Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulambira Koona Kumagwirizanitsa Anthu

Kulambira Koona Kumagwirizanitsa Anthu

Kulambira Koona Kumagwirizanitsa Anthu

NGAKHALE kuti zipembedzo nthaŵi zambiri zimagaŵanitsa anthu, kulambira Mulungu woona yekha kuli ndi mphamvu yogwirizanitsa anthu. Nthaŵi imene Israyeli unali mtundu umene Mulungu anausankha, Akunja oona mtima ambiri anakopeka ndi kulambira koona. Mwachitsanzo, Rute anasiya milungu yakwawo ku Moabu ndipo anati kwa Naomi: “Anthu a kwanu ndiwo anthu a kwa inenso, ndi Mulungu wanu ndiye Mulungu wanga.” (Rute 1:16) Podzafika mu zaka za zana loyamba C.E., Akunja ambiri an’kalambira Mulungu woona. (Machitidwe 13:48; 17:4) Ndiyeno atumwi a Yesu atayamba kulalikira uthenga wabwino m’madera akutali, anthu enanso oona mtima anagwirizana pa kulambira Mulungu woona. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Munatembenukira kwa Mulungu posiyana nawo mafano, kutumikira Mulungu weniweni wamoyo.” (1 Atesalonika 1:9) Kodi masiku ano kulambira Mulungu woona kuli ndi mphamvu yogwirizanitsa anthu yoteroyo?

Anthu osakhulupirira amalimbikira kutsutsa zoti pali “olambira oona” kapena “Mulungu woona.” Angaone chonchi chifukwa sadziŵa njira iliyonse yomwe angaphunzirire choonadi. Koma anthu ofuna choonadi a m’zipembedzo zambiri aona kuti kulambira si nkhani ya makondamakonda. Yehova Mulungu, amene analenga zinthu zonse ndiye woyenera kumulambira. (Chivumbulutso 4:11) Ameneyu ndi Mulungu woona, ndipo ndi amene ayenera kusankha njira yomulambirira.

Yehova watiuza zimene amafuna kudzera m’Mawu ake, Baibulo. Lerolino, pafupifupi aliyense padziko lapansi ali ndi Baibulo lonse kapena mbali yake chabe. Ndiponso, Mwana wa Mulungu anati: ‘Ngati mukhala m’mawu anga, mudzazindikira choonadi.’ (Yohane 8:31, 32) Choncho, tingazindikire choonadi. Ndipo anthu oona mtima ambiri amene anali m’zipembedzo zosiyana akuphunzira molimba mtima ndiponso mosangalala choonadi chimenechi ndipo akugwirizana pa kulambira koona.​—Mateyu 28:19, 20; Chivumbulutso 7:9, 10.

Kugwirizana Padziko Lonse Masiku Ano!

Ulosi wapadera m’buku la m’Baibulo la Zefaniya umanena za kusonkhana pamodzi kwa anthu okulira m’zipembedzo zosiyanasiyana. Umati: ‘Pamenepo [Yehova Mulungu] adzapatsa mitundu ya anthu mlomo woyera [“chinenero choyera,” NW], kuti onseŵa aitanire pa dzina la Yehova kum’tumikira ndi mtima umodzi.’ (Zefaniya 3:9) Chimenechitu ndi chithunzi chabwino kwambiri cha anthu osintha amene akutumikira Mulungu mogwirizana.

Kodi izi zinali kudzachitika liti? Zefaniya 3:8 amati: “Mundilindire, ati Yehova, kufikira tsiku loukira Ine zofunkha; pakuti ndatsimikiza mtima Ine kusonkhanitsa amitundu, kuti ndimemeze maufumu kuwatsanulira kulunda kwanga, ndilo mkwiyo wanga wonse waukali; pakuti dziko lonse lapansi lidzathedwa ndi moto wa nsanje yanga.” Inde, m’nthaŵi imene Yehova akusonkhanitsa mitundu asanawatsanulire mkwiyo wake waukali, akusintha anthu ofatsa a padziko lapansi kuti alankhule chinenero choyera. Nthaŵi yake ndi ino, popeza ntchito yosonkhanitsira mitundu yonse kunkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse pa Armagedo ili m’kati.​—Chivumbulutso 16:14, 16.

Yehova wapatsa anthu ake chinenero choyera kuti awagwirizanitse. Chinenero chatsopano chimenechi chimaphatikizapo kumvetsetsa bwino choonadi cha m’Baibulo chonena za Mulungu ndi zomwe amafuna. Kulankhula chinenero choyera kumaphatikizaponso kukhulupirira choonadi, kuphunzitsa ena choonadi, ndiponso kutsatira malamulo a Mulungu ndi mfundo zake za chikhalidwe. Kumafunanso kuti tisaloŵe m’ndale zimene zimagawanitsa anthu ndiponso tichotseretu malingaliro odzikonda m’mitima yathu, monga kusankhana mitundu ndi mafuko komwe n’kofala m’dziko lino. (Yohane 17:14; Machitidwe 10:34, 35) Anthu onse oona mtima amene amakonda choonadi angaphunzire chinenero chimenechi. Onani mmene anthu asanu amene tinawatchula m’nkhani yoyamba ija omwe anali m’zipembedzo zosiyana, tsopano alili ogwirizana pa kulambira Mulungu woona yekha, Yehova.

