Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Chofunika Kwambiri N’chiyani?

Kodi Chofunika Kwambiri N’chiyani?

Kodi Chofunika Kwambiri N’chiyani?

N’zosangalatsa kukhala ndi chinthu chofunika kwambiri. Koma kodi chinthu chake chingakhale chiyani? Ndalama zambiri? Ziŵiya za golide zokwera mtengo kapena zosapezekapezeka? Kutchuka ndi kudziŵika? Anthu ambiri amaona zinthu zimenezi kukhala zofunika kwambiri. Kukhala ndi zimenezi kumawathandiza kupeza zinthu zofunika pamoyo, moyo ungakhale watanthauzo kwambiri, anthu angawalemekeze ndiponso angakhale opambana. Kodi tikuyesetsa kuti tipeze zinthu zimenezi, ndi maganizo akuti zidzakwaniritsa zolinga ndi zofuna zathu za m’tsogolo?

NTHAŴI zambiri, anthu amaona chinthu kukhala chofunika kwambiri malinga ndi momwe chikuwathandizira pa zosoŵa zawo kapena zofuna zawo. Timakonda zinthu zimene zimatipatsa moyo wabwino ndiponso chiyembekezo cha tsogolo lotetezeka. Zinthu zimene zimatipatsa mpumulo, chilimbikitso, kapena kutchuka nthaŵi yomweyo, timaziona kukhala zofunika kwambiri. Komabe, kuona chinthu kukhala chofunika kwambiri malinga ndi zofuna kapena zokonda zathu zimene zimasinthasintha n’kusalingalira bwino kapena kusaganizira za m’tsogolo. Kunena zoona, chinthu chofunika kwambiri n’chomwe tifunika kukhala nacho kuposa china chilichonse.

Kodi chinthu chomwe tifunika kukhala nacho kuposa china chilichonse n’chiyani? Zonse n’chabe popanda chinthu chofunika kwambiri ichi​—moyo. Popanda moyo, sitingakhale. Mfumu Solomo ya Israyeli wakale inalemba kuti: “Koma akufa sadziŵa kanthu bi . . . Mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziŵa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.” (Mlaliki 9:5, 10) Tikafa, timakakamizika kusiya zinthu zathu zonse. Choncho, chofunika kwambiri kwa ife ndicho kupeza chinthu chimene chingateteze moyo wathu. Kodi chinthu chake n’chiyani?

Kodi N’chiyani Chingateteze Moyo Wathu?

Mfumu Solomo inati: “Ndalama zichinjiriza.” (Mlaliki 7:12) Ndalama zokwanira zingatithandize kupeza chakudya ndi nyumba yabwino. Ndalama zingatipangitse kukasangalala m’madera akutalikutali. Zingatithandize kupeza zomwe tikufuna ngati tasiya ntchito chifukwa cha ukalamba kapena matenda. Ndalama zimathandiza m’njira zambiri. Komabe, ndalama sizingateteze moyo. Mtumwi Paulo analangiza Timoteo kuti: “Lamulira iwo achuma m’nthaŵi ino ya pansi pano, kuti asadzikuze, kapena asayembekezere chuma chosadziŵika kukhala kwake, koma Mulungu.” (1 Timoteo 6:17) Ndalama zonse za padziko lapansi sizingatigulire moyo.

Onani zimene mwamuna wina dzina lake Hitoshi anakumana nazo. Mwamunayu anakulira m’banja losauka chotero ankafunitsitsa kulemera. Ankakhulupirira kwambiri kuti ndalama n’zamphamvu moti zingapangitse anthu kukukonda kapena kukukhulupirira. Kenako Hitoshi analandira mlendo yemwe anam’funsa ngati anali kudziŵa kuti Yesu Kristu anam’fera. Hitoshi anachita chidwi ndi funsoli chifukwa ankaganiza kuti palibe amene angafere munthu ngati iyeyo. Chotero anapita kukamvera nkhani ya Baibulo ya onse ndipo anadabwa kumva malangizo akuti ‘khalani ndi diso langwiro.’ Wokamba nkhaniyo anafotokoza kuti diso “langwiro” ndi diso loona za m’tsogolo ndipo limayang’ana pa zinthu zauzimu. (Luka 11:34) Hitoshi anayamba kutsogoza zinthu zauzimu m’moyo wake, m’malo movutika kufunafuna ndalama.

