Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Misonkhano Yaikulu ndi Umboni Wosangalatsa wa Ubale Wathu

Misonkhano Yaikulu ndi Umboni Wosangalatsa wa Ubale Wathu

Imani Amphumphu ndi Otsimikiza Kotheratu

Misonkhano Yaikulu ndi Umboni Wosangalatsa wa Ubale Wathu

JOSEPH F. Rutherford atatha pafupifupi chaka chimodzi m’ndende chifukwa cha mlandu wom’semera, anatumikira mosangalala monga wolandira alendo. Panthaŵiyi n’kuti ali ndi zaka 50 ndipo sanali kupeza bwino kwenikweni. Komabe ananyamula masutikesi ndiponso kuthandiza Akristu anzake kupita ku hotela m’zipinda zoti akagone. Anthu aŵiri amene anali nawo kundende​—Ophunzira Baibulo anzake​—anapereka zipinda kwaulere ku gulu lalikulu limene linkadikira kuti aliuze kumene likagone. Kunali pilingupilingu pochita zimenezi mpaka kupitirira pakati pausiku. Anthu onse anali osangalala. Kodi inali nthaŵi ya chiyani?

Chinali chaka cha 1919, ndipo Ophunzira Baibulo (amene tsopano ndi Mboni za Yehova) anali atangochoka kumene munthaŵi ya chizunzo chopweteka kwambiri. Chotero pofuna kulimbikitsanso ubale wawo, anachita msonkhano ku Cedar Point, Ohio, U.S.A, kuyambira pa September 1 mpaka 8, 1919. Patsiku lomaliza la msonkhanowo, anthu achimwemwe 7,000 anamvetsera kwambiri pamene Mbale Rutherford ankalimbikitsa opezeka pamsonkhanowo kuti: “Ndinu akazembe a Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye, lengezani kwa anthu . . . ufumu waulemerero wa Ambuye wathu.”

Misonkhano yaikulu ya anthu a Yehova, inayamba m’nthaŵi ya Israyeli wakale. (Eksodo 23:14-17; Luka 2:41-43) Misonkhano imeneyi inali nthaŵi zosangalatsa, zothandiza anthu opezekapo kuganizira Mawu a Mulungu. Chimodzimodzi masiku ano. Misonkhano ya Mboni za Yehova imakhala yokhudza zinthu zauzimu. Kwa anthu oona mtima, misonkhano yosangalatsa imeneyi imapereka umboni weniweni wakuti Mboni n’zogwirizana chifukwa cha ubale wolimba wachikristu.

Amayesetsa Kupezekapo

Akristu amakono amazindikira kuti misonkhano yawo yaikulu ndi nthaŵi yotsitsimula mwauzimu ndiponso ya malangizo a m’Mawu a Mulungu. Amaona misonkhano yaikulu imeneyi monga njira yofunika yowathandizira ‘kuima amphumphu ndi otsimikiza kotheratu za chifuniro chonse cha Mulungu.’ (Akolose 4:12, NW) Choncho, Mboni zimathandiza ndi mtima wonse misonkhano imeneyi, ndipo zimayesetsa kwambiri kupezekapo.

Ena kuti apezeke pa misonkhano yaikulu imeneyi amafunika kukhala ndi chikhulupiriro ndiponso kugonjetsa zopinga zikuluzikulu. Mwachitsanzo, lingalirani za Mboni yachikulire ya ku Austria. Ngakhale kuti inali ndi matenda a shuga ndipo inkafunika kuti tsiku lililonse izibayitsa jakisoni wa mankhwala ochepetsa shuga m’thupi, inaonetsetsa kuti yapezeka masiku onse a msonkhano wachigawo m’dzikolo. Ku India, banja lina lalikulu la Mboni losauka kwambiri, linaona kuti kunali kovuta kwambiri kupezeka pamsonkhano wachigawo. Wina m’banjamo anathandiza. Iye anati: “Posafuna kujomba kumsonkhano, ndinagulitsa ndolo zanga za golide kuti tipeze ndalama zoyendera. Ndinafunikadi kutero, popeza mayanjano ndi zokumana nazo zakumeneko zinalimbitsa chikhulupiriro chathu.”

