Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Milomo ya Ntheradi Idzakhala Nthaŵi Zonse’

‘Milomo ya Ntheradi Idzakhala Nthaŵi Zonse’

‘Milomo ya Ntheradi Idzakhala Nthaŵi Zonse’

LILIME lingawononge moyo wonse wa munthu monga mmene moto wochepa ungawotchere nkhalango yathunthu ndi kuiwononga. Lilime lingadzaze ndi ululu, koma lingakhalenso “mtengo wa moyo.” (Miyambo 15:4) Lili ndi mphamvu ya moyo ndi imfa. (Miyambo 18:21) Lilime lathu, lomwe n’kachiwalo kakang’ono, lili ndi mphamvu zimenezo zimene zingadetse thupi lonse. (Yakobo 3:5-9) N’kwanzeru kulamulira lilime lathu.

Mbali yachiŵiri ya chaputala 12 cha buku la m’Baibulo la Miyambo, Mfumu Solomo ya Israyeli wakale inapereka malangizo opindulitsa kwambiri amene angatithandize kulamulira kalankhulidwe kathu. Mwa kugwiritsa ntchito miyambi yaifupi koma yatanthauzo, mfumu yanzeruyo inasonyeza kuti mawu amene munthu walankhula amakhala ndi zotsatira zake ndiponso amavumbula kwambiri khalidwe la munthuyo. Malangizo ouziridwa a Solomo ndi ofunika kwambiri kwa munthu aliyense amene akufuna ‘kusunga pakhomo pa milomo yake.’​—Salmo 141:3.

‘Kulakwa Kumene Kumatchera Msampha’

Solomo anati: “M’kulakwa kwa milomo muli msampha woipa; koma wolungama amatuluka m’mavuto.” (Miyambo 12:13) Kunama ndiko kulakwa kwa milomo kumene kumakhala msampha wakupha munthu wokonda kunamayo. (Chivumbulutso 21:8) Chinyengo chingaoneke ngati njira yosavuta yopulumukira chilango kapena kupeŵa vuto lina lake. Koma kodi si zoona kuti bodza limodzi limayambitsa mabodza ena? Monga mmene munthu amene amayamba kutchova njuga ndi ndalama zochepa amatengeka kuyamba kubetcherana ndalama zambirimbiri pofuna kuti abwezeretse ndalama zimene wadyeredwa, munthu wonama amapezeka kuti wakodwa mumsampha wobwereza kunamako.

Kulakwa kwa milomo kumatchera msampha m’njira inanso yakuti munthu wonamiza enayo angafike podzinamiza yekha. Mwachitsanzo, munthu wabodza angaganize mosavuta kuti iye amadziŵa zambiri ndiponso ndi waluso, pamene zoona zake n’zakuti amangodziŵa zochepa chabe. Motero, moyo wake umayamba kudalira bodza basi. Inde, “adzidyoletsa yekha m’kuona kwake, kuti anthu sadzachipeza choipa chake ndi kukwiya nacho.” (Salmo 36:2) Ee, bodza limakhala msampha. Koma wolungama, sangadziike m’mavuto ngati amenewo. Ngakhale atavutika motani, sangalankhule bodza kuti zimuyendere bwino.

‘Chipatso Chimene Chimakhutitsa’

Mtumwi Paulo anachenjeza kuti: “Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.” (Agalatiya 6:7) Mosakayika, mfundo imeneyi imagwiranso ntchito pa kalankhulidwe kathu ndiponso zochita zathu. Solomo anati: “Munthu amakhuta zabwino ndi zipatso za m’kamwa mwake; zochita za manja ake zidzabwezedwa kwa iye.”​Miyambo 12:14.

Pakamwa pamene “palankhula zanzeru” pamatulutsa chipatso chimene chimakhutitsa. (Salmo 37:30) Munthu kuti akhale wanzeru afunika kudziŵa zinthu, koma palibe munthu amene amadziŵa zonse. Aliyense afunika kumvetsera malangizo abwino ndi kuwatsatira. Mfumu ya Israyeli inati: “Njira ya chitsiru n’njolungama pamaso pakepake; koma wanzeru amamvera uphungu.”​Miyambo 12:15.

