Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Ndiye Mulungu Wofunika Kum’dziŵa

Yehova Ndiye Mulungu Wofunika Kum’dziŵa

Yehova Ndiye Mulungu Wofunika Kum’dziŵa

KODI zingakhale kuti mukuphonya kanthu kena kofunika pa moyo? Ngati mumadziŵa zochepa pankhani ya Mulungu, ndiye kuti mukuphonyadi. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti kudziŵa Mulungu wa m’Baibulo, monga mmene anthu ambiri aonera, kumabweretsa phindu lalikulu pa moyo. Phindu limeneli limayamba nthaŵi yomweyo ndipo limakhalapo kosatha.

Yehova Mulungu, Mlembi wa Baibulo, amafuna kuti tim’dziŵe. Wamasalmo analemba kuti: “Kuti adziŵe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.” Iye amadziŵa kuti ndife amene timapindula tikam’dziŵa. “Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula.” Kodi timapindula bwanji tikadziŵa Yehova Mulungu, Wam’mwambamwamba?​—Salmo 83:18; Yesaya 48:17.

Phindu lenileni limodzi n’loti timapeza malangizo amene angatithandize pamene tikumana ndi mavuto a tsiku ndi tsiku, timayembekezera motsimikiza zinthu zabwino m’tsogolo ndipo timakhalanso ndi mtendere wa m’mtima. Ndiponso, kum’dziŵa bwino kwambiri Yehova kumatichititsa kukhala ndi maganizo atsopano pa nkhani zofunika zimene anthu akukumana nazo masiku ano padziko lonse lapansi. Kodi ndi nkhani zotani zimenezi?

Kodi Moyo Wanu Uli ndi Cholinga?

Ngakhale kuti anthu apita patsogolo modabwitsa m’luso la zopangapanga, anthu masiku ano amafunsabe mafunso ofunika amodzimodzi akuti: ‘N’chifukwa chiyani ndili moyo? Kodi tsogolo langa ndi lotani? Kodi cholinga cha moyo n’chiyani?’ Ngati munthu sapeza mayankho okhutiritsa, moyo wake umakhala wopanda cholinga chenicheni. Kodi anthu ambiri amaona kuti ali ndi vuto limeneli? Kafukufuku amene anachitidwa ku Germany kumapeto a zaka za m’ma 1990 anasonyeza kuti theka la anthu omwe anafunsidwa nthaŵi zambiri kapena nthaŵi zina anaona kuti moyo umaoneka kuti ulibe cholinga. Mwina ndi mmene zilili kumene mukukhala.

Popanda cholinga m’moyo, munthu amakhala ndi maziko osalimba kwenikweni omangapo zolinga zake. Ena amayesa kuthetsa vuto limeneli mwa kuphunzira ntchito yapamwamba kwambiri kapena kukhala ndi chuma. Komabe, kupanda cholinga kungakhale kovutitsa. Kukhala wopanda cholinga pa moyo kumakhumudwitsa ena moti amafika posafunanso kukhala moyo. Zimenezi ndi zomwe zinachitikira mkazi wina wachitsikana wokongola. Malinga ndi kunena kwa nyuzipepala ya International Herald Tribune iye analeredwa “pakhomo la mwana alirenji ndiponso anali ndi mwayi wochita zinthu zambiri.” Ngakhale kuti anali ndi zonse zofunika pamoyo, iye anali wosungulumwa ndipo amaona kuti moyo wake unalibe cholinga. Iye anamwa mapilisi ogonetsa tulo ndipo anam’peza atamwalira. Mwina mukudziŵa anthu ena osungulumwa omwe anamwalira momvetsa chisoni.