Ku Papua New Guinea, gulu la anthu osabatizidwa koma achidwi linafunitsitsa kukapezeka pamsonkhano wachigawo kulikulu la dzikolo. Anapita kwa munthu wina m’mudzi wawowo amene anali ndi galimoto ndipo anam’funsa kuti apereke ndalama zingati kuti akawatule kumsonkhano. Chifukwa chakuti iwo analibe ndalama zimene munthuyo anatchula, anagwirizana zogwira ntchito yokonza khichini kunyumba ya mwini galimotoyo. Chotero anapita kumsonkhano wachigawo ndi kupindula mwa kupezeka pamsonkhano wonse.

Kutalika kwa ulendo si vuto kwa Mboni za Yehova zofunitsitsa kupezeka pamisonkhano yaikulu. Mu 1978, mnyamata wa ku Poland anayenda mtunda wamakilomita 1,200 kuti akapezeke pamsonkhano wachigawo ku Lille, France. Iye anayenda panjinga mtunda umenewu kwa masiku asanu ndi limodzi. M’nthaŵi yotentha m’chaka cha 1997, Mboni zina, mwamuna ndi mkazi wake, a ku Mongolia anayenda ulendo wamakilomita 1,200 kuti akapezeke pamsonkhano wachikristu ku Irkutsk, Russia.

Kusonyeza Ubale Weniweni

Anthu a maganizo abwino amaona kugwirizana ndiponso ubale umene Mboni zimasonyeza pamisonkhano yawo yaikulu. Ambiri achita chidwi kuti sipakhala kusankhana mitundu pamsonkhanowo ndipo pamakhala chikondi chenicheni ngakhale kwa anthu oti n’koyamba kuonana.

Posachedwapa pamsonkhano wina wa mayiko ku Australia, munthu amene kwa mlungu umodzi anaonetsa malo anthu omwe anapita kumsonkhanowo, anafuna kuti azikhala nawobe kuti apitirize kucheza. Anachita chidwi ndi chikondi komanso kugwirizana kwawo ndipo anadabwa kuti zinatheka bwanji kukhala nawo bwinobwino, popeza ambiri anali anthu oti sanawaonepo. Itafika nthaŵi yoti azipita, anafuula kuti amumvetsere. Atawatchula kuti “abale ndi alongo,” anayamba kuwathokoza koma sanamalize, popeza anatsamwa chifukwa chokhudzidwa mtima ndipo anayamba kulira.

Mu 1997, ku Sri Lanka kunachitika msonkhano wachigawo woyamba m’zinenero zitatu mu sitediyamu yaikulu. Pulogalamu yonse inali kuchitika pa nthaŵi imodzimodzi mu Chingelezi, Chisinhalese, ndi Chitamil. M’dziko losankhana mitundu limeneli, kusonkhana pamodzi kwa magulu a zinenero zitatu sikunabisike. Wapolisi wina anafunsa mbale kuti: “Kodi akuyendetsa msonkhano umenewu ndi Asinhalese, Atamil, kapena Angelezi?” Mbaleyo anayankha kuti: “Si gulu limodzi limene likuyendetsa msonkhanowu. Tonse tikuchita zimenezi pamodzi.” Wapolisiyo anachoka wosakhulupirira. Pamene magulu a zinenero zitatu onseŵa anapempherera pamodzi pemphero lomaliza, kunena pamodzi kuti “Amen” kunamveka m’sitediyamu monsemo ndipo obwera pamsonkhanowo anayamba kuwomba m’manja. Pafupifupi munthu aliyense anagwetsa misozi. Inde, misonkhano yaikulu ndi umbonidi wosangalatsa wa ubale wathu.​—Salmo 133:1. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 Onani masamba 66-77, 254-82 a buku la Jehovah’s Witnesses​—Proclaimers of God’s Kingdom, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.