Yehova amatipatsa malangizo abwino kudzera m’Mawu ake ndiponso kudzera m’gulu lake pogwiritsa ntchito zofalitsa zimene “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amapereka. (Mateyu 24:45; 2 Timoteo 3:16) N’kupusatu kukana malangizo abwino ndi kuumirira maganizo athu! Tiyenera ‘kukhala wotchera khutu’ pamene Yehova, “amene aphunzitsa munthu nzeru,” atilangiza kudzera m’njira imene akuigwiritsa ntchito polankhula nafe.​—Yakobo 1:19; Salmo 94:10.

Kodi munthu wanzeru ndi munthu wopusa amachita bwanji akanyozedwa kapena kuneneredwa zachipongwe? Solomo akuyankha kuti: “Mkwiyo wa chitsiru udziŵika posachedwa; koma wanzeru amabisa manyazi.”​Miyambo 12:16.

Munthu wopusa akalakwiridwa, amakwiya mwamsanga, “posachedwa.” Koma munthu wanzeru amapempherera mzimu wa Mulungu kuti athe kudziletsa. Iye amapatula nthaŵi kuti asinkhesinkhe malangizo a m’Mawu a Mulungu ndipo amasinkhasinkhanso moyamikira mawu a Yesu akuti: “Amene adzakupanda iwe patsaya lako lamanja, um’tembenuzire linanso.” (Mateyu 5:39) Pofuna ‘kusabwezera munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa,’ munthu wanzeru amaletsa milomo yake kuti asalankhule mwansontho. (Aroma 12:17) Ifenso tikangotayira ku nkhongo mnyozo mwa njira imeneyi, timapeŵa mikangano ina.

‘Lilime Limene Limalamitsa’

Kulakwa kwa milomo kungawononge kwambiri zinthu pa milandu. Mfumu ya Israyeli inati: “Wolankhula ntheradi aonetsa chilungamo; koma mboni yonama imanyenga.” (Miyambo 12:17) Mboni yoona imalankhula ntheradi chifukwa chakuti umboni wake umakhala wodalirika ndiponso wokhulupirika. Mawu ake amathandiza kuti pachitike chilungamo. Koma mboni yonama imakhala ndi chinyengo chokhachokha ndipo imalimbikitsa kuti pasachitike chilungamo.

Solomo anapitiriza kuti: “Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga; koma lilime la anzeru lilamitsa.” (Miyambo 12:18) Mawu angapyoze ngati lupanga, kuwononga maubwenzi ndi kuyambitsa mavuto. Kapena angakhale abwino ndi osangalatsa, ndipo angalimbitse maubwenzi. Kodi si zoona kuti kutchulana mayina amwano, kukalipirana, kudzudzula kosalekeza, ndiponso mawu onyoza amapyoza ndipo amapweteka mtima wa munthu kwa nthaŵi yaitali? Zimakhala bwinotu kwambiri kukonza zinthu tikalakwitsa pambali imeneyi mwa kulankhula mawu olamitsa popepesa mochokera pansi pa mtima!

M’nthaŵi zovuta zimene tikukhala zino, n’zosadabwitsa kuti ambiri ndi “a mtima wosweka” ndiponso “a mzimu woswanyika.” (Salmo 34:18, NW) Kodi si zoona kuti pamene ‘tilimbikitsa amantha mtima [“ovutika maganizo,” NW]’ ndi ‘kuchirikiza ofooka’ timagwiritsa ntchito mphamvu yochiritsa ya mawu amene talankhula? (1 Atesalonika 5:14) Inde, mawu achifundo angalimbikitse achinyamata amene akumenyera nkhondo kuti asatsatire zochita za anzawo zimene zingawasokoneze. Kulankhula moganizira ena kungatsimikizire munthu wachikulire kuti ndi wofunika ndiponso wokondedwa. Mawu achifundo angasangalatse anthu amene akudwala. Ngakhalenso chidzudzulo chimakhala chosavuta kuchilandira chikaperekedwa “mu mzimu wa chifatso.” (Agalatiya 6:1) Ndipotu, lilime la munthu amene amaligwiritsa ntchito kuuza anthu omvera uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu limalamitsa kwambiri!

