Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndapanga Mzimu Woyera Kukhala Mthandizi Wanga?

Kodi Ndapanga Mzimu Woyera Kukhala Mthandizi Wanga?

Kodi Ndapanga Mzimu Woyera Kukhala Mthandizi Wanga?

KUWONJEZERA pa anthu wamba, akatswiri a zaumulungu ali ndi maganizo osiyanasiyana pankhani ya mmene mzimu woyera wa Mulungu uliri. Komatu palibe chifukwa chokayikirira. Baibulo limaufotokoza momveka bwino mzimu woyera. M’malo mokhala munthu, ngati momwe ena amanenera, mzimu woyera ndi mphamvu yogwira ntchito imene Mulungu amagwiritsa ntchito pochita chifuno chake.​—Salmo 104:30; Machitidwe 2:33; 4:31; 2 Petro 1:21.

Ndiye chifukwa chakuti mzimu woyera ndi wogwirizana kwambiri ndi kukwaniritsidwa kwa zolinga za Yehova, tiyenera kugwirizana nawo m’moyo wathu. Tiyenera kufuna kuti uzitithandiza.

N’chifukwa Chiyani Mthandizi Akufunika?

Pokonzekera kuchoka kwake padziko lapansi, Yesu anatsimikizira ophunzira ake kuti: “Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu Nkhoswe ina, kuti akhale ndi inu ku nthaŵi yonse.” Komanso anati: “Koma ndinena Ine choonadi ndi inu; kuyenera kwa inu kuti ndichoke Ine; pakuti ngati sindichoka, Nkhosweyo sadzadza kwa inu; koma ngati ndipita ndidzam’tuma Iye kwa inu.”​—Yohane 14:16, 17; 16:7.

Yesu anapatsa ophunzira ake ntchito yofunikira kwambiri mwa kuwalangiza kuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyu 28:19, 20) Zimenezi zinadzakhala zovuta chifukwa zinayenera kudzachitika pa nthaŵi imene akuletsedwa.​—Mateyu 10:22, 23.

Kutsutsidwa ndi anthu akunja kunkachitika pamenenso mu mpingo munali kusagwirizana. Paulo analembera Akristu a ku Roma cha m’ma 56 C.E., kuti: “Ndipo ndikudandaulirani, abale, yang’anirani iwo akuchita zopatutsana ndi zopunthwitsa, kosalingana ndi chiphunzitsocho munachiphunzira inu; ndipo potolokani pa iwo.” (Aroma 16:17, 18) Zinthu zinafika poipa kwambiri pamene atumwi onse anafa. Paulo anachenjeza kuti: “Ndidziŵa ine kuti, nditachoka ine, adzaloŵa mimbulu yosautsa, yosalekerera gululo; ndipo mwa inu nokha adzauka anthu, olankhula zokhotakhota, kupatutsa ophunzira awatsate.”​—Machitidwe 20:29, 30.

Chithandizo cha Mulungu chinafunika kuti apambane zolepheretsa zimenezi. Anachita zimenezo kudzera mwa Yesu. Ataukitsidwa kale, pa tsiku la Pentekoste mu 33 C.E., otsatira ake okwana 120 “anadzazidwa onse ndi mzimu woyera.”​—Machitidwe 1:15; 2:4.

Ophunzirawo anazindikira kuti mzimu woyera umene unatsanulidwa pa msonkhano umenewu unali chithandizo chimene Yesu anali atalonjeza. Mosakayika tsopano anamvetsa bwino chizindikiro chimene Yesu anapereka: ‘Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzam’tuma m’dzina langa, Iyeyo adzaphunzitsa inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu.’ (Yohane 14:26) Anautchanso kuti ‘nkhoswe, mzimu wa choonadi.’​—Yohane 15:26.

Kodi Mzimu Ndi Mthandizi Motani?

Mzimu unayenera kudzathandiza m’njira zosiyanasiyana. Choyamba, Yesu analonjeza kuti udzakumbutsa ophunzira ake zinthu zimene anali atawauza. Ponena zimenezi sanangotanthauza kuwathandiza kukumbukira mawu okha. Mzimuwo unali kudzawathandiza kumvetsa tanthauzo lenileni ndiponso kufunika kwa zimene anali atawaphunzitsa. (Yohane 16:12-14) Mwachidule, mzimu unali kudzathandiza ophunzira ake kumvetsa bwino choonadi. Pambuyo pake mtumwi Paulo analemba kuti: “Kwa ife Mulungu anationetsera izi mwa Mzimu; pakuti Mzimu asanthula zonse, zakuya za Mulungu zomwe.” (1 Akorinto 2:10) Kuti otsatira odzozedwa a Yesu agaŵire chidziŵitso cholongosoka kwa ena, chidziŵitso chawocho chinafunikira kuti chikhale chamaziko abwino.

