Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Wonjezerani Kudziletsa pa Chizindikiritso Chanu

Wonjezerani Kudziletsa pa Chizindikiritso Chanu

Wonjezerani Kudziletsa pa Chizindikiritso Chanu

‘Wonjezerani . . . kudziletsa pa chizindikiritso chanu.’​—2 PETRO 1:5-8.

1. Kodi mavuto ambiri a anthu amadza chifukwa cholephera kuchita chiyani?

PANTCHITO ina yaikulu yolimbana ndi kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, achinyamata m’dziko la United States anawalimbikitsa kuti: “Muzingoti toto.” Bwenzi zinthu zili bwino kwambiri kukanakhala kuti aliyense amangoti toto osati mankhwala osokoneza bongo okha koma atamateronso ndi kumwa moŵa kwambiri, makhalidwe oipa kapena achiwerewere, kuchita chinyengo pa malonda, ndiponso ‘kuchita zofuna za thupi.’ (Aroma 13:14) Komano ndani anganene kuti nthaŵi zonse n’zophweka kunena kuti toto?

2. (a) Kodi ndi zitsanzo ziti za m’Baibulo zosonyeza kuti sizachilendo kuvutika kunena kuti toto? (b) Kodi zitsanzo zimenezi ziyenera kutilimbikitsa kuchitanji?

2 Popeza kuti kudziletsa n’kovuta kwa anthu onse opanda ungwiro, tiyenera kukhala ndi chidwi chofuna kudziŵa mmene tingagonjetsere vuto lililonse lomwe takumana nalo. Baibulo limatiuza za anthu akale amene anayesetsa kutumikira Mulungu koma nthaŵi zina zinkawavuta kungonena kuti toto. Kumbukirani Davide ndi tchimo lake lochita chigololo ndi Bateseba. Tchimoli linaphetsa mwana wawo wa chigololocho ndiponso mwamuna wa Bateseba, ndipo onse aŵiriŵa anali osalakwa. (2 Samueli 11:1-27; 12:15-18) Kapena taganizirani za mtumwi Paulo, yemwe anaulula kuti: “Pakuti chabwino chimene ndichifuna, sindichichita; koma choipa chimene sindichifuna, chimenecho ndichichita.” (Aroma 7:19) Kodi inu zimakuchitikiraninso zimenezi nthaŵi zina? Paulo anapitiriza kuti: “Pakuti monga mwa munthu wa mkati mwanga, ine ndikondwera ndi chilamulo cha Mulungu: koma ndiona lamulo lina m’ziŵalo zanga, lilikulimbana ndi lamulo la mtima wanga, ndi kundigonjetsa kapolo wa lamulo la m’ziŵalo zanga. Munthu wosauka ine; adzandilanditsa ndani m’thupi la imfa iyi?” (Aroma 7:22-24) Zitsanzo za m’Baibulo ziyenera kutilimbikitsa kuti tisasiye nkhondo yathu yofuna kuti tizikhala odziletsa kwambiri.

Timachita Kuphunzira Kudziletsa

3. Fotokozani chifukwa chake sitingayembekezere kudziletsa kukhala kosavuta.

3 Kudziletsa, komwe kumaphatikizapo kutha kunena kuti toto, anakutchula pa 2 Petro 1:5-7 limodzi ndi chikhulupiriro, ukoma, chizindikiritso, chipiriro, chipembedzo, chikondi cha pa abale, ndiponso chikondi. Palibe khalidwe lililonse mwa makhalidwe abwinoŵa limene timangobadwa nalo. Timafunika kuwakulitsa. Pamafunika kuikirapo mtima ndiponso khama kuti tiwasonyeze kwambiri makhalidweŵa. Ndiyeno, kodi tingayembekezere kudziletsa kukhala kosavuta?

4. N’chifukwa chiyani anthu ambiri amaganiza kuti kudziletsa sikuwavuta, koma kodi umenewu ndi umboni wa chiyani?

4 N’zoona kuti anthu ambiri amaganiza kuti kudziletsa sikuwavuta. Iwo amangochita zofuna zawo, n’kumatsatira mwadala kapena mosadziŵa zokhumba za thupi lawo lopanda ungwiro ndipo saganizira kwenikweni zotsatira zimene iwo kapena anzawo angakumane nazo chifukwa cha zochita zawozo. (Yuda 10) Masiku ano n’zosachita kufunsa kusiyana n’kale lonseli kuti anthu satha ndiponso safuna kunena kuti toto. Umenewu ndi umboni wakuti tikukhaladi ‘m’masiku otsiriza’ omwe Paulo anatchula pamene ananeneratu kuti: “Zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, . . . osakhoza kudziletsa.”​—2 Timoteo 3:1-3.