Komano, kodi mwamvapo anthu ena akunena kuti sayansi ingatiuze zonse zokhudza moyo? Nyuzipepala ya mlungu ndi mlungu ya ku Germany yakuti Die Woche inati: “Ngakhale kuti sayansi ingakhale yolondola, ilibe malangizo okhudza nkhani zauzimu. Chikhulupiriro chakuti anthu ndiponso nyama zina zinachita kusinthika kuchokera ku zinthu zina n’chosakhutiritsa, ndiponso ngakhale sayansi ya masamu apamwamba kwambiri yomwe mfundo zake zimangosinthasintha ndi yosalimbikitsa ndiponso sithandiza kukhala ndi moyo wabwino.” Zimene asayansi atulukira zathandiza kwambiri pofotokoza mitundu yosiyanasiyana ya zinthu zamoyo ndi kufotokoza mmene zinthu zachilengedwe zimayendera ndiponso zinthu zimene zimathandiza kuti moyo ukhalepobe. Komabe, sayansi siingatiuze chifukwa chake tili moyo ndiponso mmene tsogolo lathu lilili. Ngati tidalira sayansi kotheratu, mafunso athu okhudza cholinga cha moyo sadzayankhidwa. Malinga ndi mmene nyuzipepala ya Süddeutsche Zeitung inanenera, chotsatira chake chimakhala chakuti “anthu ambiri amasoŵa chinthu choti chiwatsogolere.”

Kodi pali wina amene angatitsogolere kuposa Mlengi? Popeza iye poyamba anaika anthu padziko lapansi, iye ndi amene ayenera kudziŵa chifukwa chake anthuwo ali moyo. Baibulo limafotokoza kuti Yehova analenga anthu kuti akhale padziko lapansi ndi kulisamalira, kukhala oliyang’anira. M’zochita zawo zonse, anthu anafunika kuonetsa makhalidwe ake monga chilungamo, nzeru ndi chikondi. Tikadziŵa chifukwa chake Yehova anatilenga, timadziŵa chifukwa chake tili moyo.​—Genesis 1:26-28.

Kodi Mungachite Chiyani?

Bwanji ngati nthaŵi ya m’mbuyomu simunapeze mayankho okhutiritsa a mafunso akuti: ‘N’chifukwa chiyani ndili moyo? Kodi tsogolo langa ndi lotani? Kodi cholinga cha moyo n’chiyani?’ Baibulo limanena kuti mufunika kum’dziŵa bwino kwambiri Yehova. Ndipotu, Yesu anati: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.” Mukulimbikitsidwanso kukhala ndi makhalidwe a Mulungu, makamaka chikondi, ndipo chikhale cholinga chanu kuti mudzakhale mu Ufumu wa Umesiya wa Mulungu womwe ukubwera. Ndiyeno mudzakhala ndi cholinga pamoyo ndiponso tsogolo losangalatsa ndi lotsimikizirika. Mafunso ofunika kwambiri omwe akuvutitsani m’mbuyomu mosakayika adzayankhidwa.​—Yohane 17:3; Mlaliki 12:13.

Kodi mayankho a mafunso ofunikawo adzakukhudzani bwanji? Hans akudziŵa. * Zaka zapitazo Hans ankakhulupirira Mulungu pang’ono, koma chikhulupiriro chake sichimakhudza moyo wake. Hans anali kusangalatsidwa ndi mankhwala osokoneza bongo, akazi achiwerewere, chiwawa ndiponso njinga zamoto. Iye anati: “Koma moyo unali wopanda cholinga, wosasangalatsa kwenikweni.” Pamene anali ndi zaka pafupifupi 25, Hans anafuna kudziŵa Mulungu bwinobwino mwa kuŵerenga Baibulo mosamalitsa. Atam’dziŵa bwino kwambiri Yehova ndi kudziŵa cholinga cha moyo, Hans anasintha makhalidwe ake ndipo anabatizidwa kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova. Iye wakhala mtumiki wanthaŵi zonse zaka khumi zapitazi. Iye moona mtima anati: “Kutumikira Yehova ndiko chinthu chabwino kwambiri pa moyo wa munthu. Palibe chilichonse chimene chingafanane ndi zimenezi. Kudziŵa Yehova kwachititsa moyo wanga kukhala ndi cholinga.”

Mwachionekere, cholinga cha moyo si nkhani yokha imene imadetsa nkhaŵa anthu ambiri. Pamene zinthu m’dziko zikuipiraipira, anthu ambirimbiri amavutika ndi nkhani inanso yofunika.

N’chifukwa Chiyani Zimenezi Zinachitika?

