Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi kulambira Yehova “mumzimu” kumatanthauzanji?

Yesu Kristu polalikira kwa mkazi wa ku Samariya yemwe anafika kudzatunga madzi pachitsime cha Yakobo pafupi ndi mudzi wa Sukari anati: “Mulungu ndiye mzimu; ndipo om’lambira Iye ayenera kum’lambira mumzimu ndi m’choonadi.” (Yohane 4:24) Kulambira koona kuyenera kuchitika “m’choonadi” mulingaliro lakuti kuzigwirizana ndi zimene Yehova Mulungu wavumbula m’Baibulo zokhudza iye ndi zofuna zake. Tiyeneranso kutumikira Mulungu “mumzimu” mulingaliro lakuti tikhale achangu ndipo mtima wachikondi ndi wachikhulupiriro utilimbikitse kuchita zimenezo. (Tito 2:14) Komabe, nkhaniyo imasonyeza kuti mawu a Yesu onena za ‘kulambira Mulungu mumzimu’ amatanthauza zambiri osati malingaliro amene timatumikira nawo Yehova okha.

Zomwe Yesu anakambirana ndi mkazi pachitsime paja sizinali zokhudza kukhala wachangu kapena wopanda changu pakulambira. Ngakhale kulambira konyenga kungachitidwe mwachangu ndiponso modzipereka. Komano, Yesu atanena kuti anthu sadzalambira Atate m’phiri la ku Samariya kapena kukachisi wa ku Yerusalemu​—omwe ndi malo enieni​—anatchula njira yatsopano yolambirira yogwirizana ndi mmene Mulungu alili. (Yohane 4:21) Yesu anati: “Mulungu ndiye mzimu.” (Yohane 4:24) Mulungu woona saoneka ndiponso sitingamukhudze. Kumulambira sikudalira kachisi kapena phiri looneka ndi maso. Chifukwa cha zimenezi, Yesu ankatanthauza mbali ya kulambira kosaoneka ndi maso.

Kuwonjezera pakulambira m’choonadi, kulambira kovomerezeka kuyeneranso kutsogozedwa ndi mzimu woyera​—mphamvu yogwira ntchito yosaoneka ya Mulungu. Mtumwi Paulo analemba kuti: ‘Mzimu [woyera] usanthula zonse, ngakhale zakuya za Mulungu.’ Iye anawonjezera kuti: “Sitinalandira ife mzimu wadziko lapansi, koma Mzimu wa kwa Mulungu, kuti tikadziŵe zimene zipatsidwa kwa ife ndi Mulungu kwaufulu.” (1 Akorinto 2:8-12) Kuti tilambire Mulungu movomerezeka, tiyenera kukhala ndi mzimu wake ndipo uzititsogolera nthaŵi zonse. Ndiponso, n’kofunika kuti malingaliro athu agwirizane ndi mzimu wa Mulungu mwakuphunzira ndi kuchita zomwe Mawu ake amanena.

[Chithunzi patsamba 28]

Lambirani Mulungu “mumzimu ndi m’choonadi”