Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

ZAKUMAPETO C

Motsogozela Phunzilo la Baibo Poseŵenzetsa Buku la Kondwelani na Moyo Kwamuyaya!

Motsogozela Phunzilo la Baibo Poseŵenzetsa Buku la Kondwelani na Moyo Kwamuyaya!

Panaloŵa mapemphelo ankhani-nkhani komanso kufufuza kosaneneka pokonza buku la Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! Kuti bukulo likhale la phindu kwenikweni potsogoza maphunzilo a Baibo, gwilitsani nchito ndondomeko ya kaphunzitsidwe imene tafotokoza pansipa.

Isanafike nthawi ya phunzilo

  1. 1. Konzekelani bwino lomwe. Pamene mukutelo, ganizilani zosoŵa zake, umoyo wake, komanso zimene amakhulupilila. Yesani kuganizila mfundo zimene angafunikile thandizo kuti azimvetsetse kapena kuti azizigwilitsa nchito. Ganizilani mmene nkhani zili pa mbali yakuti “Fufuzani” zingam’thandizile wophunzila wanu, ndipo konzekelani kuzigwilitsa nchito pa phunzilo, ngati kungakhale kofunikila.

Kutsogoza phunzilo

  1. 2. Ngati wophunzila wanu akuvomeleza, yambani na kumaliza na pemphelo.

  2. 3. Pewani kufotokoza zambili. Makambilano anu atsamile kwambili pa mfundo zili m’bukulo, ndipo lolani wophunzila wanu azikambapo maganizo ake momasuka.

  3. 4. Poyamba cigawo catsopano, ŵelengani mbali yakuti nkhani yake na kuchulako mitu ina imene mudzaphunzila m’cigawo cimeneco.

  4. 5. Pomaliza cigawo, seŵenzetsani mafunso obweleza cigawo pothandiza wophunzila kukumbukila mfundo zimene waphunzila.

  5. 6. Pophunzila mutu uliwonse na wophunzila wanu, citani izi:

    1. Ŵelengani ndime.

    2. Ŵelengani malemba onse akuti “Ŵelengani.”

    3. Ŵelengani malemba osagwila mawu pakafunikila kutelo.

    4. Tambitsani mavidiyo onse olembedwa kuti “Tambani Vidiyo” (ngati muli nawo).

    5. Funsani wophunzila wanu mafunso onse.

    6. Pemphani wophunzila wanu kuyang’ana pa zithunzi zili m’cigawo cakuti “Kumbani Mozamilapo,” ndipo m’pempheni akambepo.

    7. Seŵenzetsani danga lakuti “Colinga” pom’thandiza kuona mmene akupitila patsogolo. Mwa citsanzo cimeneci, mulimbikitseni kumadziikila zolinga zina.

    8. Funsani wophunzila wanu ngati pali nkhani kapena vidiyo imene anaikonda kwambili pamene anali kukonzekela, ya pa cigawo cakuti “Fufuzani.”

    9. Yesetsani kutsiliza phunzilo lonse paulendo umodzi.

Mukabwelako ku phunzilo

  1. 7. Muganizilenibe wophunzila wanu. M’pempheleleni kwa Yehova kuti am’dalitse pamene akupita patsogolo, kutinso akuthandizeni kudziŵa mom’thandizila.