5. N’chifukwa chiyani Mboni za Yehova zili ndi chidwi ndi nkhani ya kudziletsa, ndipo ndi malangizo otani omwe akugwirabe ntchito mpaka pano?

5 Mboni za Yehova zimadziŵa kuti n’kovuta kukhala wodziletsa. Mofanana ndi Paulo, zimadziŵa za nkhondo yomwe ilipo pakati pa chikhumbo chofuna kukondweretsa Mulungu mwa kutsatira miyezo yake ndi zinthu zomwe thupi lawo lopanda ungwiro lingawalimbikitse kuchita. Chifukwa cha zimenezi Mboni zakhala ndi chidwi chofuna kudziŵa mmene zingapambanire nkhondoyi. Kale mu 1916, kope lina la magazini mukuŵerengayi linanenapo za “njira yabwino yofunika kuitsata kuti tithe kudzilamulira, kulamulira maganizo athu, mawu athu ndiponso khalidwe lathu.” Linalimbikitsa kuti tizikumbukira Afilipi 4:8. Malangizo a Mulungu omwe ali palembali akugwirabe ntchito mpaka pano, ngakhale kuti anaperekedwa koyamba zaka pafupifupi 2,000 zapitazo ndipo mwinanso panopo ngovuta kuwatsatira kusiyana ndi panthaŵiyo kapena mu 1916. Komabe Akristu amayesetsa zolimba kukana zilakolako zadzikoli, podziŵa kuti akatero, amakhala akuvomera kuchita zofuna za Mlengi wawo.

6. N’chifukwa chiyani sitiyenera kutaya mtima pamene tikukulitsa kudziletsa?

6 Kudziletsa kukutchulidwa pa Agalatiya 5:22, 23 monga mbali ya “chipatso cha Mzimu [woyera].” Tidzapindula kwambiri ngati tisonyeza khalidweli pamodzi ndi “chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, [ndi] chifatso.” Kuchita zimenezi kudzatithandiza kuti pamene tikutumikira Mulungu tisakhale “aulesi kapena opanda zipatso,” malinga n’kufotokoza kwa Petro. (2 Petro 1:8) Koma tisamataye mtima kapena kudziimba mlandu tikalephera kusonyeza makhalidweŵa mwamsanga ndiponso kwambiri monga momwe timafunira. Mosakayikira, munaonapo kuti kusukulu wophunzira wina amagwira msanga zinthu kusiyana ndi wina. Kapena pantchito munthu wina amaphunzira msanga ntchito ina yatsopano kusiyana ndi anzake. N’chimodzimodzinso ndi makhalidwe achikristu, ena amaphunzira kusonyeza makhalidweŵa mwamsanga kusiyana ndi ena. Chofunika kwambiri ndicho kuyesetsa kupitiriza kukulitsa makhalidwe a Mulungu mmene tingathere. Tingachite zimenezi mwa kugwiritsa ntchito thandizo lomwe Yehova amapereka kudzera m’Mawu ake ndiponso mu mpingo. Chofunika kwambiri si kukwaniritsa zolinga zathu mwamsanga ayi koma kuchita khama kuti tipitirize kupita patsogolo.

7. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti kudziletsa n’kofunika?

7 Ngakhale kuti kudziletsa kuli pomalizira pa mndandanda wa makhalidwe a mzimu, sikuti n’kosafunika kwenikweni kusiyana ndi makhalidwe enawo. Sichoncho m’pang’ono pomwe. Tizikumbukira kuti tikanakhala kuti timatha kudziletsa kotheratu, bwenzi tikutha kupeŵa “ntchito [zonse] za thupi.” Komatu, anthu opanda ungwiro ali n’chizoloŵezi chochita zina mwa “ntchito za thupi . . . , dama, chodetsa, kukhumba zonyansa, kupembedza mafano, nyanga, madano, ndewu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magaŵano, mipatuko.” (Agalatiya 5:19, 20) Motero tiyenera kumenya nkhondo nthaŵi zonse, titatsimikiza kuchotseratu zizoloŵezi zoipa mumtima ndi m’maganizo mwathu.