Tsoka likachitika, anthu omwe akhudzidwawo amakhala ndi funso lakuti: N’chifukwa chiyani zimenezi zinachitika? Kupirira kuvutika maganizo chifukwa cha tsoka, mokulira kumadalira kupeza yankho loyenera la funso limeneli. Ngati yankho lokhutiritsa silikupezeka, mavuto amakhalapobe ndipo wokhudzidwayo angavutike kwambiri mumtima. Mwachitsanzo, taonani zimene zinachitikira Bruni.

Bruni yemwe tsopano ndi mayi wachikulire anati: “Zaka zingapo zapitazi mwana wanga wamkazi wakhanda anamwalira. Popeza ndinali kukhulupirira Mulungu, ndinapempha wansembe wa m’dera lathu kuti andithandize. Iye anandiuza kuti Mulungu anamutenga Susanne kupita kumwamba, kumene iye tsopano ndi mngelo. Chifukwa cha kumwalira kwake, zinthu zonse m’moyo wanga zinasokonezeka ndiponso ndinada Mulungu chifukwa choti anam’tenga.” Kwa zaka zingapo Bruni anapitirizabe kuwawidwa mtima ndi kuvutika. “Ndiyeno wa Mboni za Yehova anandiuza mwa kundisonyeza m’Baibulo kuti panalibe chifukwa choti ndidane ndi Mulungu. Yehova sanam’tenge Susanne kupita kumwamba ndipo iye sali mngelo. Iye anadwala chifukwa cha kupanda ungwiro kwa anthu. Susanne ali m’tulo taimfa, kuyembekeza kuti Yehova adzamuukitse. Ndinaphunziranso kuti iye anapanga anthu kuti akhale ndi moyo kosatha m’paradaiso padziko lapansi, ndipo zimenezi zidzachitika posachedwapa. Pamene ndinayamba kudziŵa kuti Yehova ndi wotani, ndinayandikira kwa iye ndipo kuwawidwa mtima kwanga kunayamba kuchepa.”​—Salmo 37:29; Machitidwe 24:15; Aroma 5:12.

Anthu ambirimbiri amakhudzidwa ndi kuvutika m’njira zosiyanasiyana. Angakhale mavuto okhudza iwo okha, nkhondo, njala kapena masoka achilengedwe. Mtima wa Bruni unakhala pansi atadziŵa kuchokera m’Baibulo kuti Yehova si amene akuchititsa mavuto, sichinali cholinga chake kuti anthu azivutika ndiponso kuti posachedwapa adzathetsa mavuto. Kuwonjezeka kwa zinthu zoipa ndi chizindikiro choti tsopano tikukhala “m’masiku otsiriza” a dongosolo lino la zinthu. Kusintha kwakukulu kwa zinthu kukhala zabwino kumene ife tonse timafuna kuli pafupi kuchitika.​—2 Timoteo 3:1-5; Mateyu 24:7, 8.

Kum’dziŵa Mulungu

Hans ndi Bruni ankadziŵa Mulungu pang’ono. Iwo ankam’khulupirira koma sankadziŵa zambiri za iye. Pamene anakhala ndi nthaŵi yom’dziŵa bwinobwino Yehova, khama lawo linapindula. Iwo anapeza mayankho oyenera a mafunso omwe alipo masiku ano. Zimenezi zinawachititsa kukhala ndi mtendere wam’mtima ndiponso kuyembekezera zinthu zabwino m’tsogolo. Zimenezi zachitikiranso atumiki a Yehova mamiliyoni ambiri.

Kudziŵa Yehova kumayamba mwa kupenda Baibulo mosamalitsa, limene limatiuza za iye ndi zimene amafuna kwa ife. Zimenezi n’zomwe ena anachita m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino. Luka, wolemba zochitika zakale ndiponso sing’anga analemba kuti anthu a mpingo wachiyuda ku Bereya, m’dziko la Greece, “analandira mawu [kwa Paulo ndi Sila] ndi kufunitsa kwa mtima wonse, nasanthula m’malembo masiku onse, ngati zinthu zinali zotero.”​—Machitidwe 17:10, 11.