Chuma chingatipatsenso bata ndi kutiteteza nthaŵi zina. Kukhala ndi chuma chambiri kungathandize kuti tisamadere nkhaŵa kwambiri ndi zosoŵa za tsiku n’tsiku. Kukhala ndi nyumba yabwino m’dera losiririka kungatipangitse kuona ngati ndife opambana. Zovala za masitayelo ndiponso galimoto yabwino zingapangitse ena kusirira.

N’kokoma ‘kuona zabwino m’ntchito zathu zonse.’ (Mlaliki 3:13) Ndipo kukhala ndi chuma chambiri kungapangitse anthu amene timawakonda ‘kupumula, kudya, kumwa, ndi kukondwera.’ Komatu, chuma ndi m’chira wakhoswe sichichedwa kupululuka. Yesu Kristu pochenjeza za kuipa kokhumba kukhala wachuma, anati: “Moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.” (Luka 12:15-21) Chuma kaya chichuluke kapena chikhale chamtengo wapatali bwanji, sichingatipatse moyo.

Mwachitsanzo, Liz anakwatiŵa ndi mpondamakwacha. Iye akuti: “Tinali ndi nyumba yabwino ndiponso magalimoto aŵiri, ndipo chumacho chinatithandiza kupeza chilichonse chimene dziko limapanga . . . Simungakhulupirire kuti, ndinali kuvutikabe maganizo pankhani ya ndalama.” Iye akufotokoza kuti: “Tinali kusoŵa chinachake chofunika kwambiri. Zikuoneka kuti munthu ukakhala ndi ndalama zambiri, sukhala wotetezeka kwenikweni.”

Anthu ambiri amaonanso kutchuka ndi kudziŵika kukhala zinthu zofunika kwambiri popeza zingabweretse thamo ndi ulemu. M’dzikoli masiku ano ntchito yapamwamba ndi chinthu chimene anthu amasirira kwambiri. Kukhala ndi luso lapadera kungachititse kuti titchuke. Ena angatitamande, angalemekeze kwambiri malingaliro athu, ndiponso angayesetse kuti tiziwakonda. Zonsezi zingakhale zosangalatsa ndi zokhutiritsa. Komabe, zimatha m’kupita kwanthaŵi. Solomo anali ndi ulemerero ndi mphamvu zimene mfumu ingakhale nazo, koma anati: “Wanzeru saposa chitsiru kukumbukidwa . . . pakuti zonse zooneka kale zidzaiwalika.” (Mlaliki 2:16) Kutchuka kapena kudziŵika sikungapatse munthu moyo.

Celo yemwe ankasema ziboliboli anayamba kuona chinthu china kukhala chofunika kwambiri kuposa kutchuka. Popeza anali waluso, anam’sankha kupita kusukulu yowonjezera luso lakelo. Posakhalitsa, ofalitsa nkhani ndiponso ofufuza za ntchito zamanja anali kuyamikira ntchito yake. Ziboliboli zake zambiri ankazionetsa m’mizinda ikuluikulu ku Ulaya. Celo akuti: “Ndikuvomereza kuti nthaŵi inayake kusema kunali chinthu chofunika kwambiri m’moyo wanga. Komano, ndinazindikira kuti kupitiriza ntchito imeneyi kungafanane ndi kutumikira ambuye aŵiri. (Mateyu 6:24) Ndinatsimikiza kuti chofunika kwambiri chimene n’kanachita ndicho kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Choncho ndinasankha kusiya ntchito yosema ziboliboli.”

Kodi Chofunika Kwambiri N’chiyani?

Popeza popanda moyo palibe chimene chingakhale chatanthauzo kapena chofunika kwambiri, kodi tipeze chiyani chimene chidzatithandiza kukhalabe ndi moyo? Yehova Mulungu ndi amene anapereka moyo. (Salmo 36:9) Inde, “mwa iye tikhala ndi moyo ndi kuyendayenda.” (Machitidwe 17:28) Amapereka mphatso ya moyo wosatha kwa amene amawakonda. (Aroma 6:23) Kodi titani kuti atipatse mphatso imeneyi?