Ena Zimawavuta Kwambiri

8. N’zinthu ziti zimene zimachititsa kuti kudziletsa kukhale kovuta kwambiri kwa anthu ena?

8 Akristu ena amavutika kwambiri kuti asonyeze kudziletsa kusiyana ndi ena. Chifukwa chiyani? Izi zimachitika mwina chifukwa cha mmene analeredwera kapena chifukwa cha moyo wawo m’mbuyomu. N’zosangalatsa ngati ifeyo sitivutika kukulitsa ndiponso kusonyeza kudziletsa. Koma tikakhala ndi anthu omwe amavutika kwambiri kuti asonyeze kudziletsa tiyenera kukhala achifundo ndiponso omvetsa zinthu, ngakhale ngati tikuvutika ndi kusadziletsa kwawoko. Poganizira za kupanda ungwiro kwathu, kodi ndani wa ife amene ali ndi chifukwa chodzionetsera kuti ndiye wolungama?​—Aroma 3:23; Aefeso 4:2.

9. Kodi ena ali ndi zofooka zotani, ndipo ndi liti pamene zofooka zimenezi zidzatheretu?

9 Mwachitsanzo, mwina tikudziŵa kuti nthaŵi zina ena mwa Akristu anzathu amene anasiya kusuta fodya kapena kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo amene anthu amati amasangalatsa munthu, amakhalabe ndi chibaba champhamvu cha zinthu zimenezi. Kapena ena amavutika kuti achepetse kadyedwe kapena kumwa moŵa. Ena amavutika kulamulira lilime lawo, moti nthaŵi zambiri amakhumudwa pa mawu. Kuti munthu athane ndi mavuto ameneŵa amafunika kuchita khama kwambiri kuti akulitse kudziletsa. Chifukwa chiyani? Yakobo 3:2 amanena molondola kuti: “Timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri. Munthu akapanda kukhumudwa pa mawu, iye ndiye munthu wangwiro, wokhoza kumanganso thupi lonse.” Ndipotu ena amakhala ndi chikhumbo champhamvu chotchova njuga. Kapena amavutika kukhala oleza. Mwina pangatenge nthaŵi yaitali kuti aphunzire kuthana bwinobwino ndi zimenezi kapena zofooka zina zofanana ndi zimenezi. Ngakhale kuti zingatheke kuti tizichita bwino panopo, zilakolako zoipa zidzatheratu pokhapokha tikadzakhala angwiro. Panopo, kuyesetsa kukhala odziletsa kudzatithandiza kuti tisayambirenso khalidwe lauchimo. Pamene tikupitirizabe kumenya nkhondoyi, tiyeni tizithandizana kuti tisafooke.​—Machitidwe 14:21, 22.

10. (a) N’chifukwa chiyani anthu ena amavutika kwambiri kudziletsa pankhani ya kugonana? (b) Kodi ndi kusintha kwakukulu kotani kumene mbale wina anachita? (Onani bokosi patsamba 16.)

10 Mbali ina yomwe anthu ena amavutika kudziletsa ndi pa nkhani ya kugonana. Kugonana pakokha ndimo mmene Yehova Mulungu anatilengera. Komabe, ena zimawavuta kwambiri kuchita zinthu zoyenera pa nkhani ya kugonana, zogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna. Mwina vuto lawo limakula kwambiri chifukwa chakuti ali ndi chilakolako champhamvu cha kugonana. Tikukhala m’dziko lokonda za kugonana, lomwe limawonjezera chilakolako cha kugonana m’njira zambiri. Izi zingavutitse kwambiri Akristu omwe akufuna kukhala osakwatira kapena osakwatiwa, kwa kanthaŵi ndithu, n’cholinga chotumikira Mulungu popanda zododometsa za m’banja. (1 Akorinto 7:32, 33, 37, 38) Koma mogwirizana ndi langizo la m’Malemba lakuti “n’kwabwino kukwatira koposa kutentha mtima,” mwina angaganize zokwatira kapena kukwatiwa, zomwe n’zabwino kwambiri. Panthaŵi imodzimodziyo, iwo amakhala akufunitsitsa kukwatira kapena kukwatiwa “mwa Ambuye,” monga momwe Malemba amalangizira. (1 Akorinto 7:9, 39) Sitingakayikire kuti Yehova amasangalala chifukwa chakuti iwo amafuna kupititsa patsogolo miyezo yake yolungama. Akristu anzawo amasangalala kuyanjana ndi olambira oona amakhalidwe abwino kwambiri komanso okhulupirika.