‘Lilime Limene Limakhalitsa’

Solomo pogwiritsa ntchito “mlomo” monga liwu lofanana ndi “lilime,” akufotokoza kuti: “Mlomo wa ntheradi ukhazikika nthaŵi zonse; koma lilime lonama likhala kamphindi.” (Miyambo 12:19) Mawu akuti “mlomo wa ntheradi” m’Chihebri ndi mawu osonyeza chinthu chimodzi ndipo ali ndi tanthauzo lokulirapo osati kungolankhula zoona chabe. Buku lina linati mawu ameneŵa amasonyeza makhalidwe onga kukhalitsa ndiponso kudalirika. Ilo linatinso: “Kalankhulidwe kotere kamakhala . . . mpaka kalekale chifukwa kamapezeka kuti n’kodalirika, zimene zikusiyana ndi lilime labodza . . . limene linganyenge kwa kanthaŵi koma silingakhalitse ngati litayesedwa.”

Mfumu yanzeruyo inati: “Chinyengo chili m’mitima ya oganizira zoipa; koma aphungu a mtendere amakondwa.” Ndiyeno inawonjezera kuti: “Palibe vuto lidzagwera wolungama; koma amphulupulu adzadzazidwa ndi zoipa.”​Miyambo 12:20, 21.

Anthu okonza zoipa angayambitse mavuto aakulu. Koma aphungu a mtendere amakondwa chifukwa chochita zabwino. Amasangalalanso kuona zotsatira zabwino. Kuposa zonsezi, Mulungu amawayanja, chifukwa “milomo yonama inyansa Yehova; koma ochita ntheradi am’sekeretsa.”​Miyambo 12:22.

‘Kalankhulidwe Kamene Kamabisa Zomwe Munthu Ukudziŵa’

Pofotokoza kusiyana kwinanso kwa munthu amene amasamala kalankhulidwe kake ndi amene satero, mfumu ya Israyeli inati: “Munthu wanzeru abisa zomwe adziŵa; koma mtima wa opusa ulalikira utsiru.”​Miyambo 12:23.

Munthu wanzeru amadziŵa nthaŵi imene ayenera kulankhula ndi nthaŵi imene sayenera kulankhula. Amabisa zomwe adziŵa mwa kudziletsa kuti asasonyeze mwamatama zimene akudziŵa. Zimenezi sizikutanthauza kuti nthaŵi zonse amabisa zimene akudziŵa. M’malo mwake, iye amasonyeza zimenezo mwanzeru. Koma wopusa amafulumira kulankhula ndipo amachititsa kuti kupusa kwakeko kuonekere. Ndiyetu tiyeni tisamachulutse zolankhula ndipo lilime lathu lizipeŵa kudzikudza.

Popitirizabe kusiyanitsa zinthu, Solomo anafotokoza mfundo yomveka bwino yokhudza khama ndi ulesi. Anati: “Dzanja la akhama lidzalamulira; koma wolesi adzakhala ngati kapolo.” (Miyambo 12:24) Kugwira ntchito mwakhama kungachititse munthu kutukuka ndi kudzidalira pankhani za chuma, koma ulesi ungachititse munthu kukhala kapolo. Katswiri wina anati: “M’kupita kwa nthaŵi, munthu waulesi adzakhala kapolo wa munthu wakhama.”

‘Mawu Amene Amakondweretsa’

Mfumu Solomo inabwereranso pa nkhani ya kalankhulidwe ikuyang’anitsitsa chibadwa cha munthu. Inati: “Nkhaŵa iweramitsa mtima wa munthu; koma mawu abwino aukondweretsa.”​Miyambo 12:25.