Chachiŵiri, Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kupemphera ndi kutinso azitero kaŵirikaŵiri. Ngati zikanachitika nthaŵi zina kuti sakudziŵa zoti apempherere, mzimu ukanaloŵererapo kapena kuwathandiza. “Ndipo momwemonso mzimu [u]thandiza kufooka kwathu; pakuti chimene tizipempha monga chiyenera, sitidziŵa; koma mzimu mwini [u]tipempherera ndi zobuula zosatheka kuneneka.”​—Aroma 8:26.

Chachitatu, mzimu unali kudzathandiza ophunzira a Yesu poteteza choonadi poyera. Anawachenjeza kuti: “Adzakuperekani inu kwa akulu a mlandu, nadzakukwapulani inu m’masunagoge mwawo; ndiponso adzamuka nanu kwa akazembe ndi mafumu chifukwa cha ine, kukhala mboni ya kwa iwo, ndi kwa anthu akunja. Koma pamene paliponse angakuperekeni inu, musamadera nkhaŵa mudzalankhule bwanji kapena mudzanene chiyani; pakuti chimene mudzachilankhula, chidzapatsidwa kwa inu nthaŵi yomweyo; pakuti wolankhula si ndinu, koma mzimu wa Atate wanu akulankhula mwa inu.”​—Mateyu 10:17-20.

Mzimu woyera ukanathandizanso podziŵikitsa mpingo wachikristu ndi kupangitsa anthu ake kusankha zinthu zawo mwanzeru. Tiyeni tikambirane mozama zinthu ziŵirizi zokhudza nkhani imeneyi komanso tione mmene zilili zofunika kwa ifeyo lerolino.

Kukhala Monga Chizindikiro

Kwa zaka mazana ambiri Ayuda ankalamulidwa ndi Chilamulo cha Mose monga anthu osankhidwa ndi Mulungu. Chifukwa chakuti anakana Yesu kuti akhale Mesiya, iye ananeneratu kuti posapita nthaŵi iwonso adzakanidwa. Iye anati: “Kodi simunaŵerenga konse m’malembo, mwala umene anaukana omanga nyumba womwewu unakhala mutu wa pangodya. Ichi chinachokera kwa Ambuye, ndipo chili chozizwitsa m’maso mwathu? Chifukwa chake ndinena kwa inu, Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu, nudzapatsidwa kwa anthu akupatsa zipatso zake.” (Mateyu 21:42, 43) Mpingo wachikristu utapangidwa pa Pentekoste wa mu 33 C.E., otsatira Kristu anakhala “anthu akupatsa zipatso zake.” Kuyambira pamenepo mpaka m’tsogolo, mpingo umenewu unakhala njira ya Mulungu yolankhulira. Kuti athandize anthu kuzindikira kusintha kwa kuyanjidwa ndi Mulungu kumeneku, Mulungu anapereka chizindikiro chooneka bwino.

Pa Pentekoste mzimu woyera unatheketsa ophunzira kulankhula m’zinenero zimene anali asanaphunzirepo, kuchititsa oona kudabwa ndi kufunsa kuti: “Nanga ife timva bwanji, yense m’chilankhulidwe chathu chimene tinabadwa nacho?” (Machitidwe 2:7, 8) Mphamvu zotheketsa kulankhula m’zinenero zosadziŵika, pamodzi ndi “zozizwa ndi zizindikiro zambiri zinachitika ndi atumwi,” zinapangitsa anthu okwana zikwi zitatu kuzindikira kuti mzimu wa Mulungu unalidi kugwira ntchito.​—Machitidwe 2:41, 43.

Komanso, posonyeza “chipatso cha mzimu”, chomwe ndi chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso, ophunzira a Kristu anadziŵika monga atumiki a Mulungu. (Agalatiya 5:22, 23) Kwenikweni, chikondi, chinasonyeza mwapadera mpingo woona wachikristu. Yesu anali ataneneratu kuti: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.”​—Yohane 13:34, 35.

Anthu a mu mpingo wachikristu woyambirira analola kutsogoleredwa ndi mzimu woyera wa Mulungu ndipo anagwiritsa ntchito bwino thandizo limene mzimu unapereka. Akristu lerolino amazindikira kuti Mulungu tsopano sakuukitsanso akufa ndipo sakuchitanso zozizwitsa ngati m’zaka za zana loyamba, koma amalola chipatso cha mzimu wa Mulungu kuwazindikiritsa monga ophunzira enieni a Yesu Kristu.​—1 Akorinto 13:8.

Mthandizi Posankha Zinthu Zochita

Baibulo n’chipatso cha mzimu woyera. Chotero, pamene tikulola kuti Baibulo litiphunzitse, zili ngati kuti mzimu woyera ukutilangiza. (2 Timoteo 3:16, 17) Lingatithandize kusankha zinthu mwanzeru. Koma kodi timalilola?

