Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuthandiza Achinyamata ndi Malangizo Apanthaŵi Yake

Kuthandiza Achinyamata ndi Malangizo Apanthaŵi Yake

Imani Amphumphu Ndi Otsimikiza Kotheratu

Kuthandiza Achinyamata ndi Malangizo Apanthaŵi Yake

EPAFRA anali Mkristu wa m’zaka za zana loyamba yemwe anapita ku Roma. Komabe pachifukwa chabwino, iye anali kuganizirabe za mzinda wa Kolose ku Asia Minor. Anali atalalikira uthenga wabwino mumzindawo ndipo mosakayikira anathandiza Akolose ena kukhala ophunzira a Yesu Kristu. (Akolose 1:7) Epafra anali kudera nkhaŵa kwambiri okhulupirira anzake a ku Kolose monga momwe kalata ya mtumwi Paulo kuchokera ku Roma ikusonyezera kuti: “Epafra . . . akukupatsani moni, wakulimbika chifukwa cha inu m’mapemphero ake masiku onse, kuti mukaime amphumphu ndi otsimikiza kotheratu za chifuniro chonse cha Mulungu.”​—Akolose 4:​12, NW.

Mofananamo, atate ndi amayi achikristu lerolino amapempherera umoyo wauzimu wa ana awo mwakhama. Makolo ameneŵa amayesetsa kukhomereza kukonda Mulungu m’mitima mwa ana awo kuti adzakhale olimba m’chikhulupiriro.

Achinyamata ambiri achikristu apempha thandizo lothetsera mavuto omwe amakhala nawo kusukulu ndi kwina. Mtsikana wina wa zaka 15 anati: “Mavuto athu akukulirakulira ndipo moyo ndi woopsa kwambiri. Tithandizeni! Kodi zopempha za achinyamata otereŵa ndiponso mapemphero a makolo oopa Mulungu ayankhidwa? Inde! Malangizo a m’Baibulo aperekedwa kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45) Nkhani ino ikutchula ena mwa mabuku amene athandiza achinyamata zikwi mazana ambiri “kuima amphumphu ndi otsimikiza kotheratu.” Tiyeni tione oŵerengeka chabe mwa mabuku ameneŵa.

“Taonani . . . Mboni Zatsopano 15,000!”

Mu August 1941, anthu okwana 115,000 anasonkhana ku St. Louis, Missouri, U.S.A., kuchita msonkhano waukulu kwambiri wa Mboni za Yehova womwe unali usanachitikepo m’mbuyomo. Tsiku lomaliza​—“Tsiku la Ana”​—ana okwana 15,000 omwe anakhala kufupi ndi pulatifomu anamvetsera mwachidwi nkhani yakuti “Ana a Mfumu” yomwe Joseph F. Rutherford ankakamba. Ali pafupi kumaliza nkhaniyo, Rutherford yemwe anali ndi zaka 71, anauza anawo ndi mawu autate amvekere:

“Ana nonsenu . . . amene mwavomereza . . . kumvera Mulungu ndi Mfumu yake, imirirani chonde.” Ana onse anaimirira nthaŵi imodzi. Kenako Mbale Rutherford anafuula kuti: “Taonani mboni zatsopano za Ufumu zopitirira 15,000!” Ndiyetu kunali kuwomba m’manja. Iye anawonjezera amvekere: “Inu nonse amene mudzachita zomwe mungathe kuuza ena za ufumu wa Mulungu . . . , nenani kuti, Inde!” Anawo anavomera mokweza amvekere, “Inde!” Atatero, anatulutsa buku latsopano lakuti Children (Ana). Ndipo posonyeza kuti alilandira ndi manja aŵiri omvetsera anawombera m’manja kwakanthaŵi ndithu.

Itatha nkhani yogwira mtima imeneyi, achinyamata anapanga mzere wautali kupita ku pulatifomu kumene Mbale Rutherford anali kuwapatsa mphatso ya buku latsopanolo. Zochitikazo zinasangalatsa omvetsera kwambiri mpaka kukhetsa misozi. Munthu wina yemwe anali pomwepo anasimba kuti: “Okhawo osayamikira ndiwo sanaonetse kukhudzidwa kwawo pamene ana anali kusonyeza chidaliro ndi chikhulupiriro mwa Mulungu wawo, Yehova.”