Pali nkhaŵa zambiri zimene zingachititse mtima kulema ndi chisoni. Chimene chikufunika kuti kulemako kupepuke ndiponso kuti mtima ukondwere ndicho mawu abwino olimbikitsa a munthu wachifundo. Koma kodi anthu ena angadziŵe bwanji kuti tili ndi nkhaŵa yaikulu mumtima mwathu ngati sitiwauza nkhaŵa yathuyo? Inde, tikamavutika maganizo, tifunika kufotokozera zakukhosi munthu wachifundo amene angatithandize. Ndiponso kufotokoza mmene tikumvera kumachepetsa kuvutika mtima. Motero, ndi bwino kuuza mnzathu amene tili naye pa banja, kholo, kapena mnzathu wachifundo ndiponso wokhwima mwauzimu.

Kodi si zoona kuti mawu olimbikitsa kwambiri kuposa ena alionse ndi amene ali m’Baibulo? Motero tiyenera kuyandikira kwa Mulungu mwa kusinkhasinkha moyamikira Mawu ake ouziridwa. Kusinkhasinkha kumeneko kungasangalatsedi mtima wovutika ndipo kungawalitse maso achisoni. Wamasalmo akutsimikizira zimenezi ponena kuti: “Malamulo a Yehova ali angwiro, akubwezera moyo; mboni za Yehova zili zokhazikika, zakuwapatsa opusa nzeru; malangizo a Yehova ali olungama, akukondweretsa mtima: malamulo a Yehova ali oyera, akupenyetsa maso.”​—Salmo 19:7, 8.

Njira Yopindulitsa

Posiyanitsa njira ya munthu woongoka ndi ya munthu woipa, mfumu ya Israyeli inati: “Wolungama atsogolera mnzake; koma njira ya oipa iwasokeretsa.” (Miyambo 12:26) Munthu wolungama amasamala posankha anthu amene angacheze nawo ndiponso anzake. Amasankha mwanzeru, kupeŵa kucheza ndi anthu olakwika. Koma oipa satero popeza amakana malangizo ndipo amaumirira maganizo awo. Amanyengeka ndipo amasokera.

Kenako Mfumu Solomo inafotokoza kusiyana kwa ulesi ndi khama m’lingaliro lina. Inati: “Wolesi samaotcha nyama yake anaigwira; koma wolungama [“wakhama,” NW] amalandira chuma chopambana cha anthu.” (Miyambo 12:27) Inde, munthu waulesi saotcha nyama yake. N’chifukwa chake, iye sangamalize chinthu chimene wayamba kuchichita. Koma khama limayendera limodzi ndi chuma.

Ulesi ndi wovulaza kwambiri moti mtumwi Paulo anaona kuti kunali koyenera kuwalembera Akristu anzake a ku Tesalonika ndi kuwongolera anthu ena amene ‘ankayenda dwakedwake,’ osagwira ntchito m’pang’ono pomwe koma kumangolimbana ndi nkhani zoti sizinali kuwakhudza. Anthu oterewo analemetsa kwambiri anzawo. Chifukwa cha zimenezi, Paulo anawalangiza mosapita m’mbali, kuwadandaulira kuti “agwire ntchito pokhala chete, nadye chakudya cha iwo okha.” Ndipo ngati sakanatsatira langizo lamphamvu limeneli, Paulo analangiza ena mumpingomo kuti ‘abwevuke’ kwa anthu oterowo, kuwapeŵa, mwachionekere sanayenera kucheza nawo.​—2 Atesalonika 3:6-12.

Tiyenera kumvera langizo la Solomo loti tizikhala akhama ndiponso langizo lake la mmene tingagwiritsire ntchito lilime lathu. Tiyeni tiyesetse kugwiritsa ntchito kachiwalo kakang’ono kameneka pochiritsa ndi kusangalatsa ena pamene tikupeŵa kulakwa kwa milomo ndiponso titsatire njira yoongoka. Solomo akutitsimizira kuti: “M’khwalala la chilungamo muli moyo; m’njira ya mayendedwe ake mulibe imfa.”​Miyambo 12:28.

[Zithunzi patsamba 27]

“Wanzeru amamvera uphungu”

[Zithunzi patsamba 28]

Lilime la anzeru lilamitsa”

[Chithunzi patsamba 29]

Kumuuza zakukhosi mnzathu wodalirika kungatithandize kupeza chilimbikitso

[Chithunzi patsamba 30]

Kusinkhasinkha moyamikira Mawu a Mulungu kumasangalatsa mtima