Bwanji za ntchito imene timasankha? Mzimu woyera udzatithandiza kuona ntchito imene tikufuna mmene Yehova amaionera. Ntchito yathu iyenera kugwirizana ndi mfundo zachikhalidwe za Baibulo, ndipo makamaka iyenera kukhala yotitheketsa kukwaniritsa zolinga zaulamuliro waumulungu. Malipiro kapena kutchuka komanso ulemelero wobwera chifukwa cha ntchito inayake ndi zosafunikira kwenikweni. Chofunika kwambiri n’chakuti ntchitoyo izitipatsa zinthu zofunika m’moyo ndiponso nthaŵi yokwanira komanso mipata kuti tikwaniritse maudindo athu achikristu.

Chikhumbo chofuna kusangalala ndi moyo n’chachibadwa ndiponso n’choyenera. (Mlaliki 2:24; 11:9) Choncho Mkristu wolingalira bwino angasangalale n’cholinga choti apumule. Koma ayenera kusankha zosangalatsa zimene zimasonyeza chipatso cha mzimu, osati zimene zimasonyeza “ntchito za thupi.” Paulo anati: “Ndipo ntchito za thupi zionekera, ndizo dama, chodetsa, kukhumba zonyansa, kupembedza mafano, nyanga, madano, ndewu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magaŵano, mipatuko, njiru, kuledzera, mchezo, ndi zina zotere.” Tiyeneranso kupeŵa kukhala “odzikuza, outsana, akuchitirana njiru.”​—Agalatiya 5:16-26.

N’chimodzimodzinso tikamasankha anzathu. N’kwanzeru kusankha anzathu mogwirizana ndi mkhalidwe wawo wauzimu, osati kungotsata kaonekedwe kapena zinthu zimene alinazo. N’zachidziŵikire kuti Davide anali bwenzi la Mulungu, chifukwa Mulungu anamutcha kuti “munthu wa pamtima panga.” (Machitidwe 13:22) Mosayang’ana maonekedwe akunja, Mulungu anasankha Davide kuti akhale mfumu ya Israyeli, mogwirizana ndi mfundo yakuti: “Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang’ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang’ana mumtima.”​—1 Samueli 16:7.

Maunansi zikwizikwi atha chifukwa anayambika mwa kungoona maonekedwe akunja kapena zinthu zakuthupi. Maubwenzi oyambika chifukwa cha chuma akhoza kutha mosayembekezeka. (Miyambo 14:20) Mawu a Mulungu owuziridwa ndi mzimu amatilangiza kuti pamene tikusankha anzathu, tiyenera kusankha anzathu amene angatithandize kutumikira Yehova. Amatiuzanso kuti tiziganizira kwambiri zakupatsa osati kulandira chifukwa kupatsa kumabweretsa chimwemwe chachikulu. (Machitidwe 20:35) Nthaŵi ndi chikondi ndi zina mwa zinthu zamtengo wapatali kwambiri zomwe tingapatseko anzathu.

Kwa Mkristu amene akufuna wokwatirana naye, Baibulo limapereka malangizo otsogozedwa ndi mzimu. Tinganene kuti limati: ‘Usaone nkhope ndi maonekedwe. Ona mapazi.’ Mapazi? Inde, m’lingaliro lakuti: Kodi akugwiritsidwa ntchito ya Yehova yolalikira uthenga wabwino, ndipo kodi tingati n’ngokongola, pamaso pake? Kodi mapaziwo avala uthenga wa choonadi ndi uthenga wabwino wa mtendere? Timaŵerenga kuti: “Ha, akongolatu pamapiri mapazi a iye amene adza ndi uthenga wabwino, amene abukitsa mtendere, amene adza ndi uthenga wabwino wa zinthu zabwino, amene abukitsa chipulumutso; amene ati kwa Ziyoni, Mulungu wako ndi mfumu.”​—Yesaya 52:7; Aefeso 6:15.

Kuti tikhale mu “nthaŵi zoŵaŵitsa” zino, ngati momwe tikukhaliramu, tikufunikira thandizo pochita chifuno cha Mulungu. (2 Timoteo 3:1) Mthandizi, mzimu woyera wa Mulungu, unapereka chithandizo champhamvu pa ntchito ya Akristu mu zaka za zana loyamba, komanso unakhala mthandizi wawo. Kuphunzira Mawu a Mulungu mokhazikika, omwe ali okonzedwa ndi mzimu woyera, ndiyo njira yoyamba imene ifenso tingapangitsire mzimu woyera kukhala mthandizi wathu. Kodi tatero?

[Chithunzi chachikulu patsamba 23]