11. Kodi tingam’thandize motani mbale kapena mlongo amene akufuna banja koma sanalipeze?

11 Bwanji ngati Mkristu sakupeza mkazi kapena mwamuna womuyenera? Tangoganizirani mmene angakhumudwire munthu woti akufuna banja koma sakulipeza! Mwina angamaone anzake akuloŵa m’banja n’kumasangalala, iye akali mkati mofufuza mnzake womuyenera. Kwa anthu ena omwe ali m’mavuto ngati ameneŵa angathe kuyamba chizoloŵezi chodetsa choseŵeretsa maliseche pofuna kudzisangalatsa. Mulimonsemo, palibe Mkristu amene amafuna kukhumudwitsa mosadziŵa Mkristu mnzake amene akuyesetsa kukhala wodzisunga. Koma mosadziŵa tingathe kum’khumudwitsa ndi mawu osaganizirana monga akuti, “Mukwatira liti kodi inu?” Mwina tinganene zimenezo popanda maganizo alionse olakwika, komatu zingakhale bwino kwambiri titasonyeza kudziletsa mwa kulamulira lilime lathu. (Salmo 39:1) Tikufunika kuwayamikira kwambiri anzathu omwe akudzisunga asanaloŵe m’banja. M’malo monena zinthu zomwe zingawagwetse mphwayi, tiziyesetsa kuwalimbikitsa. Mwachitsanzo, tikhoza kumayesetsa kuti pagulu laling’ono la anthu achikulire amene asonkhana kuti adye chakudya kapena kusangalala ndi macheza abwino achikristu pazikhalanso anthu osakwatira kapena osakwatiwa.

Kudziletsa M’banja

12. N’chifukwa chiyani kudziletsa kuli kofunikabe ndithu ngakhale kwa anthu apabanja?

12 Munthu akaloŵa m’banja sindiye kuti wathana nayo nkhani ya kudziletsa pambali ya kugonana. Mwachitsanzo, chikhumbo cha kugonana cha mwamuna ndi mkazi wake chingakhale chosiyana kwambiri. Kapena thanzi la wina mwa aŵiriwo nthaŵi zina lingapangitse kuti kugonana kwa masiku onse kukhale kovuta kapenanso kosatheka. Mwina chifukwa cha moyo wa m’mbuyomu, wina m’banjamo angamavutike kutsatira lamulo lakuti: ‘Mwamuna apereke kwa mkazi mangawa ake; koma modzimodzinso mkazi kwa mwamuna.’ Zinthu zikakhala choncho, winayo angafunike kukhala wodziletsa kwambiri. Koma onse afunika kukumbukira malangizo abwino a Paulo kwa Akristu apabanja, akuti: “Musakanizana, koma ndi kuvomerezana kwanu ndiko, kwa nthaŵi, kuti mukadzipereke kwa kupemphera, nimukakhalenso pamodzi, kuti Satana angakuyeseni, chifukwa cha kusadziletsa kwanu.”​—1 Akorinto 7:3, 5.

13. Kodi tingawachitire chiyani anthu amene akuyesetsa kuti akhale odziletsa?

13 Mwamuna ndi mkazi angasangalale kwambiri ngati onse aŵiri aphunzira kukhala odziletsa moyenerera mu ubwenzi wapamtima umenewu. Komanso ndi bwino kuti azisonyeza kuti amawamvetsa olambira anzawo amene akuyesetsabe kuti akhale odziletsa pankhani imeneyi. Tisamaiwale kupemphera kuti Yehova apatse abale athu auzimu nzeru, khama, ndi mtima wofunitsitsa kuti apitirize nkhondo yawo yofuna kuti akhale odziletsa ndiponso kuti achite zomwe zikufunika kuti agonjetse zilakolako zolakwika.​—Afilipi 4:6, 7.

Pitirizani Kuthandizana

14. N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zinthu mwachifundo ndiponso momvetsa ndi Akristu anzathu?

14 Nthaŵi zina tingalephere kuwamvetsa Akristu anzathu amene akuyesetsa kusonyeza kudziletsa pankhani yomwe ifeyo sitivuta n’komwe kudziletsa. Komatu anthufe mwachibadwa ndife osiyanasiyana. Ena sachedwa kutengeka mtima ndi zinthu; pamene ena ayi. Ena amaona kuti savutika kwenikweni kulamulira matupi awo, ndipo sachita kuvutikira kuti adziletse. Ena amavutika kwambiri. Komabe, kumbukirani kuti munthu amene akuyesetsa kuti athane ndi vuto linalake sindiye kuti munthuyo ndi woipa. Tifunika tiziwamvetsa ndi kuwachitira chifundo Akristu anzathu. Timapeza chimwemwe tikamapitiriza kuchitira chifundo anthu amene akumenyerabe nkhondo kuti azisonyeza kudziletsa kwambiri. Tingaone zimenezi m’mawu a Yesu opezeka pa Mateyu 5:7.

