Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Sitingapeŵe Kusankha Zochita

Sitingapeŵe Kusankha Zochita

Sitingapeŵe Kusankha Zochita

NTHAŴI ina Napoleon Bonaparte, mfumu ya ku France ya m’ma 1800, anati: “Palibe chinthu chovuta kwambiri komanso chamtengo wapatali ngati kutha kusankha zochita.” Mungavomereze kuti zimenezi n’zoona, popeza nthaŵi zambiri anthu amasangalala kulamulira moyo wawo. Komanso, anthu aona kuti kusankha zochita n’kovuta.

Kaya n’kovuta kapena ayi, sitingapeŵe kusankha zochita. Tsiku lililonse timafunika kuchita zimenezi. Tikadzuka m’maŵa, timafunika kusankha zoti tivale, zoti tidye pa chakudya cham’maŵa, ndiponso mmene tichitire zinthu zina zambiri patsikulo. Zambiri mwa zosankha zimenezi n’zazing’ono. Kaŵirikaŵiri sitiziganizira mofatsa. Si nthaŵi zambiri zimene timasoŵa tulo chifukwa choganizira ngati tinasankha zinthu zimenezi mwanzeru.

Komano, zina zimene timasankha kuchita zimakhala zazikulu zedi. Achinyamata ambiri m’dziko la masiku ano ayenera kusankha zochita pamoyo wawo. Ayenera kusankha maphunziro amene akufuna ndiponso kuti adzafike nawo pati. M’kupita kwa nthaŵi ambiri a iwo adzafunika kusankha kaya kuloŵa m’banja kapena kupitirizabe kukhala opanda mnzawo wa muukwati. Amene akufuna kuloŵa m’banja ayenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndine wamkulu ndi wokhwima mokwanira moti n’kuloŵa m’banja? Kodi ndimafuna munthu womanga naye banja wotani, kapena chofunika kwambiri, kodi ndimafunikira munthu womanga naye banja wotani?’ Ndi zinthu zochepa chabe zimene timasankha kuchita zimene zimakhudza kwambiri moyo wathu monga mmene kusankha munthu womanga naye banja kumachitira.

Pa zinthu zofunika kwambiri, n’kofunika kusankha zochita mwanzeru. Izi n’zofunika chifukwa chakuti kusangalala kwathu pamoyo kumadalira kwambiri kuchita zimenezi. Anthu ena amaona kuti akhoza kusankha bwino zochita zoterozo ndipo amakana anthu kuwathandiza. Kodi zimenezo ndi nzeru? Tiyeni tione.

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

Napoleon: From the book The Pictorial History of the World