Kuti tilandire mphatso ya moyo wosatha tiyenera kupalana ubwenzi wolimba ndi Yehova. Choncho, kuyanjana naye n’kofunika kwambiri kuposa chilichonse chomwe tingakhale nacho. Tikatero timakhala ndi chiyembekezo chakuti tidzasangalala kwenikweni ndiponso kosatha. Komabe, ngati Mulungu satiyanja, tidzatha psiti. Chotero, n’zoonekeratu kuti chilichonse chimene chidzatithandiza kukhala paubale weniweni ndi Yehova ndicho chofunika kwambiri.

Chomwe Tiyenera Kuchita

Kuti tipambane, tiyenera kupeza chidziŵitso. Gwero la chidziŵitso cholondola ndilo Mawu a Yehova, Baibulo. Ndi lokhalo limene limatiuza zochita kuti tikondweretse Mulungu. Choncho tifunika kuphunzira Malemba mosamala. Kuphunzira mwakhama zambiri za Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu, kumatipatsa chidziŵitso chimene chimatsogolera ku “moyo wosatha.” (Yohane 17:3) Chidziŵitso chimenecho ndi chuma chofunika kuchisungitsitsa.​—Miyambo 2:1-5.

Zimene timadziŵa tikaphunzira Mawu a Mulungu zimatithandiza kuchita chinthu china​—kukhulupirira Yesu Kristu. Yehova walamula kuti onse amene amapita kwa Iye azidzera mwa Yesu. (Yohane 14:6) Ndipotu, “palibe chipulumutso mwa wina yense.” (Machitidwe 4:12) Sitidzapulumuka chifukwa cha ‘golidi ndi siliva, koma ndi mwazi wamtengo wapatali wa Kristu.’ (1 Petro 1:18, 19) Tiyenera kusonyeza chikhulupiriro chathu mwa kukhulupirira zimene Yesu anaphunzitsa ndi kutsatira chitsanzo chake. (Ahebri 12:1-3; 1 Petro 2:21) Ndipo nsembe yake ndi yamtengo wapatali kwabasi! Mapindu ake adzabweretsa tsogolo losatha kwa anthu onse. Podzaigwiritsa ntchito mokwanira, adzatipatsa mphatso yofunikadi kwambiri ya moyo wosatha.​—Yohane 3:16.

Yesu anati: “Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.” (Mateyu 22:37) Kukonda Yehova kumatanthauza kuti “tisunge malamulo ake.” (1 Yohane 5:3) Malamulo ake amafuna kuti tisakhale mbali ya dziko, tikhalebe ndi khalidwe labwino, ndi kuchirikiza mokhulupirika Ufumu wake. Ndimo mmene ‘tingasankhire moyo’ m’malo mwa imfa. (Deuteronomo 30:19) Ngati ‘tiyandikira kwa Mulungu, adzayandikira kwa ife.’​—Yakobo 4:8.

Chinthu chofunika kwambiri kuposa china chilichonse cha m’dziko ndicho kutsimikizira kuti tikuyanjana ndi Mulungu. Oyanjana ndi Mulungu ndi amene ali olemera kwambiri padziko lonse. Chotero, tiyesetse kupeza chinthu chofunika kwambiri​—kuyanjana ndi Yehova. Ndiyetu tiyeni timvere malangizo a mtumwi Paulo akuti: ‘Tsatani chilungamo, chipembedzo, chikhulupiriro, chikondi, chipiriro, chifatso. Limbani nayo nkhondo yabwino ya chikhulupiriro, gwirani moyo wosatha.’​—1 Timoteo 6:11, 12.

[Zithunzi patsamba 21]

Kodi chofunika kwambiri kwa inu n’chiyani? Kodi ndi ndalama, zinthu zimene mulinazo, kutchuka, kapena palinso china?

[Chithunzi patsamba 23]

Tifunika kuphunzira Malemba mosamala