Agwirizana pa Kulambira Koona

Fidelia, m’Katolika wodzipereka uja atagulira mwana wake wamkazi Baibulo la kusukulu, anam’funsa wansembe wake kuti afotokoze kuchokera m’Baibulolo chimene chinali kuchitikira ana ake asanu omwe anamwalira aja. Iye akuti: “Si mmene ndinakhumudwira!” Choncho Mboni za Yehova zitam’fikira, anawafunsa funso lofananalo. Ataŵerenga kuchokera m’Baibulo lake zoona zenizeni za mmene akufa alili, anazindikira kuti tchalitchi chake chinkamunamiza. Anaphunzira kuti akufa sadziŵa kanthu, chotero ana ake sakuzunzika ku Limbo, kapena kwina kwake. (Salmo 146:4; Mlaliki 9:5) Fidelia anataya mafano onse a chipembedzo chake, ndipo anachoka m’chipembedzocho, n’kuyamba kuphunzira Baibulo. (1 Yohane 5:21) Zaka khumi zapitazi, wakhala akuphunzitsa anthu ena choonadi cha m’Malemba.

Tara wa ku Kathmandu anasamukira m’dziko limene akachisi a Chihindu ndi ochepa. Choncho anayamba kupita kutchalitchi cha Methodist pokhulupirira kuti akakwaniritsa zosoŵa zake zauzimu. Koma sanapeze yankho la funso lake lonena za kuvutika kwa anthu. Ndiyeno Mboni za Yehova zinam’fikira ndi kum’pempha kuphunzira naye Baibulo. Tara akuti: “Tsopano ndinazindikira kuti Mulungu wachikondi sindiye amachititsa mavuto m’dziko . . . Chiyembekezo cha dziko latsopano lamtendere ndi bata chinandisangalatsa kwambiri.” (Chivumbulutso 21:3, 4) Tara anataya mafano ake a Chihindu, anasiya kutsatira miyambo ya chipembedzo ya m’dziko lakwawo, ndipo monga Mboni ya Yehova anapeza chimwemwe chenicheni pothandiza kukwaniritsa zosoŵa zauzimu za anthu ena.

Panya, Mbuda uja, anali wolosera za m’tsogolo pamene Mboni za Yehova zinam’fikira ku Bangkok, choncho anachita chidwi ndi maulosi a m’Baibulo. Panya anati: “Nditaphunzira chifukwa chake zinthu panopo sizili monga momwe Mlengi anafunira ndiponso zimene wakonza kuti achotse zoipa zimene anthu amene amam’kana ndi kukananso ulamuliro wake abweretsa, zinali ngati kuti andichotsa khungu m’maso. Uthenga wa m’Baibulo wonse unali wogwirizana. Ndinayamba kukonda Yehova monga munthu, ndipo zimenezi zinandipangitsa kuchita zabwino. Ndinali wokonzeka kuthandiza ena kusiyanitsa nzeru za anthu ndi za Mulungu. Nzeru yeniyeni yasinthadi moyo wanga.”

M’kupita kwa nthaŵi Virgil anayamba kukayikira kwambiri zikhulupiriro za chipembedzo chake. M’malo mopempha Mulungu kuti athandize anthu akuda ndi kuthandizanso gulu limene ankati ndi lodzikonda limene linkadana ndi azungu, anapempha kuti apeze choonadi china chilichonse, kulikonse komwe chinali. Virgil akuti: “Tsiku lina ndinapemphera kwa Mulungu kuchokera pansi pamtima. Nditadzuka m’maŵa mwake, ndinapeza Nsanja ya Olonda m’nyumba. . . . Iyenera kuti wina analowetsera pansi pa chitseko.” Posakhalitsa anali kuphunzira kwambiri Baibulo ndi Mboni za Yehova. Akutinso: “Aka n’koyamba m’moyo wanga, kupeza yankho lokhutiritsa. . . Chiyembekezo chinayamba kuŵala pang’onopang’ono m’kati mwanga.” Posapita nthaŵi, Virgil anagwirizana ndi anthu amene amauza anthu ena chiyembekezo choona chokha chimene chili m’Mawu a Mulungu, m’Baibulo.

Charo wa ku Latin America anachita chidwi ndi zimene Mboni ina dzina lake Gladys inachita. Mboniyo itaona kuti Charo ankavutika ndi ana ake ang’onoang’ono, inayamba kumuthandiza mwa kum’pitira ku msika. M’kupita kwa nthaŵi, Charo anavomera pempho la Gladys loti aziphunzira naye Baibulo panyumba kwaulere. Charo anadabwa kuphunzira m’Baibulo lake kuti anthu onse abwino sapita kumwamba koma kuti Yehova adzadalitsanso anthu padziko lapansi mwa kuwapatsa moyo wosatha. (Salmo 37:11, 29) Charo wakhala akuuza ena chiyembekezo chimenechi kwa zaka 15 zapitazi.

Tangoganizirani mmene zingakhalire dziko lonse litadzala ndi anthu oona mtima okhaokha ogwirizana pa kulambira Yehova, Mulungu woona yekha. Izi sizongoyerekezera. Ndi zimene Yehova walonjeza. Mwa mneneri wake Zefaniya, Mulungu anati: “Ndidzasiya pakati pako anthu ozunzika ndi osauka [“odzichepetsa ndi ofatsa,” NW], ndipo iwo adzakhulupirira dzina la Yehova. . . . Sadzachita chosalungama, kapena kunena mabodza; ndi m’kamwa mwawo simudzapezeka lilime lonyenga; . . . palibe wakuwawopsa.” (Zefaniya 3:12, 13) Ngati lonjezo limeneli lakugwirani mtima, mverani langizo la m’Baibulo ili: “Funani Yehova, ofatsa inu nonse a m’dziko, amene munachita chiweruzo chake; funani chilungamo, funani chifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.”​—Zefaniya 2:3.