Akristu a m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino ankasonkhananso pamodzi m’mipingo. (Machitidwe 2:41, 42, 46; 1 Akorinto 1:1, 2; Agalatiya 1:1, 2; 2 Atesalonika 1:1) Zimenezi zikuchitikanso masiku ano. Mipingo ya Mboni za Yehova imasonkhana pamodzi pamisonkhano yomwe imakonzedwa makamaka ndi cholinga chothandiza anthu kuyandikira kwa Yehova ndi kusangalala pom’tumikira. Kusonkhana ndi Mboni za kudera lanu kuli ndi phindu linanso. Popeza anthu pang’ono ndi pang’ono amafanana ndi Mulungu amene amam’lambira, Mboni za Yehova zimasonyeza, ngakhale ndi pamlingo wochepa, makhalidwe amene Yehova amawasonyeza. Chotero, kusonkhana ndi Mboni kumatithandiza kum’dziŵa bwino kwambiri Yehova.​—Ahebri 10:24, 25.

Kodi zimenezi zikuoneka ngati n’chintchito chachikulu chongofuna kum’dziŵa Munthu mmodzi yekha basi? Ndithudi khama n’lofunika. Koma kodi si chimodzimodzi ndi zinthu zambiri zimene mumafuna kukhala nazo pamoyo? Taganizirani khama limene wamaseŵero wotchuka amakhala nalo pokonzekera. Mwachitsanzo, Jean-Claude Killy, katswiri wampikisano wa olimpiki wa ku France, yemwe anapata mendulo ya golide anafotokoza zimene zimafunika kuti munthu akhale wamaseŵero wopambana. Iye anati: “Munthu afunika kuyamba zaka khumi pasadakhale ndipo akonzekeretu zimenezi kwa zaka zambiri ndi kumaganizira mpikisano tsiku lililonse . . . Ndi ntchito ya masiku onse 365 a pachaka, yomwe munthu afunika kuiganizira ndiponso kuigwira kumene.” Nthaŵi yonseyo ndi khama lonselo n’longofuna kudzatenga nawo mbali m’mpikisano womwe mwina ungachitike kwa mphindi khumi zokha. Kuli bwanji ndi chinthu chofunika kwambiri ndi chokhalitsa chimene mungapeze mwakudziŵa Yehova!

Ubwenzi Umene Umakulirakulira

Kodi ndani amene akufuna kuphonya kanthu kofunika kwambiri pamoyo? Palibe. Chotero, ngati muona kuti moyo wanu ulibe cholinga chenicheni kapena ngati mumafuna kudziŵa chifukwa chimene mavuto amachitikira, tsimikizani mtima kwambiri kum’dziŵa Yehova, Mulungu wa m’Baibulo. Kuphunzira za iye kungasinthe moyo wanu kuti ukhale wabwino kosatha.

Kodi padzakhala nthaŵi imene tidzasiya kuphunzira za Yehova? Anthu amene akhala akum’tumikira kwa zaka zambiri amakhala odabwa kuona zimene aphunzira ndiponso zinthu zatsopano zimene akuphunzirabe za iye. Kuphunzira zinthu zimenezi kumatisangalatsa ndipo kumatiyandikizitsa kwa iye. Tiyeni tigwirizane ndi mawu a mtumwi Paulo, amene analemba kuti: “Ha! kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziŵa kwake kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweruzo ake, ndi njira zake n’zosalondoleka! Pakuti anadziŵitsa ndani mtima wake wa Ambuye? Kapena anakhala mphungu wake ndani?”​—Aroma 11:33, 34.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 Mayina asinthidwa.

[Mawu Otsindika patsamba 5]

Anthu amafunsabe mafunso ofunika amodzimodzi akuti: ‘N’chifukwa chiyani ndili moyo? Kodi tsogolo langa ndi lotani? Kodi cholinga cha moyo n’chiyani?’

[Mawu Otsindika patsamba 6]

“Pamene ndinayamba kudziŵa kuti Yehova ndi wotani, ndinayandikira kwa iye”

[Mawu Otsindika patsamba 7]

“Kutumikira Yehova ndiko chinthu chabwino kwambiri pa moyo wa munthu. Palibe chilichonse chimene chingafanane ndi zimenezi. Kudziŵa Yehova kwachititsa moyo wanga kukhala ndi cholinga”