Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

N’chifukwa chiyani Baibulo limanena kuti munthu ayenera kufuula ngati wina akufuna kumugwirira?

Munthu amene sanam’gwirirepo sangamvetse mokwanira mmene kugwiriridwa kungawonongere moyo wa munthu. Kugwiriridwako kumachititsa mantha kwambiri munthu amene wagwiriridwayo moti zikhoza kumuvutitsa maganizo moyo wake wonse. * Mtsikana wina wachikristu amene anagwiriridwa zaka zingapo zapitazo ananena kuti: “Sindingathe kufotokoza mantha adzaoneni amene ndinali nawo usiku umenewo kapena kupwetekedwa mtima kumene ndakhala ndikuvutika nako kuyambira nthaŵi imeneyo.” N’zomveka kuti ena amaona kuti kuli bwino osaganiza n’komwe za nkhani yochititsa mantha imeneyi. Komabe, kugwiriridwa kukuchitikadi m’dziko loipali.

Baibulo silipeŵa kufotokoza nkhani zina zokhudza kugwiriridwa kapena kufuna kugwiriridwa zimene zinachitika kalelo. (Genesis 19:4-11; 34:1-7; 2 Samueli 13:1-14) Koma limaperekanso malangizo ofotokoza zimene munthu ayenera kuchita ngati wina akufuna kumugwirira. Pa Deuteronomo 22:23-27 timapeza zimene Chilamulo chinanena pa nkhani imeneyi. Zimenezi zikukhudza mbali ziŵiri. Mbali yoyamba, mwamuna anapeza namwali m’mudzi ndiyeno n’kugona naye. Ngakhale zinali choncho, namwaliyo sanafuule kuti anthu amuthandize. Motero, iye ankakhala ndi mlandu “popeza sanafuula angakhale anali m’mudzi.” Akanafuula, anthu amene anali pafupi mwina akanatha kum’pulumutsa. Pa mbali yachiŵiri, mwamuna anapeza namwali kunja kwa mudzi kumene “[a]namgwira mwamunayo, nagona naye.” Podziteteza, namwaliyo “anafuula, koma panalibe wom’pulumutsa.” Mosiyana ndi namwali woyamba uja, namwali uyu mwachionekere sanalolere kugwiriridwa. Anamukana mwamunayo kwamtuwagalu, anafuula kuti anthu amuthandize, koma wogwirirayo anagonjetsa namwaliyo. Kufuula kwakeko kunatsimikizira kuti sankafuna kugwiriridwa. Motero, iye analibe mlandu.

Ngakhale kuti Akristu masiku ano satsatira Chilamulo cha Mose, mfundo za m’chilamulocho zingawatsogolere. Nkhani imene ili pamwambapa ikutsindika kufunika kokana ndi kufuulira thandizo. Anthu akuona kuti kufuula munthu wina akamafuna kukugwirira, ndi chinthu chanzerube mpaka pano. Katswiri wina wa nkhani zopeŵa upandu anati: “Mkazi akagwidwa, chida chake chabwino kwambiri ndicho kufuula.” Anthu ena angamve kufuula kwake ndipo angabwere kudzamuthandiza, kapena kufuula kwakeko kungachititse mantha wom’gwirirayo ndipo angamusiye. Mtsikana wina wachikristu amene munthu wina ankafuna kumugwirira anati: “Ndinafuula ndi mphamvu zanga zonse, ndipo anandisiya. Pamene anali kundiyandikira kachiŵiri, ndinafuula ndi kuthawa. Kale ndinkaganiza kuti, ‘Kodi kufuula kungandithandize bwanji ngati mwamuna wamphamvu zake wandigwira ali ndi cholinga chimodzi m’maganizo mwake?’ Koma ndaona kuti zimathandiza!”

Ngakhale ngati momvetsa chisoni mkaziyo wagonjetsedwa ndi kugwiriridwa, kulimbana kwake ndi munthuyo ndi kufuula kwake kuti athandizidwe sikuli kopanda pake. M’malo mwake, zimatsimikizira kuti anachita zonse zimene akanatha kuti amukanize wom’gwirirayo. (Deuteronomo 22:26) Ngakhale atakumana ndi zinthu zopweteka zimenezi, iye angakhalebe ndi chikumbumtima choyera, kudziona kuti ndi wofunika, ndi kutsimikiza kuti ndi woyera pamaso pa Mulungu. Zinthu zochititsa mantha zimene zamuchitikirazo zingamusiyire mabala m’maganizo, koma kudziŵa kuti anachita zonse zimene akanatha kuti amukanize wom’gwirirayo kudzathandiza kwambiri kuti achire pang’onopang’ono.

Pomvetsa tanthauzo la Deuteronomo 22:23-27, tiyenera kuzindikira kuti nkhani yaifupi imeneyi siikufotokoza mbali zonse. Mwachitsanzo, siikufotokoza chilichonse m’zochitika monga zoti mkazi wogwiriridwayo sangathe kufuula chifukwa chakuti ndi wosalankhula, wakomoka, kapena mantha amufoola kwambiri kapenanso akamulepheretsa kufuula mwa kum’gwira pakamwa kapena kum’mata pakamwa ndi tepi. Komabe, popeza Yehova amatha kupenda zochitika zonse, ngakhalenso maganizo a munthuyo, amasamalira nkhani zoterozo mwachifundo ndiponso mwachilungamo, pakuti “njira zake zonse ndi chiweruzo [“chilungamo,” NW].” (Deuteronomo 32:4) Iye amadziŵa zimene zinachitikadi ndiponso kuyesetsa kwa mkaziyo kuti amukanize wogwirirayo. Motero, munthu wogwiriridwa amene sanathe kufuula koma anachita zonse zimene akanatha malinga ndi mmene zinthu zinalili, angasiye nkhaniyo m’manja mwa Yehova.​—Salmo 55:22; 1 Petro 5:7.

Ngakhale zili choncho, akazi ena achikristu amene anagwidwa ndi kuipitsidwa akupitirizabe kuvutika maganizo kuti ali ndi mlandu. Poganizira zimene zinachitika, amaona kuti akanatha kuchita zambiri kuti alepheretse zimenezo kuchitika. Komabe, m’malo modziimba mlandu, anthu oterowo angapemphere kwa Yehova, kum’pempha kuti awathandize, ndi kukhulupirira kuti adzawasonyeza kukoma mtima kwake kwachikondi komwe n’kwakukulu.​—Eksodo 34:6; Salmo 86:5.

Motero, akazi achikristu amene pakalipano akuvutika ndi mabala a m’maganizo chifukwa chogwiriridwa, angakhulupirire kuti Yehova akumvetsa bwinobwino kuvutika maganizo kumene akulimbana nako. Mawu a Mulungu amawatsimikizira kuti: “Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi [“woswanyika,” NW].” (Salmo 34:18) Thandizo lina loti apirire kupwetekedwa mtima kwawo lingapezeke mwa kulandira thandizo lachifundo ndi kumvetsa bwino zinthu kwa okhulupirira anzawo mu mpingo wachikristu. (Yobu 29:12; 1 Atesalonika 5:14) Ndiponso, kuyesetsa kwa munthu wogwiriridwayo kuganizira kwambiri zinthu zolimbikitsa, kudzamuthandiza kukhala ndi “mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse.”​—Afilipi 4:6-9.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Ngakhale kuti nkhaniyi ikunena za kugwiriridwa kwa akazi, mfundo zimene tazifotokoza zikugwiranso ntchito kwa amuna amene anthu ena akufuna kuwagwirira.