Pamsokhano wosaiŵalikawo, achinyamata 1,300 anasonyeza kudzipatulira kwawo kwa Yehova mwa kubatizidwa. Ambiri mwa iwo akhalabe olimba m’chikhulupiriro mpaka lero. Amathandiza mipingo ya m’dera lawo, kugwira ntchito yodzifunira pa Beteli kapena kutumikira monga amishonale m’mayiko ena. Inde, “Tsiku la Ana” ndiponso buku lakuti Children n’zosaiŵalika kwa achinyamata ambiri.

“Mabukuŵa Akuoneka Kuti Amabwera Panthaŵi Yake”

M’ma 1970, Mboni za Yehova zinafalitsa mabuku enanso atatu omwe anali ogwira mtima kwa achinyamata zikwi mazana ambiri. Mabukuŵa ndi: Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkulu’yo, Your Youth​—Getting the Best out of It, ndiponso Buku Langa la Nkhani za Baibulo. Mu 1982, nkhani zakuti Achinyamata Akufunsa Kuti . . . ”zinayamba kutuluka m’magazini a Galamukani! Achinyamata ndi achikulire omwe akuziyamikira kwambiri nkhani zimenezi. “Usiku uliwonse ndimathokoza Mulungu chifukwa chakuti nkhanizi zikufalitsidwa,” anatero wachinyamata wina wa zaka 14. Mtsikana wina wa zaka 13 anati: “Nkhanizi ndimazikonda kwambiri ndipo zikuoneka kuti zimabwera panthaŵi yake.” Makolo ndiponso akulu oikidwa achikristu akuvomereza kuti nkhanizi zimafikadi panthaŵi yake ndipo n’zopindulitsa kwambiri.

Pomwe chimafika chaka cha 1989, n’kuti nkhani zakuti “Achinyamata Akufunsa Kuti . . . ”zokwana 200 zitatuluka m’magazini a Galamukani! Pamsonkhano Wachigawo wa chaka chimenecho wakuti “Kudzipereka Kwaumulungu,” buku lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa​—Mayankho Amene Amathandiza linatulutsidwa. Kodi bukuli lathandizadi achinyamata kukhalabe olimba m’chikhulupiriro? Anyamata atatu analemba kuti: “Bukuli latithandiza kwambiri kumvetsa mavuto athu ndiponso kudziŵa zoyenera kuchita kuti tiwagonjetse. Zikomo kwambiri chifukwa cha chidwi chanu pa moyo wathu.” Oŵerenga ambiri achinyamata padziko lonse akuvomereza mawu ameneŵa.

“Inathetsa Njala Yathu”

Mu 1999, Mboni za Yehova zinatulutsa malangizo enanso apanthaŵi yake a achinyamata​—vidiyo yakuti, Young People Ask​—How Can I Make Real Friends? Anthu akuyamikira kwambiri vidiyo imeneyi. “Vidiyoyi inandikhudza kwambiri,” anatero mtsikana wina wa zaka 14. Mayi wina yemwe sali pabanja anati, “vidiyo imeneyi idzakhala mbali ya chakudya chathu chauzimu nthaŵi zonse.” Mtsikana wina wapabanja anati, “n’zosangalatsa kudziŵa kuti Bwenzi lathu lapamtima, Yehova, amakonda ndi kusamaladi achinyamata m’gulu lake lapadziko lonse.”

Kodi vidiyo imeneyi yakwaniritsa chiyani? Achinyamata akunena kuti: “Yandithandiza kusankha bwino ocheza nawo, kuwonjezera oyanjana nawo mumpingo ndiponso kupalana ubwenzi ndi Yehova. Yandithandiza kukhalabe olimba anzanga akamandikakamiza kuchita zosayenera. Yandichititsa kukhala wotsimikiza kotheratu kutumikira Yehova ndi mtima wonse.” Ndipo mwamuna wina ndi mkazi wake analemba kuti: “Tikuthokoza kuchokera pansi pa mtima chifukwa chotipatsa ‘chakudya chauzimu chimenechi.’ Chinathetsa njala yathu.”

Chifukwa chokhulupirika pantchito yomwe Mulungu anam’patsa, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wodzozedwayo, wapereka chakudya chauzimu chapanthaŵi yake kwa onse amene adzachilandira. Ndipotu n’zosangalatsa kwambiri kuona mmene malangizo a m’Malemba otereŵa akuthandizira achinyamata lerolino ‘kuima amphumphu ndi otsimikiza kotheratu za chifuniro chonse cha Mulungu’!