Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tsiku Lofunika Kwambiri

Tsiku Lofunika Kwambiri

Tsiku Lofunika Kwambiri

LINALI tsiku limene linasinthiratu tsogolo la anthu kukhala labwino. Palibe tsiku lina limene limakhudza tsogolo la anthu kuposa limeneli. Ndi tsiku limene Yesu anamaliza zonse zimene anabwerera kudzachita padziko lapansi. Atatsala pang’ono kufa pamtengo wozunzirapo, anafuula kuti: “Kwatha.” (Yohane 19:30) Kodi Yesu anabwera kudzatani padziko lapansi?

Baibulo limati: “Mwana wa munthu sanadza kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.” (Mateyu 20:28) Yesu anapereka moyo wake kuti anthu apulumutsidwe ku uchimo ndi imfa zimene amabadwa nazo. Indedi, “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Nsembe ya Yesu ndi yofunikatu kwambiri!

Tsiku la imfa ya Yesu ndi tsiku lofunika kwambiri pa chifukwa chinanso. Patsiku limeneli, Mwana wa Mulungu anaphunzitsa atumwi ake mfundo zabwino zedi zimene zikanawathandiza kukhalabe okhulupirika. Si mmene mawu ake omaliza kwa ophunzirawo anakhudzira mitima yawo! Kodi anawaphunzitsa zotani? Kodi tingapindule chiyani ndi zimene Yesu anawaphunzitsa? Mafunso ameneŵa ayankhidwa mu nkhani yotsatirayi.