18; Yer. 10:10.

  2. 11. Mulungu anatipatsa uthenga wofunika.​—2 Tim. 3:16, 17; 2 Pet. 1:20, 21.

  3. 12. Mulungu alibe tsankho ndipo sakondera.​—Deut. 10:17; Mac. 10:34, 35.

  4. 13. Mulungu amafuna kutithandiza.​—Sal. 46:1; 145:18, 19

 KUPEMPHERA

  1. 14. Mulungu amafuna kuti tizipemphera kwa iye.​—Sal. 62:8; 65:2; 1 Pet. 5:7.

  2. 15. Baibulo limatiphunzitsa mmene tingapempherere.​—Mat. 6:7-13; Luka 11:1-4.

  3. 16. Tizipemphera nthawi zonse.​—Mat. 7:7, 8; 1 Ates. 5:17.

 YESU

  1. 17. Yesu anali mphunzitsi waluso kwambiri ndipo malangizo ake ndi othandiza nthawi zonse.​—Mat. 6:14, 15, 34; 7:12.

  2. 18. Yesu ananeneratu za zinthu zomwe tikuziona masiku ano.​—Mat. 24:3, 7, 8, 14; Luka 21:10, 11.

  3. 19. Yesu ndi Mwana wa Mulungu.​—Mat. 16:16; Yoh. 3:16; 1 Yoh. 4:15.

  4. 20. Yesu si Mulungu Wamphamvuyonse.​—Yoh. 14:28; 1 Akor. 11:3.

 UFUMU WA MULUNGU

  1. 21. Ufumu wa Mulungu ndi boma lenileni lomwe lili kumwamba.​—Dan. 2:44; 7:13, 14; Mat. 6:9, 10; Chiv. 11:15.

  2. 22. Ufumu wa Mulungu udzalowa m’malo mwa maboma a anthu.​—Sal. 2:7-9; Dan. 2:44.

  3. 23. Ndi Ufumu wa Mulungu wokha womwe udzathetse mavuto omwe anthu akukumana nawo.​—Sal. 37:10, 11; 46:9; Yes. 65:21-23.

 MAVUTO

  1. 24. Mulungu si amene amachititsa kuti tizivutika.​—Deut. 32:4; Yak. 1:13.

  2. 25. Satana ndi amene akulamulira dzikoli.​—Luka 4:5, 6; 1 Yoh. 5:19.

  3. 26. Mulungu zimam’khudza mukamavutika.​—Sal. 34:17-19; Yes. 41:10, 13.

  4. 27. Posachedwapa Mulungu adzathetsa mavuto onse. ​—Yes. 65:17; Chiv. 21:3, 4.

 IMFA

  1. 28. Akufa sadziwa chilichonse ndipo sakuzunzika.​—Mlal. 9:5; Yoh. 11:11-14.

  2. 29. Akufa sangatithandize kapenanso kutivulaza.​—Sal. 146:4; Mlal. 9:6, 10.

  3. 30. Okondedwa athu omwe anamwalira adzaukitsidwa.​—Yobu 14:13-15; Yoh. 5:28, 29; Mac. 24:15.

  4. 31. “Imfa sidzakhalaponso.”​—Chiv. 21:3, 4; Yes. 25:8.

 CHIPEMBEDZO

  1. 32. Si zipembedzo zonse zomwe zimasangalatsa Mulungu.​—Yer. 7:11; Mat. 7:13, 14, 21-23.

  2. 33. Mulungu amadana ndi zachinyengo.​—Yes. 29:13; Mika 3:11; Maliko 7:6-8.

  3. 34. Anthu a m’chipembedzo choona amadziwika ndi chikondi.​—Mika 4:3; Yoh. 13:34, 35.