15. N’chifukwa chiyani mawu a pa Salmo 130:3 ali olimbikitsa pankhani ya kudziletsa?

15 Sitikufuna kum’ganizira molakwika Mkristu mnzathu amene nthaŵi ina angalephere kusonyeza khalidwe lachikristu. N’zolimbikitsa kwambiri kudziŵa kuti kuwonjezera pa kuona nthaŵi imodzi imene sitinathe kudziletsa, Yehova amaonanso nthaŵi zambiri zomwe tasonyeza kudziletsa, ngakhale Akristu anzathu atapanda kuona zonsezo. N’zolimbikitsa kukumbukira mawu a pa Salmo 130:3 akuti: “Mukasunga mphulupulu, Yehova, adzakhala chilili ndani, Ambuye?”

16, 17. (a) Kodi tingagwiritse ntchito motani Agalatiya 6:2, 5 pankhani ya kudziletsa? (b) Kodi tidzaonanji pankhani ya kudziletsa m’nkhani yotsatira?

16 Kuti tikondweretse Yehova, aliyense wa ife ayenera kukulitsa khalidwe la kudziletsa, komabe tingakhale otsimikiza kuti abale athu achikristu adzatithandiza. Ngakhale kuti aliyense ayenera kunyamula katundu wake, koma tikulimbikitsidwa kuti tizithandizana polimbana ndi zofooka. (Agalatiya 6:2, 5) Tingayamikire kwambiri kholo, mkazi kapena mwamuna wathu, kapenanso mnzathu amene akutiletsa kupita malo amene sitiyenera kupitako, kuona zinthu zomwe sitiyenera kuona, kapena kutiletsa kuchita zinthu zomwe sitiyenera kuchita. Iwo akutithandiza kukhala odziletsa, kutha kunena kuti toto motsimikiza mtima.

17 N’kutheka kuti Akristu ambiri akuchita zimene takambiranazi, komabe mwina akuona kuti padakali zambiri zoti achite pankhani ya kudziletsa. Akufuna kuti akhale odziletsa kwambiri, afike pamlingo womwe amaona kuti anthu opanda ungwiro angaukwanitse. Kodi inu mukuona choncho? Ndiye mungachite chiyani kuti mukulitse mbali imeneyi ya chipatso cha mzimu wa Mulungu? Ndipo kuchita zimenezo kungakuthandizeni motani kukwaniritsa zolinga zanu zam’tsogolo monga Mkristu? Tidzaona zimenezi m’nkhani yotsatirayi.

Kodi Mukukumbukira?

N’chifukwa Chiyani Kudziletsa . . .

• n’kofunika kwa Akristu?

• n’kovuta kwambiri kwa ena?

• n’kofunika m’banja?

• ndi khalidwe limene tingathandizane kulikulitsa?

[Mafunso]

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 16]

Anaphunzira Kunena Kuti Toto

Mwamuna wina wa Mboni za Yehova amene amakhala ku Germany analembedwa ntchito yoyang’anira ndi kukonza zipangizo zoulutsira mawu. Ina mwa ntchito yake inali kuona mmene mapulogalamu 30 a pa TV ndi a pawailesi anali kuulutsidwira. Pulogalamu ikakhala kuti sikumveka kapena kuoneka bwino, iye ankafunika kuonetsetsa kapena kuimvetsera mwatcheru pulogalamuyo n’cholinga choti apeze pamene pagona vutolo. Iye anati: “Nthaŵi zambiri izi zinkachitika nthaŵi yolakwika. Zinkachitika nthaŵi yomwe akuonetsa zachiwawa kapena zachiwerewere. Zithunzi zoipazo zinkakhala m’maganizo mwanga masiku angapo, mwinanso milungu ingapo, ndiye ngati kuti zadindika mu ubongo wanga.” Iye anavomereza kuti zimenezi zinali kumusokoneza mwauzimu, anati: “Ndine munthu waphuma kwambiri, motero zithunzi zachiwawa zinkandilepheretsa kukhala wodziletsa. Ndinkakangana ndi mkazi wanga chifukwa cha zithunzi zachiwerewere. Ndinkalimbana ndi vutoli tsiku ndi tsiku. Pofuna kuti ndisagonje, ndinaganiza zopeza ntchito ina, ngakhale yamalipiro ochepa. Sikale kwambiri pamene ndinaipeza. Cholinga changa chinakwaniritsidwa.”

[Zithunzi patsamba 15]

Zimene timadziŵa kudzera m’phunziro la Baibulo zimatithandiza kukhala odziletsa